Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


108 Mauthenga a Baibulo Okhudza Mimba

108 Mauthenga a Baibulo Okhudza Mimba

Mulungu amafuna kukhala nawe pa chilichonse chimene ukuchita. Afuna ukhale ndi chikhulupiriro chonse kuti Atate akuyang’anira zinthu zonse zazing’ono ndi zazikulu m’moyo wako.

Pa nthawi yokongola iyi m’moyo wako, uli ndi dalitso lalikulu, mphatso yapadera yomwe uyenera kuisamalira ndi kuikonda kwambiri. Uyenera kuisamalira kuti ikule bwino, ukhale woleza mtima ndipo uiiyetse mwanzeru pamene ikukula.

Kukhala ndi pakati kukubweretsera chimwemwe chachikulu, chifukwa uli ndi munthu amene akukufuna tsiku lililonse. Muzipsompsona, muziimbira nyimbo, ndipo muzipempherera.

Sangalala ndi gawo lililonse la mimba yako ndipo ukhale ndi chiyembekezo kuti zonse zidzayenda bwino. Lankhula ndi Mzimu Woyera, umupemphe kuti akuthandize pa mantha ako ndi kukupatsa mphamvu pa nthawi yobereka.

Mwana akangobadwa, yamikani Mulungu ndipo sangalalani ndi mphindi iliyonse naye. Kubweretsa moyo padziko lapansi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.




Yohane 16:21

Mkazi pamene akuti abale ali nacho chisoni, chifukwa yafika nthawi yake; koma pamene wabala mwana, sakumbukiranso kusaukako, chifukwa cha chimwemwe kuti wabadwa munthu kudziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:13

Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:3

Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:13-14

Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 25:21

Ndipo Isaki anampembedzera mkazi wake kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwake, ndipo Rebeka mkazi wake anatenga pakati.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 4:1

Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 1:5

Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 30:22-23

Ndipo Mulungu anakumbukira Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m'mimba mwake. Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, nati, Mulungu wachotsa manyazi anga;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:27-28

Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi. Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:24-25

Ndipo atatha masiku awa, Elizabeti mkazi wake anaima; nadzibisa miyezi isanu, nati, Ambuye wandichitira chotero m'masiku omwe Iye anandipenyera, kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:24

Atero Yehova, Mombolo wako, ndi Iye amene anakuumba iwe m'mimba, Ine ndine Yehova, amene ndipanga zinthu zonse, ndi kufunyulula ndekha zakumwamba, ndi kuyala dziko lapansi; ndani ali ndi Ine?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:36-37

Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna m'ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma. Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:41-44

Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera; nakweza mau ndi mfuu waukulu, nati, Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo chodalitsika chipatso cha mimba yako. Ndipo ichi chichokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amake wa Ambuye wanga? Pakuti ona, pamene mau a moni wako analowa m'makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m'mimba mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:11

Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 29:35

Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna; nati, Tsopano ndidzamyamikira Yehova; chifukwa chake anamutcha dzina lake Yuda; pamenepo analeka kubala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 3:16

Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 35:17

Ndipo panali pamene anavutidwa, namwino anati kwa iye, Usaope: pakuti udzakhala ndi mwana wina wamwamuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 1:20

Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samuele, nati, Chifukwa ndinampempha kwa Yehova,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:36

Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna m'ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:28

Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 113:9

Asungitsa nyumba mkazi wosaona mwana, akhale mai wokondwera ndi ana. Aleluya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 1:27-28

Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa chopempha changa ndinachipempha kwa Iye; chifukwa chake inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 128:3

Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:26

M'dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuwerenga kwa masiku ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:3

Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 1:20-21

Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:1

Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutali; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m'mimba mwa amai Iye anatchula dzina langa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:19

Tiana tanga, amene ndilikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu aumbika mwa inu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 1:16

ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:16

Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:7

Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:6

Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:7

Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:6

Zidzukulu ndizo korona wa okalamba; ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:14

Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:11

Iye adzadyetsa zoweta chake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa pachepa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:9

Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 21:1-2

Ndipo Yehova anayang'anira Sara monga momwe anati, ndipo Yehova anamchitira iye monga ananena. Chifukwa chake anati kwa Abrahamu, Chotsa mdzakazi uyo, ndi mwana wake wamwamuna; chifukwa mwana wa mdzakazi uyo sadzalowa m'nyumba pamodzi naye mwana wanga Isaki. Ndipo mauwo anaipira Abrahamu chifukwa cha mwana wake. Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ake; chifukwa kuti mwa Isaki zidzaitanidwa mbeu zako. Ndipo mwana wamwamuna wa mdzakazi uyo ndidzayesa mtundu, chifukwa iye ndiye mbeu yako. Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi mchenje wa madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba. Ndipo anatha madzi a m'mchenje ndipo anaika mwana pansi pa chitsamba. Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patali, monga pakugwa muvi: chifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ake nalira. Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali. Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; chifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukulu. Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwake, ndipo anaona chitsime cha madzi; namuka nadzaza mchenje ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe. Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu m'ukalamba wake mwana wamwamuna, nthawi yomweyo Mulungu anamuuza iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:15

Thupi langa silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:4-5

Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:17-18

Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:9

Kodi Ine ndidzafikitsira mkazi nthawi yakutula osamtulitsa? Ati Yehova; kodi Ine amene ndibalitsa ndidzatseka mimba? Ati Mulungu wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:73

Manja anu anandilenga nandiumba; mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:57-58

Ndipo inakwanira nthawi ya Elizabeti, ya kubala kwake, ndipo anabala mwana wamwamuna. Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 30:1-2

Pamene Rakele anaona kuti sanambalire Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe. Ndipo Zilipa mdzakazi wake wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna. Ndipo Leya anati, Wamwai ine! Ndipo anamutcha dzina lake Gadi. Ndipo Zilipa mdzakazi wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri. Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana akazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere. Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m'thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako. Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako. Ndipo Yakobo anadza madzulo kuchokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo. Ndipo Mulungu anamvera Leya, ndipo anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu. Ndipo Leya anati, Mulungu wandipatsa ine mphotho yanga, chifukwa ndapatsa mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga: namutcha dzina lake Isakara. Ndipo Leya anatenganso pakati nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu ndi chimodzi. Ndipo Yakobo anapsa mtima ndi Rakele; nati, Kodi ine ndikhala m'malo a Mulungu amene akukaniza iwe zipatso za mimba?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:26

Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:5

Onani, ndinabadwa m'mphulupulu, ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:15-16

Ndipo anadza nao kwa Iye ana amakanda kuti awakhudze; koma pamene ophunzira anaona anawadzudzula. Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 8:5

Pakuti munamchepsa pang'ono ndi Mulungu, munamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:7

Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 29:31

Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m'mimba mwake; koma Rakele anali wouma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:8

Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:15

Maso a onse ayembekeza Inu; ndipo muwapatsa chakudya chao m'nyengo zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:12

Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:2

Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:11

Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:26

Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:1

Imba, iwe wouma, amene sunabala; imba zolimba ndi kufuula zolimba, iwe amene sunabala mwana; pakuti ana a mfedwa achuluka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:41

Koma aika waumphawi pamsanje posazunzika, nampatsa mabanja ngati gulu la nkhosa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:30-31

Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Maria; pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu. Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:5

Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:165

Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:17

Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa; nadzasangalatsa moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:11

Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:10

Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Ine wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 29:11

Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu, Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:24

Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera, kuti apatuke kusiya kunsi kwa manda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:31

Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chake kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:10

Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 21:6-7

Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine. Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? Pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna m'ukalamba wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:13

Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa, simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe? Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu m'kuunika kwa amoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:3

Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6-7

Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:13

Monga munthu amene amake amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima m'Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 130:5

Ndilindira Yehova, moyo wanga ulindira, ndiyembekeza mau ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:18

Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:30

Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wa kuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:16

Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:92

Chilamulo chanu chikadapanda kukhala chikondweretso changa, ndikadatayika m'kuzunzika kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:3

Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:19

Koma Mulungu anamvadi; anamvera mau a pemphero langa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:4

Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 18:10

Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yake; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:15

Nyengo zanga zili m'manja mwanu, mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 135:4

Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo, Israele, akhale chuma chake chenicheni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:26

Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 130:7

Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:5

Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:1

Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 28:7

Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 2:21

Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana amuna atatu, ndi ana akazi awiri. Ndipo mwanayo Samuele anakula pamaso pa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:114

Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 29:32

Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:17

Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:19

Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:20

ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:9

Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:28

Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni: Mundilimbitse monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, ndinu Alfa ndi Omega! Atate, mlengi wa thambo ndi dziko lapansi, ndinu woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi chimaliziro. Atate pakali pano ndikubwera kwa inu m'dzina la Yesu kuti ndikuthokozani ndi mtima wanga wonse chifukwa cha mimba yanga, chifukwa mwasankha kundipatsa dalitso lokongola komanso losangalika lomwe nthawi yomweyo ndi udindo waukulu, zikomo chifukwa chopeza chisomo pamaso panu ndipo mwandisankha kukhala chida chobweretsera mwana uyu wodabwitsa padziko lapansi amene akukula m'mimba mwanga. Mulungu wokondedwa tambasulani dzanja lanu pa ine kuti ndimve mtendere ndi mpumulo pakati pa gawo lino, mawu anu amati: "Sipadzakhala mkazi amene adzataya mimba, kapena wosabala m'dziko lanu; ndipo Ine ndidzakwaniritsa masiku anu," chifukwa chake, ndimakhulupirira kuti mumasamalira miyoyo yathu ndipo mumasamalira thanzi la mwana wanga. Atate ndikuyika chitukuko, kukula ndi ubwino wa mwana wanga m'manja mwanu, ndikupemphani kuti mumupange kukhala munthu wabwino, wakhama, wolimba mtima, wachilungamo wodzala ndi chisomo ndi chiyanjo chanu. Mundipatse nzeru kuti ndimulangize m'njira yanu ndipo akule poopa dzina lanu, Mulungu ndithandizeni kukhala mawu olimbikitsa ndi uphungu kwa iye. M'dzina la Yesu, Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa