Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, tchimo lopita ku imfa ndi tchimo limene timachita modziwa bwino, mobwerezabwereza, popanda kulapa. Mulungu watiitana ife ana ake kukhala m’chiyero (1 Petro 1:16), ndipo Mulungu amatilangiza tikachimwa.
Sitikulangidwa chifukwa cha machimo athu mpaka kutaya chipulumutso chathu kapena kulekanitsidwa ndi Mulungu kosatha, koma Mulungu amatitsutsa. Pakuti Ambuye am’tsutsa iye amene am’konda, ndipo am’kwapula aliyense amene am’vomereza kukhala mwana wake (Ahebri 12:6).
Kale, tisanakhale ndi Yesu mumtima mwathu, tinali akufa chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa zathu, koma Yesu anafa ndi kuuka kuti tikhale ndi moyo wochuluka. Chifukwa cha ichi, palibe chiweruzo cha tchimo kwa ife amene timavomeza machimo athu, kulapa, ndi kusiya machimo, chifukwa cha nsembe ya Yesu Khristu. Lero mungasangalale ndi moyo woyera, chifukwa magazi ake amatitsuka, amatikhululukira, ndi kutiyeretsa ku zoipa zonse.
Tsiku lililonse, mukadzuka, yanjanani ndi Mulungu wanu, siyani njira zanu zoipa, lapani machimo anu, ndipo mudzapeza chifundo cha Ambuye nthawi zonse. Kumbukirani kuti popanda Khristu sitingathe kuchita chilichonse, ndipo mwa Iye muli chitsimikizo chonse cha kusangalala ndi moyo waufulu.
Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa.
Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.
Wina akaona mbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere, ndipo Mulungu adzampatsa moyo mbale wakeyo. Ndikunenatu za ochita tchimo losadzetsa imfa. Koma lilipo tchimo lina lodzetsa imfa, za tchimo limenelo sindikunena kuti apemphere ai.
Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu.
Ife tikudziŵa kuti mu imfa tidatulukamo nkuloŵa m'moyo, popeza kuti timakonda anzathu. Munthu amene sakonda mnzake, akali mu imfa.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Wobisa machimo ake sadzaona mwai, koma woulula ndi kuleka machimo, adzalandira chifundo.
Tsono tembenukani mtima ndi kubwerera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthaŵi ya mpumulo,
Kodi tsono ndiye kuti chinthu chabwinochi chidandiphetsa? Mpang'ono pomwe. Koma uchimo ndiwo udandipha pakugwiritsa ntchito chinthu chabwinocho kuti khalidwe lenileni la uchimowo liwonekere poyera kuti ndi uchimodi. Motero kudzera mwa malamulo, uchimo umaoneka woipa kopitirira.
Yesu adaŵayankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo.
Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni.
Ululu wake wa imfa ndi uchimo, ndipo chimene chimapatsa uchimo mphamvu, ndi Malamulo.
Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita.
Pamene tinkatsata mkhalidwe wathu wachibadwa, zilakolako zoipa zimene Malamulo adaaziwutsa zinkagwira ntchito mwa ife, ndipo zidabala imfa.
Nanga pamenepo mudapindula chiyani pakuchita zinthu zimene tsopano mukuchita nazo manyazi? Pajatu zimene zija mathero ake ndi imfa.
Pamakhala njira ina yooneka yowongoka kwa munthu, koma kumapeto kwake imakhala njira ya ku imfa.
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.
Tsono uchimo sudzakhalanso ndi mphamvu pa inu, pakuti chimene chimalamulira moyo wanu si Malamulo ai koma kukoma mtima kwa Mulungu.
“Munthu akachimwa pochita mosadziŵa zimene Chauta amaletsa, ndi wopalamulabe ndithu ameneyo, ndipo ndi woyenera kumlanga.
Monga munthu wokhuta vinyo ali wosokonezeka, chonchonso munthu wodzitama ndi wosakhazikika. Ndi waumbombo kwambiri ngati manda, ngati imfa amakhala wosakhuta. Amagwira anthu a mitundu yonse, amaŵasonkhanitsa ngati ake.”
Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
kupatula mtengo wokhawo umene umadziŵitsa zabwino ndi zoipa. Zipatso za mtengo umenewo usadye. Ukadzadya, ndithu udzafa!”
Udzayenera kukhetsa thukuta kuti upeze chakudya, mpaka udzabwerera kunthaka komwe udachokera. Udachokera ku dothi, udzabwereranso kudothi komweko.”
Moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa mwana ndi wanga, wa bambo ndi wanganso. Munthu amene wachimwa, ndiye amene adzafe.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni. Tayani zoipa zanu zonse zakale zimene mudachimwira Ine. Mukhale ndi mtima watsopano ndi nzeru zatsopano. Nanga muferenji, inu anthu a ku Israele? Sindikondwera nayo imfa ya munthu wina aliyense. Nchifukwa chake lapani, kuti mukhale ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.
Wina akaona mbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere, ndipo Mulungu adzampatsa moyo mbale wakeyo. Ndikunenatu za ochita tchimo losadzetsa imfa. Koma lilipo tchimo lina lodzetsa imfa, za tchimo limenelo sindikunena kuti apemphere ai. Chinthu chilichonse chosalungama ndi tchimo, koma pali lina tchimo losadzetsa imfa.
Zoonadi, ndidabadwa mu uchimo, ndinali mu uchimo kuyambira pamene mai wanga adatenga pathupi pa ine.
“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri.
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
Kale inu munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu. Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite. Inu amene mtundu wanu sindinu Ayuda, kumbukirani m'mene munaliri kale. Ayuda amadzitchula oumbala, chifukwa cha mwambo umene amachita pa thupi lao, ndipo inu amakutchulani osaumbala. Tsono kumbukirani kuti nthaŵi imene ija munali opanda Khristu. Munali alendo, ndipo simunali a mtundu wa anthu osankhidwa ndi Mulungu. Munali opanda gawo pa zimene Mulungu, mwa zipangano zake, adaalonjeza anthu ake. Munkakhala pansi pano opanda chiyembekezo, opandanso Mulungu. Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu. Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa. Iye adathetsa Malamulo a Mose pamodzi ndi malangizo ake ndi miyambo yake. Adachita zimenezi kuti kuchokera ku mitundu iŵiri ija, alenge mtundu umodzi watsopano, wokhala mwa Iye, kuti choncho adzetse mtendere. Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu. Khristu adadzalalika Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu a mitundu inanu, amene munali kutali ndi Mulungu, ndiponso kwa Ayuda, amene anali pafupi naye. Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya. Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera. Nthaŵi imene ija ifenso tonse tinali ndi moyo wonga wao, ndipo tinkatsata zilakolako za khalidwe lathu lokonda zoipa. Tinkachitanso zilizonse zimene matupi athu ndi maganizo athu ankasirira. Nchifukwa chake, mwachibadwa chathu, tinali oyenera mkwiyo wa Mulungu, monga anthu ena onse.
Zoipa za munthu woipa zimamtchera msampha iyeyo, ntchito za machimo ake zimamkwidzinga. Amafa chifukwa chosoŵa mwambo, amatayika chifukwa cha uchitsiru wake waukulu.
Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu, ndipo Iye wakufulatirani chifukwa cha machimo anuwo. Choncho saamva zimene inu mumanena.
Chilango chao nchakuti adzaonongedwa kwamuyaya, sadzaona konse nkhope ya Ambuye kapena ulemerero wa mphamvu zake,
“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.
Iye adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. Anthu amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pakuchita ntchito zabwino molimbikira, Mulungu adzaŵapatsa moyo wosatha. Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira.
Moyo ndiye malipiro a anthu ochita zabwino, koma phindu la ochimwa limadzetsa machimo ena.