Kumvera Mulungu kuyenera kuchokera mumtima mwanga ngati kuyankha chikondi Chake ndi zonse zomwe wandichitira ndi zomwe akundichitira. Sikuti ndingongotsatira kapena kuvomereza mopanda chikhumbo chimene Iye akufuna, chifukwa nthawi zina sindimvetse chifukwa chake wandilamula kuchita kapena kusiya chinthu china. Komabe, ndimaonetsa chikhulupiriro changa ndi kudalira Mulungu mwa kumvera ngakhale sindikumvetsa zifukwa Zake.
Mwa kumvera malamulo a Mulungu, ndikudzikonzekeretsa moyo wosatha ndi kukwezedwa. Ndikukumbukira kuti ndine mtumiki wa amene ndikumvera, kaya ndi uchimo kapena Mulungu ndi Mawu Ake, ndipo ndimakhala mtumiki wa chilungamo.
Pomaliza, zilibe kanthu kuchuluka kwa ntchito zomwe ndimachita kapena utumiki womwe ndimapereka, khalidwe langa lofunika kwambiri pamaso pa Mulungu liyenera kukhala kumvera, chifukwa kwa Ambuye wanga, kumvera n’kofunika kwambiri kuposa nsembe zambiri (1 Samueli 15:22).
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
Okondedwa, mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tili nako kulimbika mtima mwa Mulungu; ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.
Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye.
Chifukwa chake muzikonda Yehova Mulungu wanu, ndi kusunga chilangizo chake, ndi malemba ake, ndi maweruzo ake, ndi malamulo ake, masiku onse.
osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu ina kuitumikira.
Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a pa dziko lapansi;
koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni.
Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.
Pakuti ukamveratu mau ake, ndi kuchita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe.
Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.
Muziyenda m'njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani, kuti mukakhale ndi moyo, ndi kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke m'dziko limene mudzakhala nalo lanulanu.
Potero imvani, Israele, musamalire kuwachita, kuti chikukomereni ndi kuti muchuluke chichulukire, monga Yehova Mulungu wa makolo anu anena ndi inu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.
Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita;
Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;
Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.
Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu?
Taonani, ndilikuika pamaso panu lero dalitso ndi temberero; dalitso, ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikuuzani lero lino; koma temberero, ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kupatuka m'njira ndikuuzani lero lino, kutsata milungu ina imene simunaidziwa.
Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mau ake, ndi kumtumikira Iye, ndi kummamatira.
Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a pa dziko lapansi; Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani. Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo. Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha. Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita; osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu ina kuitumikira. Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani. Mudzakhala otembereredwa m'mudzi, ndi otembereredwa pabwalo. Lidzakhala lotembereredwa dengu lanu ndi choumbiramo mkate wanu. Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu. Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa potuluka inu. ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu.
popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, kuti mukakhale ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m'dziko limene mulowako kulilandira.
Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipatukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako. Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.
Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka m'Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi.
Koma samalirani bwino kuti muchite chilangizo ndi chilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake zonse ndi kusunga malamulo ake, ndi kumuumirira Iye, ndi kumtumikira Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
Mukaopa Yehova ndi kumtumikira ndi kumvera mau ake, ndi kusakana lamulo lake la Yehova, ndipo inu ndi mfumu imene iweruza inu mukadzatsata Yehova Mulungu wanu, chabwino. Koma mukapanda kumvera mau a Yehova, ndi kupikisana ndi lamulo la Yehova, dzanja la Yehova lidzatsutsana nanu, monga linatsutsana ndi makolo anu.
Ndipo Saulo anati kwa Samuele, Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; chifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.
nusunge chilangizo cha Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zake, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wake, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, kuti ukachite mwa nzeru m'zonse ukachitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako;
Ndipo ukadzayenda m'njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, Ine ndidzachulukitsa masiku ako.
Mitima yanu ikhale yangwiro ndi Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malemba ake ndi kusunga malamulo ake, monga lero lino.
Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kuchita chilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga ndinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israele.
Pakuti anaumirira Yehova osapatuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.
Ndipo tsopano, pamaso pa Aisraele onse, khamu la Yehova, ndi m'makutu a Mulungu wathu, sungani, nimufunefune malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti mukhale nalo lanulanu dziko lokoma ili, ndi kulisiyira ana anu pambuyo panu cholowa chao kosalekeza.
ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera m'Mwamba, ndi kukhululukira choipa chao, ndi kuchiritsa dziko lao.
Ndipo m'ntchito iliyonse anaiyamba m'utumiki wa nyumba ya Mulungu, ndi m'chilamulo, ndi m'mauzo, kufuna Mulungu wake, anachita ndi mtima wake wonse, nalemerera nayo.
ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake;
amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'chilamulo cha Mulungu anachipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kuchita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake;
Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.
Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; motero nkhokwe zako zidzangoti thee, mbiya zako zidzasefuka vinyo. Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye. Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala. Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zamwamba ndi luntha. pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.
Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja;
Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.
limene ndinauza makolo anu tsiku lomwe ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, m'ng'anjo ya chitsulo, kuti, Mverani mau anga, ndi kuwachita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu;
Chifukwa chake tsopano konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka choipa chimene ananenera inu.
Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, chomwecho kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.
Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwachita.
Ndipo ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse, zidzapatsidwa kwa anthu a opatulika a Wam'mwambamwamba; ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi maiko onse adzamtumikira ndi kummvera.
Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi chifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,
Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza.
Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.
Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo.
Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye.
Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Iye ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.
Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.
amene ife tinalandira naye chisomo ndi utumwi, kuti amvere chikhulupiriro anthu a mitundu yonse chifukwa cha dzina lake;
pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama.
Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama.
Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo? Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene munaperekedweracho; ndipo pamene munamasulidwa kuuchimo, munakhala akapolo a chilungamo.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Pakuti chifukwa cha ichi ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m'zonse.
ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;
Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.
Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo. pakutinso munawachitira ichi abale onse a m'Masedoniya lonse. Koma tikudandaulirani, abale, muchulukireko koposa, ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani; kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu. Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo. Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu. Pakuti ichi tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo. Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka; pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse. Chomwecho, tonthozanani ndi mau awa. Pakuti mudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa Ambuye Yesu.
M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.
m'lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu;
kuti usunge lamulolo, lopanda banga, lopanda chilema, kufikira maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu;
Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi.
Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino;
ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha;
Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.
Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.
Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake.
Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;
Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse;
Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?
Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake. Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi; koma iye amene akasunga mau ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. M'menemo tizindikira kuti tili mwa Iye;
ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.
Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kuchita malamulo ake. Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha. Tiana, dzisungireni nokha kupewa mafano. Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.
Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo.
Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira.
Ndipo iye amene alakika, ndi iye amene asunga ntchito zanga kufikira chitsiriziro, kwa iye ndidzapatsa ulamuliro wa pa amitundu;
Popeza unasunga mau a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza pa dziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko.
Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, nichinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.
Pano pali chipiriro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu.
Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake.
Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.