Ndikukuuzani inu, Bukhu la Chivumbulutso limatiuza za Nyanja ya Moto, malo omwe Mulungu anakonzeratu kuti mwina adzazunzike Satana, angelo ake, ndi anthu onse omwe mayina awo sanalembedwe m'Buku la Moyo. Iwo amene sanalandire chipulumutso cha Yesu Khristu.
Monga mmene Chivumbulutso 21:8 imanenera, "Koma amantha, osakhulupirira, onyansa, ambanda, ochita chigololo, olowa, opembedza mafano, ndi onse onama, gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto ndi sulufule, ndicho chifa chachiŵiri." Yesu Khristu ndiye njira yokha yopita Kumwamba.
Ngati simukufuna kuzunzika kosatha, funani Yesu, mupemphe chikhululukiro pa machimo anu, ndipo yambani kutsatira ziphunzitso zake. Mukatero, mudzamasulidwa ku zinthu zomwe zimakuvutitsani ndipo mudzakhala okonzeka pamene Yesu adzabwera kudzatenga mpingo wake.
Kufa muli mwa Khristu ndi phindu lalikulu, koma kukhala opanda Iye ndi kuvutika. Yesetsani kuti dzina lanu lilembedwe m'Buku la Moyo kuti mudzalowe ufumu wa Ambuye wathu, amene ndi woyenera ulemerero wonse, ulemu, ndi kukhulupirika.
Wamoyo uja ndine. Ndidaafa, koma tsopano ndili moyo mpaka muyaya. Imfa ndi Malo a anthu akufa makiyi ake ali ndi Ine.
Masiku amenewo anthuwo adzafunafuna imfa, koma osaipeza. Adzafunitsitsa kufa, koma imfa izidzaŵathaŵa.
Umodzi mwa mitu yake unkaoneka ngati uli ndi bala lofa nalo, koma balalo linali litapola. Pamenepo anthu onse ankachitsata chilombocho ali odabwa.
Ngodala anthu amene adzauke nao pa kuuka koyamba kumeneku. Ameneŵa ndiwo akeake a Mulungu. Imfa yachiŵiri ilibe mphamvu pa iwo, koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Yesu Khristu, ndipo azidzalamulira pamodzi naye zaka chikwi chimodzi.
Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”
Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”
Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zidaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.
“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, siidzamkhudza imfa yachiŵiri.”
Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.
Lirani kwamphamvu pakuti tsiku la Chauta layandikira. Likubwera ndi chiwonongeko chochokera kwa Mphambe.
Nditayang'ana, ndidaona kavalo wotuŵa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa, ndipo Malo a anthu akufa ankamutsata pambuyo. Aŵiriwo adaalandira ulamuliro pa chimodzi mwa zigawo zinai za dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi nkhondo, njala, nthenda, ndi zilombo zolusa.
Dziko lapansi lidzathyokathyoka, lidzang'ambika kwathunthu ndi kugwedezeka kwamphamvu. Aliyense adzaona zimodzimodzi: ansembe ndi anthu, akapolo aamuna ndi ambuyao aamuna, adzakazi ndi ambuyao aakazi, ogula ndi ogulitsa, obwereka ndi oŵabwereka, ndiponso okongola ndi okongoza. Dziko lapansi lidzadzandira ngati munthu woledzera, lidzagwedezeka ngati chisimba nthaŵi ya mkuntho. Dziko lapansi lalemedwa ndi zoipa zake, lidzagwa ndipo silidzaukanso.
Pambuyo pake ndidamva mau ochokera Kumwamba. Adati, “Lemba kuti, Ngodala anthu akufa amene kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno afa ali otumikira Ambuye.” Mzimu Woyera akuti, “Inde, ngodaladi. Akapumule ntchito zao zolemetsa, pakuti ntchito zaozo zimaŵatsata.”
(Akufa ena onse sadaukenso mpaka zitatha zaka zomwezo chikwi chimodzi.) Kumeneku ndiye kuuka koyamba.
Musachite nazo mantha zoŵaŵa zimene mukukakumana nazo. Ndithu enanu Satana adzakuponyetsani m'ndende kuti akuyeseni, ndipo mudzazunzika pa masiku khumi. Khalani okhulupirika mpaka kufa, ndipo ndidzakupatsani moyo ngati mphotho yanu.
Ana akenso ndidzaŵapha. Motero mipingo yonse idzazindikira kuti Ine ndine uja ndimadziŵa za m'mitima mwa anthu ndi za m'maganizo mwao. Aliyense mwa inu ndidzachita naye molingana ndi ntchito zake.
Nchifukwa chake miliri yomugwera idzamufikira pa tsiku limodzi. Miliriyo ndi iyi: nthenda, chisoni, ndi njala. Ndipo adzamtentha ndi moto. Pakuti ndi amphamvu Ambuye Mulungu amene amuweruza.”
Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake.
Nditamuwona, ndidagwa kumapazi kwake ngati munthu wakufa. Koma Iye adandisanjika dzanja lake lamanja nati, “Usaope. Woyamba ndiponso Wotsiriza ndine.
Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka magazi, tsiku lalikulu ndi loopsa la Chauta lisanafike.
Tsoka kwa inu amene mumalilakalaka tsiku la Chauta! Kodi tsiku limenelo lidzakupinduliraninji inuyo? Kudzakhalatu mdima, osati kuŵala ai. Kudzakhala monga m'mene kumachitira munthu akamathaŵa mkango, ndipo akumana ndi chimbalangondo, kapena monga munthu woti wakaloŵa m'nyumba, atsamira chipupa ndi dzanja lake, njoka nkumuluma. “Namwali Israele wagwa chonse osati nkudzukanso ai. Wagwa ndi kuiŵalika pa dziko lake, popanda wina womdzutsa.” Kodi suja tsiku la Chauta ndi mdima wokhawokha osati kuŵala, kodi suja lili ngati usiku wabii wopanda mpoti mbee pomwe!
Onani, tsiku likubwera, la Chauta, pamene zinthu zomwe adani ako adakulanda, azidzagaŵana iwe uli pomwepo. Dziko lonse adzalisalaza kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu. Koma Yerusalemu adzakwezedwa pamalo pakepo, kuyambira ku chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene kunali chipata chakale mpaka ku chipata chapangodya, ndiponso kuchokera ku Nsanja ya Hananele mpaka ku malo opondera mphesa za mfumu. Anthu adzakhala ku Yerusalemu mwamtendere, poti sadzaopsezedwanso ndi chiwonongeko kumeneko. Pambuyo pake Chauta adzalanga ndi mliri adani onse amene ankamenyana nkhondo ndi Yerusalemu. Matenda ake adzakhala motere: matupi ao adzaola eni ake akuyendabe, maso ao adzaola ali chikhalire m'malo mwake, ndipo malilime ao adzaola m'kamwa mwao. Pa tsiku limenelo Chauta adzasokoneza anthu ndi mantha aakulu, mpaka aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndipo adzayamba kumenyana okhaokha. Nawonso anthu a ku Yuda adzachita nkhondo ku Yerusalemu. Ndipo chuma cha anthu a mitundu yozungulira adzachisonkhanitsa pamodzi. Chuma chake ndi golide ndi siliva wambiri ndiponso zovala zochuluka. Mliri uja udzaphanso akavalo, ngamira ndi abulu a mitundu yonse, ndiponso nyama zonse zokhala ku zithando zankhondo. Zitatha zimenezi anthu onse otsala mwa adani amene ankamenyana ndi Yerusalemu, azidzabwera chaka ndi chaka kudzapembedza Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse, ndiponso kudzachita chikondwerero chamisasa. Ngati mabanja ena pa dziko lapansi sadzapita ku Yerusalemu kukapembedza Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse, mvula sidzaŵagwera. Ngati anthu a ku Ejipito sadzapita kukaonekera kumeneko, adzalandiranso chilango chonga chomwe Chauta adzalange nacho mtundu wina uliwonse wa anthu osapita kukachita chikondwerero chamisasa. Chimenechi ndicho chidzakhale chilango cha Aejipito ndiponso cha mtundu uliwonse wa anthu amene sadzachita nao chikondwerero chamisasacho. Chauta adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu. Adzaulanda mzindawo ndi kuphwasula nyumba zonse, ndipo akazi am'menemo adzaŵachita chigololo. Theka la anthu a mu mzindawo lidzatengedwa ukapolo, koma ena onse otsala mumzindamo sadzachotsedwa.
Chifukwa masautso amene adzaoneka masiku amenewo, sanaonekepo chilengedwere dziko lapansi mpaka pano, ndipo sadzaonekanso. Masiku amenewo, akadapanda kuŵachepetsa, sakadapulumukapo munthu ndi mmodzi yemwe. Koma Mulungu adzaŵachepetsa masikuwo chifukwa cha anthu amene Iye adaŵasankha.
“Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, dzuŵa lidzada, mwezi udzaleka kuŵala, nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka. Tsono Yesu atakhala pansi, pa Phiri la Olivi, ophunzira ake adadza kwa Iye paokha. Adamufunsa kuti, “Tatiwuzani, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti nthaŵi yakwana ya kubweranso kwanu, ndiponso ya kutha kwa dziko lapansi?” Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka ku thambo. Anthu a mitundu yonse ya pansi pano adzayamba kulira, ndipo adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Kudzamveka lipenga lamphamvu, ndipo Iye adzatuma angelo ake, kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.”
“Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa; amadziŵa ndi Atate okha basi.
“Nanunso tsono, khalani maso, chifukwa simudziŵa tsiku limene Ambuye anu adzabwere. Koma dziŵani kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi yofika mbala, bwenzi atakhala maso, osalola kuti mbala imuthyolere nyumba. Choncho inunso muzikhala okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene inu simukuyembekeza.”
“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera ndi ulemerero wake, pamodzi ndi angelo onse, adzachita kukhalira pa mpando wake wachifumu. Adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse pamaso pake, ndipo adzaŵalekanitsa monga momwe mbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi.
“Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa, amadziŵa ndi Atate okha basi. Tsono chenjerani, khalani maso, chifukwa simudziŵa kuti nthaŵiyo idzakwana liti.
Choncho inunso khalani okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene simukuyembekeza.”
“Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuŵa, pa mwezi ndi pa nyenyezi. Pansi pano anthu a mitundu yonse adzada nkhaŵa nkutha nzeru, pomva kukokoma kwa nyanja ndi mafunde ake. Ena adzakomoka ndi mantha poyembekezera zimene zikudza pa dziko lonse lapansi, pakuti mphamvu zonse zakuthambo zidzagwedezeka.
“Chenjerani kuti mitima yanu ingapusitsidwe ndi maphwando, kuledzera, ndi kudera nkhaŵa za moyo uno, kuti tsikulo lingakufikireni modzidzimutsa. Pajatu lidzaŵagwera ngati msampha anthu onse okhala pa dziko lonse lapansi. Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso. Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao. Mundikhulupirire kuti Ine ndimakhala mwa Atate ndipo Atate amakhala mwa Ine. Kupanda apo, khulupiriranitu chifukwa cha ntchito zanga zomwezo. Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate. Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.” “Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse. Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu. Sindidzakusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ndidzabweranso kwa inu. Kwangotsala kanthaŵi pang'ono, ndipo anthu ongokonda zapansipano sadzandiwonanso, koma inu mudzandiwona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo. Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu. “Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.” Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. “Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani. “Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine.
Ndidzachita zozizwitsa ku thambo lakumwamba, ndipo pansi pano zizindikiro izi: magazi, moto ndi utsi watolotolo. Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo. Dzuŵa lidzangoti bii ngati mdima ndipo mwezi udzangoti psuu ngati magazi, lisanafike tsiku la Ambuye Mulungu lalikulu ndi laulemerero.
Chifukwa adaika tsiku pamene Iye adzaweruza anthu a pa dziko lonse lapansi molungama kudzera mwa Munthu amene Iye adamsankha. Adatsimikizira anthu onse zimenezi pakuukitsa Munthuyo kwa akufa.”
Mvetsetsani, ndikuuzeni chinsinsi. Sikuti tonse tidzamwalira, komabe tonse tidzasandulika. Zidzachitika mwadzidzidzi, pa kamphindi ngati kuphethira kwa diso, pamene lipenga lotsiriza lidzalira. Likadzaliratu lipengalo, akufa adzauka ndi matupi amene sangaole, ndipo ife tidzasandulika.
Padzakhala mfuu wa mau a mngelo wamkulu ndi wa lipenga la Mulungu. Ndipo pamenepo Ambuye mwini adzatsika kuchokera Kumwamba. Anthu amene adafa akukhulupirira Khristu, adzayamba ndiwo kuuka. Pambuyo pake ife amoyofe, otsalafe, tidzatengedwa pamodzi nawo m'mitambo kuti tikakumane ndi Ambuye mu mlengalenga. Motero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse.
Inu nomwe mukudziŵa bwino kuti tsiku la Ambuye likadzafika ngati mbala yausiku. Musanyoze mau olalikidwa m'dzina la Mulungu, koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino, ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse. Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu. Iye amene akukuitanani ngwokhulupirika, ndipo adzakuchitirani zimenezi. Abale, muzitipempherera. Abale onse muŵapatseko moni mwachikondi. M'dzina la Ambuye ndikukulamulani kuti kalatayi muŵaŵerengere abale onse. Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima. Pamene anthu azikati, “Pali mtendere, tili pabwino”, pamenepo chiwonongeko chidzaŵagwera modzidzimutsa. Chidzaŵadzidzimutsa monga momwe zoŵaŵa zimamchitira mkazi pa nthaŵi yoti achire; ndipo sadzatha konse kuchizemba.
Pa za kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso za kusonkhana kwathu kuti tikakumane naye, tifuna kukupemphani kanthu, abale. Mwa njira iliyonse adzanyenga anthu amene adzaonongedwa chifukwa chokana kukonda choona chimene chikadaŵapulumutsa. Nchifukwa chake Mulungu adzatumiza mphamvu zoŵasokoneza, kuti akhulupirire zonama. Motero adzalangidwa onse amene sadakhulupirire choona, koma adakondwerera kusalungama. Koma ife tikuyenera kumathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, amene Ambuye amakukondani. Paja Mulungu adakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke. Mudapulumuka chifukwa Mzimu Woyera adakusandutsani anthu akeake a Mulungu, ndipo mudakhulupirira choona. Mulungu adakuitanirani zimenezi kudzera mwa Uthenga Wabwino umene tidakulalikirani. Adakuitanani kuti mulandire nao ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu. Tsono abale, khalani olimbika, ndipo mugwiritse miyambo imene tidakuphunzitsani ndi mau apakamwa kapena am'makalata. Mulungu Atate athu adatikonda, ndipo mwa kukoma mtima kwake adatipatsa kulimba mtima kosatha ndi chiyembekezo chokoma. Iye pamodzi ndi Yesu Khristu Ambuye athu athuzitse mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu za kuchita ndi kulankhula zabwino zilizonse. Maganizo anu asasokonezeke msanga, ndipo musaopsedwe ndi mau akuti, “Tsiku la Ambuye lafika,” ngakhale anene kuti mauwo ngochokera kwa Mzimu Woyera, kapena kuti taŵanena ndife, kapena tachita kuŵalemba m'kalata. Musalole kuti wina akupusitseni mwa njira iliyonse. Pajatu lisanafike tsikulo, kudzayamba kwachitika zoti anthu ochuluka akupandukira Mulungu, ndipo kudzaoneka Munthu Woipitsitsa uja, woyenera kutayikayu. Ameneyu ndi mdani, ndipo adzadziika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza, kotero kuti mwiniwakeyo adzadzikhazika m'Nyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.
Tsono pamenepo Munthu Woipitsitsa uja adzaululuka. Ndipo Ambuye Yesu adzamthetsa ndi mpweya wa m'kamwa mwake, nkumuwonongeratu ndi maonekedwe ake aulemerero a kubwera kwake.
Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.
Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta. Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi. Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe. Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa. Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu. Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino, opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu. Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.
Pajatu tikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tikuyembekeza, pamene Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu adzaonetsa ulemerero wake.
Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.
Tsono abale, khazikani mtima pansi mpaka Ambuye adzabwere. Onani m'mene amachitira mlimi. Amadikira kuti zipatso zokoma ziwoneke m'munda mwake. Amangoyembekeza mokhazika mtima kuti zilandire mvula yachizimalupsa ndi yachikokololansanu. Inunso khazikani mtima. Limbani mtima, pakuti Ambuye ali pafupi kubwera.
Chimalizo cha zonse chayandikira. Nchifukwa chake khalani ochenjera ndi odziletsa, kuti muthe kupemphera.
Choyamba mumvetse izi: pa masiku otsiriza kudzafika anthu olalata, otsata zilakolako zao zoipa. Azidzalalata nkumanena kuti, “Kodi suja Ambuye adalonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nkale adamwalira makolo athu, koma zonse zili monga momwe Mulungu adazilengera poyamba paja.”
Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikulo zakumwamba zidzatha ndi phokoso loopsa. Zinthu zonse zidzayaka moto nkusungunuka, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili m'menemo zidzapseratu.
Ananu, ino ndi nthaŵi yotsiriza. Mudamva kuti kukubwera Woukira Khristu, ndipo tsopano aoneka kale ambiri oukira Khristu. Zimenezi zikutizindikiritsa kuti ino ndi nthaŵi yotsirizadi.
Enoki, wa mbadwo wachisanu ndi chiŵiri kuyambira pa Adamu, adaalosa za anthu okhaokhaŵa pamene adati, “Onani, Ambuye akubwera ndi angelo ake osaŵerengeka, kuti adzaweruze anthu onse. Adzagamula kuti ngolakwa onse osasamala za Mulungu, chifukwa cha ntchito zao zonse zosalungama, zimene adachita mosaopa Mulungu. Adzaŵatsutsa chifukwa cha mau onse achipongwe amene iwo, anthu ochimwa ndi onyozera za Mulungu, adanyoza nawo Ambuye.”
Mvetsetsani! Akubwera pa mitambo! Aliyense adzamuwona, amene adamubaya aja nawonso adzamuwona. Ndipo anthu a mitundu yonse pansi pano adzalira chifukwa cha Iye. Nzoonadi zimenezi. Ndithudi!
Popeza kuti mwasunga mau anga oti mupirire mosatepatepa, Inenso ndidzakusungani pa nthaŵi yamayeso imene ilikudza m'dziko lonse lapansi, kuti anthu onse okhalamo adzayesedwe.
Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chimodzi. Ndipo padachitika chivomezi champhamvu. Dzuŵa lidadzangoti bii ngati chiguduli chakuda, mwezi wathunthu nkungoti psuu ngati magazi. Nyenyezi zakuthambo zidagwa pansi, ngati muja zimayoyokera nkhuyu zaziŵisi, mkuyu ukamagwedezeka ndi mphepo yamkuntho. Thambo lidachoka monga momwe imakulungidwira mphasa akamaiyalula. Ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zidachotsedwa m'malo mwake.
Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adaliza lipenga lake. Atatero kumwamba kudamveka mau okweza. Mauwo adati, “Tsopano mphamvu zolamulira dziko lapansi zili m'manja mwa Ambuye athu ndi mwa Wodzozedwa wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”
Chinkakakamiza anthu onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, ndiye kuti dzina la chilombo choyamba chija, kapena nambala yotanthauza dzina lake.
“Mvetsetsani! Ndikubwera ngati mbala. Ngwodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuwopa kuti angamayende osavala, ndipo anthu angaone maliseche ake.”
Pambuyo pake ndidaona Kumwamba kutatsekuka, kavalo woyera nkuwoneka. Wokwerapo wake dzina lake ndi “Wokhulupirika”, ndiponso “Woona.” Poweruza, ndi pomenya nkhondo, amachita molungama. Maso ake anali psuu ngati malaŵi a moto, ndipo pamutu pake panali zisoti zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lolidziŵa iye yekha, osati wina aliyense. Chovala chake chinali choviika m'magazi, ndipo ankatchedwa, “Mau a Mulungu.” Magulu a ankhondo a Kumwamba ankamutsatira atakwera akavalo oyera, ndipo iwowo atavala zabafuta, zoyera ndi zangwiro. M'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa lotulukira kunja, loti adzalangire mitundu ya anthu. Adzaŵalamulira ndi ndodo yachitsulo, ndipo m'chopondera mphesa adzaponda mphesa za vinyo wa mkwiyo waukali wa Mulungu Mphambe. Pa mkanjo wake, ndi pantchafu pake padaalembedwa dzina loti, “Mfumu ya mafumu onse, ndi Mbuye wa ambuye onse.”
Pambuyo pake ndidaona mngelo akutsika kuchokera Kumwamba. M'manja mwake anali ndi kiyi ya Chiphompho chija, ndiponso unyolo waukulu. Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya. Pambuyo pake ndidaona mpando wachifumu woyera, waukulu, ndiponso amene amakhalapo. Dziko lapansi ndi thambo zidathaŵa pamaso pake, ndipo sizidapezekenso konse. Ndidaonanso anthu akufa, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja, ndipo mabuku adafutukulidwa. Adafutukula buku linanso, limene lili buku la amoyo. Tsono anthu akufawo adaweruzidwa poyang'anira ntchito zao monga momwe zidaalembedwera m'mabukumo. Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake. Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zidaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri. Aliyense wopezeka kuti dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo lija, adaponyedwa m'nyanja yamotoyo. Adagwira Chinjoka chija, ndiye kuti njoka yakale ija yotchedwa Mdyerekezi ndiponso Satana, nachimanga zaka chikwi chimodzi. Kenaka adachiponya m'Chiphompho muja, nachitsekera nkumatirira potsekerapo kuti chisadzanyengenso mitundu ya anthu mpaka zitatha zaka zija chikwi chimodzi. Zitatha zakazo ayenera kudzachimasulanso nthaŵi pang'ono.
Pambuyo pake ndidaona mpando wachifumu woyera, waukulu, ndiponso amene amakhalapo. Dziko lapansi ndi thambo zidathaŵa pamaso pake, ndipo sizidapezekenso konse. Ndidaonanso anthu akufa, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja, ndipo mabuku adafutukulidwa. Adafutukula buku linanso, limene lili buku la amoyo. Tsono anthu akufawo adaweruzidwa poyang'anira ntchito zao monga momwe zidaalembedwera m'mabukumo.
Pambuyo pake ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Paja thambo loyamba lija ndi dziko lapansi loyamba lija zinali zitazimirira, ndipo nyanja panalibenso. Pamenepo mngelo uja adandinyamula chamumzimu nakanditula pa phiri lalikulu ndi lalitali. Adandiwonetsa Mzinda Woyera uja, Yerusalemu, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unkaŵala ndi ulemerero wa Mulungu. Kuŵala kwake kunali ngati kuŵala kwa mwala wamtengowapatali, ngati mwala wambee, wonyezimira ngati galasi. Mzindawo unali ndi linga lalikulu ndi lalitali. Lingalo linali ndi zipata khumi ndi ziŵiri, pazipatapo panali angelo khumi ndi aŵiri, ndipo pa zitseko zake padaalembedwa maina a mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele. Pa mbali zonse zinai za mzindawo panali zipata zitatuzitatu: kuvuma zitatu, kumwera zitatu, kumpoto zitatu, kuzambwe zitatu. Linga la mzindawo lidaamangidwa pa maziko khumi ndi aŵiri, ndipo pamazikopo padaalembedwa maina a atumwi khumi ndi aŵiri a Mwanawankhosa uja. Mngelo amene ankalankhula naneyo anali ndi ndodo yoyesera yagolide, yoti ayesere mzinda uja, zipata zake ndi linga lake. Mzindawo unali wolingana ponseponse, m'litali mwake ndi m'mimba mwake munali chimodzimodzi. Mngelo uja adayesa chozungulira mzindawo ndi ndodo yake ija, napeza kuti kutalika kwake kunali makilomita 2,200. M'litali mwake, m'mimba mwake ndi msinkhu wake, zonse zinali zolingana. Kenaka adayesa linga la mzindawo, napeza kuti msinkhu wake unali mamita 65. Mngeloyo ankayesa ndi muyeso womwe anthu amagwiritsa ntchito. Linga la mzindawo linali la miyala yambee, ndipo mzinda weniweniwo unali wa golide wangwiro, woŵala ngati galasi. Maziko aja omwe linga la mzindawo lidaamangidwapo, adaaŵakongoletsa ndi miyala yamitundumitundu yamtengowapatali. Maziko oyamba anali a mwala wambee; achiŵiri anali a mwala wabuluu ngati thambo; achitatu anali a mwala wotuŵira; achinai anali a mwala wobiriŵira; Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake. achisanu anali a mwala mwina mofiira mwina mwabrauni; achisanu ndi chimodzi anali a mwala wofiira; achisanu ndi chiŵiri anali a mwala wachikasu; achisanu ndi chitatu anali a mwala wobiriŵira modera; achisanu ndi chinai anali a mwala wakadzira; achikhumi anali a mwala wachisipu; achikhumi ndi chimodzi anali a mwala wabuluu ngati changululu; achikhumi ndi chiŵiri anali a mwala wofiirira. Zitseko za pa zipata khumi ndi ziŵiri zija zinali za miyala yamtengowapatali kwambiri. Chitseko chilichonse chinali cha mwala umodzi wa mtundu womwewo. Ndipo mseu wamumzindamo unali wa golide wangwiro, woonekera mpaka pansi, ngati galasi. Sindidaonenso Nyumba ya Mulungu mumzindamo, pakuti Nyumba yake ndi Ambuye Mulungu, Mphambe, mwini wake, ndiponso Mwanawankhosa uja. Palibe chifukwa choti dzuŵa kapena mwezi ziziŵala pamzindapo, pakuti ulemerero wa Mulungu ndiwo umaŵalapo, ndipo nyale yake ndi Mwanawankhosa uja. Anthu a mitundu yonse adzayenda m'kuŵala kwake kwa mzindawo, ndipo mafumu a pa dziko lonse lapansi adzabwera ndi ulemerero wao m'menemo. Zitseko za pa zipata zake zidzakhala zosatseka tsiku lonse, chifukwa kumeneko kudzakhala kulibe usiku. Ndipo m'menemo adzabwera ndi ulemerero wa anthu a mitundu yonse, pamodzi ndi chuma chao. Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo. Ndidamva mau amphamvu ochokera ku mpando wachifumu uja. Mauwo adati, “Tsopano malo okhalamo Mulungu ali pakati pa anthu. Iye adzakhala nawo pamodzi, ndipo iwo adzakhala anthu akeake. Mulungu mwini adzakhala nawo, ndipo adzakhala Mulungu wao. Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”
Yesu akuti, “Mvetsetsani, ndikubwera posachedwa. Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense molingana ndi zimene adachita.
Amene akufotokoza zimenezi akuti, “Indedi, ndikubwera posachedwa.” Inde, bwerani, Ambuye Yesu.