Mulungu watipatsa malamulo, ndipo lachisanu limati: “Usaphe” (Ekisodo 20:13). Kuchotsa moyo wa munthu ndi tchimo lalikulu, chifukwa Mulungu amatilimbikitsa kukonda ndi kukhululukira mnzathu. Mulungu amakhululukira machimo athu onse ndipo amatipatsa mwayi watsopano, kodi ife ndife yani kuti tilephere kukhululukira ena? Khulupirira kuti Mulungu adzakuteteza. Iye amakukonda ndipo akufuna kuti uchotse chilakolako chilichonse cha kubwezera, uchotse m’maganizo mwako chilichonse chokhudza kupweteka ena. Mupemphe Mulungu kuti akuthandize, kuti amenyere nkhondo yako ndipo akupatsenso chipambano mosasamala kanthu za mmene zinthu zilili, chifukwa kukhala ndi maganizo oterewa mkati mwako sikudzapulumutsa moyo wako ku gehena. Bwerera kwa Mulungu lero, lapa ndi mtima wonse ndipo upereke kwa Iye chimene chikukuvutitsa. Mupemphe kuti chifuniro chake chichitike osati chako, usatenge chilungamo m’manja mwako. Tontholetsa mawu a mdani amene akukulimbikitsa kuchita zoyipa. Usalole kuti choyipa chikulamulire, koma gonjetsa choyipa ndi chabwino, motero Yesu adzakukondwera nawe ndipo udzatchedwa wolungama padziko lapansi.
Ndikudziwa kuti zingakhale zopweteka, ngakhale zovuta kwambiri, koma chonde lolera Mzimu Woyera kuti adzitamandire mwa iwe. Lero ndikupempha kuti udziwombole ndipo ulandire thandizo kuti usachite zinthu zimene pambuyo pake zidzakhala ndi vuto lalikulu. Sungani ufulu umene Khristu anakupatsa pamene anafera pa mtanda chifukwa cha iwe ndipo usagwere mumsampha woyipa wa Satana. Itana Yesu kuti alowe m’moyo mwako ndipo uyende naye, m’manja mwake muli chipambano chako chotsimikizika.
Aliyense wopha munthu, adzaphedwa. Nyama iliyonse yopha munthu, idzaphedwa. Munthu aliyense wopha mnzake, iyenso aphedwe. “Aliyense wopha munthu, nayenso adzaphedwa, pakuti munthu adalengedwa muchifaniziro cha Mulungu.
Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
“Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usaphe. Aliyense wopha mnzake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu,’
Koma mumvetsetse kuti saika malamulo chifukwa cha anthu olungama, koma chifukwa cha anthu osamvera, ndi osaweruzika, anthu ochimwa ndi osapembedza, monga anthu opha atate ao, amai ao, kapena anthu ena.
Pakuti Mulungu amene adanena kuti, “Usachite chigololo”, adanenanso kuti, “Usaphe”. Ngati inu chigololo simuchita, koma kupha mumapha, ndiye kutitu mwachimwira Malamulo onse. Tsono muzilankhula ndi kuchita zinthu monga anthu oti Mulungu adzaŵaweruza potsata lamulo loŵapatsa ufulu.
Ndiye amene adandipulumutsa kwa adani anga. Zoonadi Inu mudandikweza pamwamba pa ondiwukira, mudandilanditsa kwa anthu ankhanza.
“Koma ngati munthu amenya mnzake ndi chitsulo, mnzakeyo nkufa, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Ndipo wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa. Ngati munthu amenya mnzake ndi mwala, mwala wake woti nkupha munthu, mnzakeyo nafadi, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Tsono wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa. Kapena munthu akamenya mnzake ndi chibonga choti nkupha munthu, mnzakeyo nafadi, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Tsono wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa.
Mwina mwake munthu adana ndi mnzake, ndipo amkhalizira namupha mwadala, nkuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti apulumuke. Zikatero, akuluakulu akwao adzamuitanitse kuchokera ku mzinda wakewo, ndi kukampereka kwa woyenera kumlipsira uja kuti aphedwe ndithu. Musamchitire chifundo. Mchotseni pakati pa Aisraele munthu wopha mnzake wosalakwa, kuti zinthu zikuyendereni bwino.
Munthu amene wapalamula mlandu wopha mnzake, akhale womathaŵathaŵa mpaka kufa kwake. Wina aliyense asamthandize.
Iye adati, “Malamulo ake oti?” Yesu adayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama,
Kanthani adani anga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika pa ine. Muwononge onse ondizunza, pakuti ine ndine mtumiki wanu.
Udzafunafuna amene amakangana nawe, koma osaŵapeza. Amene amamenyana nawe nkhondo adzakhala ngati salinso kanthu.
“Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usaphe. Aliyense wopha mnzake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu,’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena.
“Aliyense wopha munthu, nayenso adzaphedwa, pakuti munthu adalengedwa muchifaniziro cha Mulungu.
Anthu amene amandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino ndiwo adani anga, chifukwa ine ndimachita zabwino.
Ulewe zabodza, zosinjirira. Usaphe munthu wosalakwa ndi wosapalamula, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.
Musaipitse dziko limene mukukhalamolo. Magazi amaipitsa dziko, ndipo nkosatheka kulipirira dziko chifukwa cha magazi amene akhetsedwa m'menemo, kupatula pokhetsa magazi a munthu amene adakhetsa magaziyo. Musaipitse dziko limene mukukhalamo, dziko limene Inenso ndikukhalamo. Paja Ine Chauta ndimakhala pakati pa Aisraele.”
Apo Yesu adamuuza kuti, “Bwezera lupangalo m'chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzaphedwa ndi lupanga.
Pajatu malamulo amene amati, “Usachite chigololo, usaphe, usabe, usasirire”, ndiponso malamulo ena onse, amaundidwa mkota m'lamulo ili lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Aliyense wodana ndi mnzake, ndi wopha anthu. Ndipo mukudziŵa kuti aliyense wopha anthu, alibe moyo wosatha mumtima mwake.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa,
Mumalakalaka zinthu, koma zimakusoŵani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.
Musabwezere choipa, ndipo musakwiyire anthu a mtundu wanu, koma mukonde mnzanu monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Ine ndine Chauta.
“Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Ukonde mnzako, ndi kudana ndi mdani wako.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.
Koma munthu akapha mnzake mwadala mwa njira yonyenga, aphedwe ndithu ngakhale wathaŵira ku guwa langa.
Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.
“Anthu aamuna akamayambana, ndipo nkupweteka mai wapathupi, maiyo napititsa padera, koma osafa, amene adampwetekayo adzalipira mtengo uliwonse umene mwamuna wa maiyo angadzatchule. Ndipo adzalipira monga momwe anthu oweruza anganenere. Koma maiyo akampweteka, chilango chake chidzakhala chotere: moyo kulipa moyo,
Musazunze alendo kapena ana amasiye kapena akazi amasiye. Musaphe anthu osachimwa pa malo ano. Musamatsate milungu ina, kuti ingakuwonongeni.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
“Atembereredwe onse olandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”
Popeza kuti iwo adaapitirirabe kumufunsa, Yesu adaŵeramuka naŵauza kuti, “Pakati panupa amene sadachimwepo konse, ayambe ndiye kumponya mwala maiyu.”
“Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo ikanthidwa nkufa, asalipsire magazi chifukwa cha mbalayo. “Aliyense wopereka nsembe kwa milungu, osati kwa Chauta yekha, aphedwe ameneyo. “Musazunze mlendo kapena kumkhalitsa m'phanthi, poti paja inunso munali alendo ku dziko la Ejipito. Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. Mukamaŵazunza, Ine ndidzaŵamva iwowo akamalira kwa Ine. Ndidzakukwiyirani, ndipo ndidzakuphani ku nkhondo. Akazi anu adzasanduka amasiye, ndipo ana anunso adzasanduka amasiye. “Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja. Mukatenga mwinjiro wa munthu wina ngati chigwiriro kuti adzakulipireni, muubweze dzuŵa lisanaloŵe, poti chofunda nchokhacho, ndicho chotetezera thupi lake. Nanga adzafunda chiyani? Akalira kwa Ine iyeyu kuti ndimthandize, ndidzamuyankha chifukwa ndine wachifundo. “Musanyoze Mulungu, ndipo musatemberere mtsogoleri wa anthu anu. “Musachedwe kundipatsa zopereka zotapa pa zokolola zanu zambiri ndiponso pa vinyo wanu wochuluka. “Mundipatse ana anu achisamba aamuna. Koma ikaphedwa dzuŵa litatuluka, apo padzakhala kulipsira magazi. Pajatu wakuba aliyense ayenera kulipira ndithu. Ngati mbala igwidwa, ndipo ilephera kulipira mlandu, aigulitse chifukwa cha kubako.
Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
“Koma inu amene mukumva mau anga, ndikukuuzani kuti, Muzikonda adani anu, muziŵachitira zabwino amene amadana nanu. Muziŵafunira madalitso amene amakutembererani, muziŵapempherera amene amakuvutitsani.
Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse. Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Tsono Mulungu adalankhula mau onseŵa, adati, Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako. Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera. “Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa. “Usaphe.” “Usachite chigololo.” “Usabe.” “Usachite umboni womnamizira mnzako.” “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”
Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.
Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Muzidzachita zimenezi kuti musadzalakwe pakupha anthu osachimwa m'dziko limene Chauta akukupatsanilo.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.
Chauta aonetse kuti wolakwa ndani pakati pa ine ndi inu. Akulangeni chifukwa cha zimene mukundichitazi. Koma ine sindikupwetekani, ai.
Mdani wako akakhala ndi njala, umpatse chakudya, akamva ludzu, umpatse madzi akumwa. Potero udzamchititsa manyazi aakulu, ndipo Chauta adzakupatsa mphotho.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.
Mukamatambasula manja anu popemphera, sindidzayang'anako. Ngakhale muchulukitse mapemphero anu chotani, sindidzasamalako, chifukwa manja anu ndi odzaza ndi magazi. Sambani, dziyeretseni, chotsani pamaso panga ntchito zanu zoipa. Inde, lekani kuchita zoipa. Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”
Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziŵeto zake, koma munthu woipa mtima chifundo chake nchankhwidzi.
Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Nali lamulo lokhalira munthu wopha mnzake, amene angapulumutse moyo wake pothaŵira kumeneko: Munthu akapha mnzake mwangozi, osati chifukwa cha chidani, athaŵire ku mzinda uliwonse mwa mizinda imeneyo kuti apulumuke. Mwachitsanzo, anthu aŵiri apita ku thengo limodzi kukadula mitengo. Wina podula mtengo, nkhwangwa nkuguluka, nipha mnzakeyo. Iye angathe kuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, napulumuka. Akapanda kutero, mwina chifukwa cha kutalika kwa mtunda, wachibale wofuna kumlipsira adzamthamangira mwaukali, nkumugwira wothaŵayo namupha, ngakhale ali wosayenera kuphedwa, chifukwa paja popha munthu mwangozi analibe chidani chilichonse ndi amene adafayo.
Koma makamaka, monga mau a Mulungu akunenera, “Ngati mdani wako wamva njala, iwe umpatse chakudya. Ngati wamva ludzu, iwe umpatse madzi akumwa. Ukatero udzamchititsa manyazi kwambiri.” Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.
Koma ikakhala ngozi, kuti sadaganize konse zomupha mnzakeyo, angathe kuthaŵira ku malo amene ndidzakupatsani.
Muzitipempherera ifeyo, pakuti sitipeneka konse kuti tili ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndipo tatsimikiza kuchita zonse mwachilungamo.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.