Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


58 Mau a Mulungu Oyambitsa Msonkhano

58 Mau a Mulungu Oyambitsa Msonkhano

Moyoyo wanga uli ndi cholinga choposa kungopeza madigiri kapena ulemu. Ndife okhulupirira, ntchito yathu ndiyo kulambira Mulungu, ndipo kuti tichite izi tiyenera kusonkhana ndi abale ndi alongo athu kuti timange guwa la chitamando ndi kudzipereka pamaso pake.

Timamutambasula Mulungu mwa kusonyeza kudzichepetsa, kudzipereka, ndi kulambira. Mzimu Woyera utitsogolera pakulambira Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, amene anatipatsa mpweya wa moyo, amene anatipulumutsa, amene anatikhululukira machimo athu, ndi amene anatilongonzera ufumu wakumwamba kudzera mwa mwana wake Yesu Khristu.

Monga mmene Yohane 4:23 imanenera, nthawi yafika pamene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi, pakuti Atate amawafuna olambira oterowo.




1 Mbiri 16:34

Thokozani Chauta, pakuti ngwabwino, chikondi chake chosasinthika nchamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yona 2:9

Koma ine ndidzapereka nsembe kwa Inu ndi mau okuthokozani. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita ndithu. Chipulumutso nchochokera kwa Inu Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:16

Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:33

Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:25

Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:20

Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 122:1

Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:8

Pajatu Inu mudati, “Muzifunafuna nkhope yanga.” Inu Chauta, ndidzafunafuna nkhope yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28

“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:22

Koma tsopano mwamasulidwa ku uchimo, ndipo ndinu otumikira Mulungu. Phindu lake ndi kuyera mtima, ndipo potsiriza pake kulandira moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:11

Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:5

Mbuye wathu ndi wamkulu, ndipo ndi wa mphamvu zambiri, nzeru zake nzopanda malire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:2-3

M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo. Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu. “Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.” Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. “Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani. “Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:17

Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:11-12

Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina, mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo. Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:14

Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:1-2

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera. Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu. Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife. Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza. Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi. Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo. Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake. Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake. Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake. Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:18

Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:1-2

Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau, inu anthu onse a pa dziko lapansi. Inu Mulungu, mwatiyesa, mwatiyeretsa monga m'mene amayeretsera siliva. Inu mudatiloŵetsa mu ukonde wa adani, mudatisenzetsa katundu wolemera pamsana pathu. Inu mudalola kuti adani atikwere pa mutu, tidaloŵa m'moto ndiponso m'madzi, komabe Inu mwatifikitsa ku malo opulumukirako. Ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzachitadi zimene ndidazilumbira kwa Inu, zimene ndidalankhula ndi pakamwa panga, ndiponso zimene ndidalonjeza pamene ndinali pa mavuto. Ndidzapereka kwa Inu nsembe zopsereza za nyama zonenepa, utsi wa nsembe za nkhosa zamphongo udzafika kwa Inu. Ndidzaperekanso ngati nsembe ng'ombe zamphongo ndi mbuzi. Bwerani mudzamve, inu nonse amene opembedza Mulungu, ndidzakusimbireni zimene Iye wandichitira. Ndidafuula kwa Iye, ndipo ndidamtamanda ndi pakamwa panga. Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera. Koma zoonadi, Mulungu wandimvera, wasamala mau a pemphero langa. Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:1-5

Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse. Tumikirani Chauta mosangalala. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa. Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake. Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake! Paja Iye ndi wabwino. Chikondi chake nchamuyaya, kukhulupirika kwake nkosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 29:11

Chauta amapatsa anthu ake mphamvu. Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere. Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:42

Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:12-13

Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani. Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:23-24

Koma ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza. Mulungu ndi mzimu, ndipo ompembedza Iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:16

Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 95:1-7

Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa. Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.” Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo. Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda. Pakuti Chauta ndiye Mulungu wamkulu, ndiye Mfumu yaikulu yopambana milungu yonse. Maziko ozama a dziko lapansi ali m'manja mwake. Mapiri aatali omwe ngakenso. Nyanja ndi yake, popeza kuti ndiye adailenga. Mtunda ndi wakenso, popeza kuti ndiye adaupanga. Bwerani, timpembedze ndi kumlambira. Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu. Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake, ndife nkhosa zodyera m'manja mwake. Lero mukadamverako mau ake!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 95:1-3

Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa. Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.” Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo. Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda. Pakuti Chauta ndiye Mulungu wamkulu, ndiye Mfumu yaikulu yopambana milungu yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:2

Paja Mulungu akuti, “Pa nthaŵi yanga yabwino ya kukomera anthu mtima, ndidakumvera, pa nyengo ya kupulumutsa anthu, ndidakuthandiza.” Mvetsani, ndi inotu nthaŵi yabwinoyo, imene Mulungu akukomera anthu mtima. Ndi Lerotu tsiku la chipulumutsolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:28

Mzimu Woyera adakuikani kuti muziyang'anira mpingo wonse. Tsono mudzisamale nokha, ndipo musamalenso mpingowo. Ŵetani nkhosa za mpingo wa Ambuye umene Iwo adauwombola ndi magazi aoao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:7

Muzikumbukira atsogoleri anu amene ankakulalikirani mau a Mulungu. Muzilingalira za moyo wao ndi m'mene adafera, ndipo muzitsanzira chikhulupiriro chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 28:7

Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 29:2

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta. Mumpembedze mu ulemu wa ungwiro wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:4

Muzikondwa mwa Ambuye nthaŵi zonse. Ndikubwerezanso kuti, “Muzikondwa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 150:1-2

Tamandani Chauta! Tamandani Mulungu m'malo ake opatulika. Mtamandeni ku thambo lake lamphamvu. Mtamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu, mtamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 150:1-6

Tamandani Chauta! Tamandani Mulungu m'malo ake opatulika. Mtamandeni ku thambo lake lamphamvu. Mtamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu, mtamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana. Mtamandeni pomuimbira lipenga, mtamandeni ndi gitara ndi zeze. Mtamandeni poimba ng'oma ndi povina, mtamandeni ndi zipangizo zansambo ndi mngoli. Mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira, mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira kwambiri. Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Chauta. Tamandani Chauta!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:42-47

Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi. Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao. Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense. Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:7

Pa tsiku loyamba la sabata, tidasonkhana kuti tidye Mgonero, ndipo Paulo ankakamba ndi anthu. Popeza kuti ankayembekeza kupita m'maŵa mwake, adapitiriza kulankhula mpaka pakati pa usiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 12:4-6

Tsiku limenelo mudzati: “Thokozani Chauta, tamandani dzina lake. Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, mulalike kuti dzina lake ndi lopambana. “Imbirani Chauta nyimbo zotamanda, pakuti wachita zazikulu. Zimenezi zidziŵike pa dziko lonse lapansi. Fuulani ndi kuimba mokondwa, inu anthu a ku Ziyoni, pakuti Woyera Uja wa Israele ndi wamkulu pakati panu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:1-3

Ndidzayamika Chauta nthaŵi zonse, pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza. Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino. Bwerani ana anga, mundimvere, ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta. Ndani mwa inu amakhumba moyo ndi kulakalaka kuti akhale masiku ambiri, kuti asangalale ndi zinthu zabwino? Ngati ufunadi moyo, usalankhule zoipa, pakamwa pako pasakambe zonyenga. Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino. Funafuna mtendere ndi kuulondola. Ngati mumvera Chauta, adzakuyang'anirani ndipo adzayankha kupempha kwanu. Koma Chauta amaŵakwiyira anthu ochita zoipa, anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano. Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima. Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse. Moyo wanga umanyadira Chauta. Anthu ozunzika amve ndipo akondwere. Chauta amasunga thupi la munthuyo, palibe fupa limene limasweka. Choipa chitsata mwini, anthu odana ndi munthu wa Mulungu adzalangidwa. Chauta amaombola moyo wa atumiki ake. Palibe wothaŵira kwa Iye amene adzalangidwe. Lalikani pamodzi nane ukulu wa Chauta, tiyeni limodzi tiyamike dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16

Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:12

Inu Ambuye, Mulungu wanga, ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse, ndidzalemekeza ukulu wanu mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:5

Inu Chauta, Mulungu wanga, mwatichitira zodabwitsa zambiri, mwatikonzera zabwino zambiri zakutsogolo. Palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulingana nanu. Ndikati ndisimbe ndi kulongosola za zimenezo, sindingathe kuziŵerenga zonse chifukwa cha kuchuluka kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:23-25

Imbirani Chauta, inu anthu a dziko lonse lapansi. Lengezani tsiku ndi tsiku za m'mene Iye adapulumutsira anthu ake. Lalikani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse. Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri, ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:5-6

Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:1-2

Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:19-20

Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu. Muziyamika Mulungu Atate nthaŵi zonse chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 47:1-2

Ombani m'manja inu anthu a mitundu yonse. Fuulani kwa Mulungu poimba nyimbo zachimwemwe. Paja Chauta Wopambanazonse, ndi woopsa, ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:1-3

Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi. Iwo adzaperekedwa kuti akaphedwe ku nkhondo, motero adzasanduka chakudya cha nkhandwe. Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu. Onse olumbirira Iye, adzamtamanda, koma pakamwa pa anthu abodza padzatsekedwa. Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu. Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 113:1-3

Tamandani Chauta! Mtamandeni, inu atumiki ake, tamandani dzina la Chauta. Yamikani Chauta kuyambira tsopano mpaka muyaya. Dzina la Chauta litamandike kuyambira ku matulukiro a dzuŵa mpaka ku maloŵero ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:2

Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:15

Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 25:1

Inu Chauta, ndinu Mulungu wanga. Ndidzakulemekezani ndi kutamanda dzina lanu. Pakuti mwachita zinthu zodabwitsa mokhulupirika ndi motsimikiza, zinthu zimene mudakonzeratu kalekale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:4-5

Imbani nyimbo zotamanda Chauta, inu anthu ake oyera mtima, mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera. Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:4

Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, ndinu Alfa ndi Omega! Atate, Mlengi wa thambo ndi dziko lapansi, ndinu woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi chimaliziro. Atate, zikomo chifukwa palibe malo abwino padziko lapansi kuposa kukhala m'nyumba mwanu ndi kupereka pamaso panu kulambira kwanga kopambana ndi kukwezetsa kwanu. Ndi mtima wofunitsitsa ndikupereka nsembe yanga yachikondi ndi chiyamiko, ndikudzipereka pamaso panu chifukwa cha zonse zomwe mwachita ndi zomwe mupitirize kuchita mwa ine ndi m'banja langa. Ndi chisangalalo ndi chimwemwe pamodzi ndi abale ndi alongo anga ndikufuulira kumwamba, kufunafuna nkhope yanu mu mzimu ndi m'choonadi. Mawu anu amati: "Pakuti pamene pali awiri kapena atatu osonkhana m'dzina langa, Ine ndili komweko pakati pawo". Ambuye, ndikupempha kuti mu msonkhano uliwonse tizione thambo likutseguka chifukwa cha mphamvu ya kukhalapo kwanu, kuti mafuta ndi mphamvu ya Mzimu Woyera zizithira pa miyoyo ya abusa athu, monga mpingo woyamba kumene onse anali okhazikika m'chiphunzitso ndi m'chiyanjano. Ambuye, kuti mu msonkhano uliwonse cholinga changa chikhale kudzipereka ngati nsembe yolandirika, chifukwa palibe vuto lomwe simungathe kulithetsa. Mawu anu amati: "Perekani matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera, yolandirika kwa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera". Ndikufuna kudalitsa miyoyo ya abale ndi alongo anga kudzera mu utumiki wanga, osatumikira maso, monga ofuna kukondweretsa anthu, koma monga mtumiki wa Khristu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa