Ndikufuna kukuuzani nkhani yokhudza ulemu kwa makolo athu. Mulungu amafuna tonse, ana, achinyamata, ndi akuluakulu, kuti tiphunzire kulemekeza ndi kumvera makolo athu kuti tizikhala moyanjana ndi nzeru. Baibulo limati, "Lemekeza atate wako ndi amako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira, kuti masiku ako akhale ochuluka, ndi kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa." (Deuteronomo 5:16).
Mukadziwa, ngakhale Yesu, ali mwana, anamvera makolo ake a padziko lapansi ndipo anakulanso mu nzeru. Iye anali Mwana wa Mulungu, koma anasonyeza chitsanzo chabwino cha kumvera. Ndipo ife, kodi sitingatsanzire chitsanzo chake cha ulemu?
Tikamamvera makolo athu, timadalitsa kwambiri. Mulungu amatipatsa madalitso ambiri chifukwa chomvera mawu ake ndi mfundo zake zosatha. Ndikukhulupirira kuti tonse tingatsatire chitsanzo cha Yesu ndi kukhala odalitsidwa.
Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Lemekeza atate wako ndi amai ako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke, ndi kuti chikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,
Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu.
Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu;
Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wake kapena mai wake. Ndi anthu onse anene, Amen.
Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mai ako; uwamange pamtima pako osaleka; uwalunze pakhosi pako.
Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.
Wolanda za atate, ndi wopirikitsa amai, ndiye mwana wochititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.
Atate wa wolungama adzasekeradi; wobala mwana wanzeru adzakondwera naye. Atate wako ndi amai ako akondwere, amai ako akukubala asekere.
Wosunga chilamulo ndiye mwana wozindikira; koma mnzao wa adyera achititsa atate wake manyazi.
Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makungubwi a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.
Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo;
Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamchitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.
Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?
Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.
Nanga mutani? Munthu anali nao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa. Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake analapa mtima napita. Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza. Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anavomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapite. Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.
Udziwa malamulo: Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amai ako.
Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.
Udziwa malamulo. Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amai ako.
Pamenepo Yesu pakuona amake, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu! Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amai wako. Ndipo kuyambira ora lomweli wophunzirayo ananka naye kwao.
Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), chifukwa cha umene ndili mtumiki wa m'unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.
Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.
Ngati mkazi wina wokhulupirira ali nao amasiye, iye awathandize, ndipo Mpingowo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu.
Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,
Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
Pakuti aliyense wakutemberera atate wake kapena mai wake azimupha ndithu; watemberera atate wake kapena amai wake; mwazi wake ukhale pamutu pake.
Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mau a atate wake, kapena mau a mai wake, wosawamvera angakhale anamlanga; azimgwira atate wake ndi mai wake, ndi kutulukira naye kwa akulu a mudzi wake, ndi ku chipata cha malo ake; pamenepo azituluka akulu anu ndi oweruza anu, nayese kumidzi yomzinga wophedwayo; ndipo anene kwa akulu a mudzi wake, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera. Pamenepo amuna onse a mudzi wake amponye miyala kuti afe; chotero muchotse choipacho pakati panu; ndipo Israele wonse adzamva, nadzaopa.
Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Yese; ndipo iye anafika ku linga la magaleta, napeza khamu lilikutuluka kunka poponyanira nkhondo lilikufuula.
Ndipo Davide anasiya akatundu ake m'dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nawalonjera abale ake.
Tsono Bateseba ananka kwa mfumu Solomoni kukanenera Adoniya kwa iye. Ndipo mfumu inanyamuka kukomana naye, namuweramira nakhalanso pa mpando wake wachifumu, naikitsa mpando wina wa amake wa mfumu, nakhala iye ku dzanja lake lamanja.
Ndipo Yeremiya anati kwa nyumba ya Arekabu, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa mwamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndi kusunga zonse anakulangizani inu, ndi kuchita monga mwa zonse anakuuzani inu; chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Yonadabu mwana wa Rekabu sadzasowa munthu wakuima pamaso panga kumuyaya.
Taonani, nthawi yachitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amai, koma atate ndi amai kuunjikira ana.
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.
Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye m'Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso. Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake.
Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa. Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu. Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake; ndipo idzani naye mwanawang'ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere; chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.
Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi.
Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita. Kawirikawiri nanga anapikisana ndi Iye kuchigwako, nammvetsa chisoni m'chipululu. Pakuti anabwerera m'mbuyo, nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Israele. Sanakumbukire dzanja lake, tsikuli anawaombola kwa msautsi. Amene anaika zizindikiro zake m'Ejipito, ndi zodabwitsa zake kuchidikha cha Zowani. Nasanduliza nyanja yao mwazi, ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa. Anawatumizira pakati pao mitambo ya ntchentche zakuwatha; ndi achule akuwaononga. Ndipo anapatsa mphuchi dzinthu dzao, ndi dzombe ntchito yao. Anapha mphesa zao ndi matalala, ndi mikuyu yao ndi chisanu. Naperekanso zoweta zao kwa matalala, ndi ng'ombe zao kwa mphezi. Anawatumizira mkwiyo wake wotentha, kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso, ndizo gulu la amithenga ochita zoipa. Anakhazika mboni mwa Yakobo, naika chilamulo mwa Israele, ndizo analamulira atate athu, akazidziwitse ana ao; Analambulira mkwiyo wake njira; sanalekerere moyo wao usafe, koma anapereka moyo wao kumliri. Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Ejipito, ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu. Koma anatulutsa anthu ake ngati nkhosa, nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'chipululu. Ndipo anawatsogolera mokhulupirika, kotero kuti sanaope; koma nyanja inamiza adani ao. Ndipo anawafikitsa kumalire a malo ake oyera, kuphiri ili, dzanja lamanja lake lidaligula. Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao. Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam'mwambamwamba, osasunga mboni zake; koma anabwerera m'mbuyo, nachita zosakhulupirika monga makolo ao, anapatuka ngati uta wolenda. Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao, namchititsa nsanje ndi mafano osema. Pakumva ichi Mulungu, anakwiya, nanyozatu Israele; kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa; amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao. ndipo anachokera chokhalamo cha ku Silo, chihemacho adachimanga mwa anthu; napereka mphamvu yake m'ukapolo, ndi ulemerero wake m'dzanja la msautsi. Naperekanso anthu ake kwa lupanga; nakwiya nacho cholandira chake. Moto unapsereza anyamata ao; ndi anamwali ao sanalemekezeke. Ansembe ao anagwa ndi lupanga; ndipo amasiye ao sanachite maliro. Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo; ngati chiphona chakuchita nthungululu ndi vinyo. Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo; nawapereka akhale otonzeka kosatha. Tero anakana hema wa Yosefe; ndipo sanasankhe fuko la Efuremu; koma anasankha fuko la Yuda, Phiri la Ziyoni limene analikonda. Ndipo anamanga malo oyera ake ngati kaphiri, monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha. Ndi kuti chiyembekezo chao chikhale kwa Mulungu, osaiwala zochita Mulungu, koma kusunga malamulo ake ndiko.
Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.
Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.
Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; motero nkhokwe zako zidzangoti thee, mbiya zako zidzasefuka vinyo. Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye. Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala. Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zamwamba ndi luntha. pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.
Mwananga, sunga mau anga, ukundike malangizo anga, Ndipo taona, mkaziyo anamchingamira, atavala zadama wochenjera mtima, ali wolongolola ndi wosaweruzika, mapazi ake samakhala m'nyumba mwake. Mwina ali kumakwalala, mwina ali kumabwalo, nabisalira pa mphambano zonse. Ndipo anagwira mnyamatayo, nampsompsona; nati kwa iye ndi nkhope yachipongwe, nsembe zamtendere zili nane; lero ndachita zowinda zanga. Chifukwa chake ndatuluka kudzakuchingamira, kudzafunitsa nkhope yako, ndipo ndakupeza. Ndayala zofunda pakama panga, nsalu zamawangamawanga za thonje la ku Ejipito, ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira a mure ndi chisiyo ndi sinamoni. Tiye tikondwere ndi chikondano mpaka mamawa; tidzisangalatse ndi chiyanjano. Pakuti mwamuna kulibe kwathu, wapita ulendo wa kutali; Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo; ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako. watenga thumba la ndalama m'dzanja lake, tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu. Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ake, ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake. Mnyamatayo amtsata posachedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa; ndi monga unyolo umadza kulanga chitsiru; mpaka muvi ukapyoza mphafa yake; amtsata monga mbalame yothamangira msampha; osadziwa kuti adzaononga moyo wake. Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, labadirani mau a m'kamwa mwanga. Mtima wako usapatukire kunjira ya mkaziyo, usasochere m'mayendedwe ake. Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa; ndipo ophedwa ndi iye achulukadi. Nyumba yake ndiyo njira ya kumanda, yotsikira kuzipinda za imfa. Uwamange pa zala zako, uwalembe pamtima pako.
Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, ngodala akusunga njira zanga. Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana.
Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.
Nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa. Ndinapita pa munda wa waulesi, polima mphesa munthu wosowa nzeru. Taonani, ponsepo panamera minga, ndi kuwirirapo khwisa; tchinga lake lamiyala ndi kupasuka. Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira, ndinaona ndi kulandira mwambo. Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono m'kugona, ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala; ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa. Kudziwa kudzaza zipinda zake ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake.
Mwamuna wokonda nzeru akondweretsa atate wake; koma wotsagana ndi akazi adama amwaza chuma.
woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nao ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse.
Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha.
m'zonse udzionetsere wekha chitsanzo cha ntchito zabwino; m'chiphunzitso chako uonetsere chosavunda, ulemekezeko, mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.
Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.
Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.
Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m'malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu; Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anabwera naye Zipora mkazi wa Mose (atamtuma kwao), ndi ana ake awiri; nuwamasulire malemba, ndi malamulo, ndi kuwadziwitsa njira imene ayenera kuyendamo, ndi ntchito imene ayenera kuchita. Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna amtima, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makhumi; ndipo iwo aweruze milandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti milandu yaikulu yonse abwere nayo kwa iwe; koma milandu yaing'ono yonse aweruze okha; potero idzakuchepera ntchito, ndi iwo adzasenza nawe. Ukachite chinthuchi, ndi Mulungu akakuuza chotero, udzakhoza kupirira, ndi anthu awa onse adzapita kwao mumtendere. Ndipo Mose anamvera mau a mpongozi wake, nachita zonse adazinena.
Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;
Mwananga, ukalandira mau anga, ndi kusunga malamulo anga; Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziwa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza; kukupulumutsa kunjira yoipa, kwa anthu onena zokhota; akusiya mayendedwe olungama, akayende m'njira za mdima; omwe asangalala pochita zoipa, nakondwera ndi zokhota zoipa; amene apotoza njira zao, nakhotetsa mayendedwe ao. Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake; wosiya bwenzi la ubwana wake, naiwala chipangano cha Mulungu wake. Nyumba yake itsikira kuimfa, ndi mayendedwe ake kwa akufa; onse akunka kwa iye sabweranso, safika kunjira za moyo; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira;
Menya mwanako, chiyembekezero chilipo, osafunitsa kumuononga. Munthu waukali alipire mwini; pakuti ukampulumutsa udzateronso.
nuwamasulire malemba, ndi malamulo, ndi kuwadziwitsa njira imene ayenera kuyendamo, ndi ntchito imene ayenera kuchita.
ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;
Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.
Ndipo wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiye Iye pa ndekha; chifukwa ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse.
Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso; ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro;
Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.
Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.
Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.
Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha.