Mu Baibulo, nkhani ya chilango imabwerezedwa nthawi zambiri, ndipo imatilimbikitsa kuganizira za chilungamo cha Mulungu ndi mmene Iye amalangirira ana ake.
M’malembo onse oyera, tikuona kuti Mulungu amalanga anthu amene asiya kumvera mawu ake ndipo amatsata zolakwa zawo ndi zokondweretsa zawo. Komabe, ziphaso zimenezi sitiyenera kuziona ngati kubwezera kapena nkhanza, koma monga chiwonetsero cha chikondi ndi chilungamo cha Mulungu.
Mu Chipangano Chakale, tiona mmene Mulungu analangira anthu ake pamene anasiya malamulo ake n’kulambira milungu ina. Izi sizinachitike kuti awononge, koma kuti awalangire ndi kuwaphunzitsa maphunziro ofunika. Monga mombere amawongolera ana ake kuti awakonze ndi kuwatsogolera panjira yoyenera, Mulungu amatilangiranso mwachikondi.
Mu Chipangano Chatatsopano, tikupeza nkhani ya mwana wolowerera, pamene Yesu akutiwonetsa mmene chilango cha Mulungu chimatibwezeretsera. Ngakhale mwana wolowererayu anasiya bambo ake n’kuwononga chuma chake monse mopanda nzeru, pamene anabwerera mwachisoni, analandiridwa ndi manja awiri. Chilango, pankhaniyi, sichinali chakuti chiwononge mwanayo, koma kuti chim’bweretse ku kulapa ndi kukonzanso ubwenzi wake ndi bambo ake.
Choncho, chilango sitiyenera kuchiona ngati chinthu choipa chokha, koma monga mwayi wokulira, kuphunzira, ndi kubwererana ndi Mulungu. Chimatilimbikitsa kuganizira za zochita zathu ndi kudzifufuza ngati tikukhala moyo wathu mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Ngati tilakwitsa ndipo talangidwa, tingadalire chifundo ndi chikhululukiro cha Mulungu.
Chauta akuti, “Ndidzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha kuipa kwao, ndidzalanga oipa chifukwa cha kuchimwa kwao. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
Pamenepo iwowo adzachoka kumapita ku chilango chosatha, olungama aja nkumapita ku moyo wosatha.”
Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.
Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda, amakwapula mwana aliyense amene Iwo amamlandira.”
Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.
Inu Chauta, ngwodala munthu amene mumamlangiza, amene mumamphunzitsa ndi malamulo anu.
Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.
Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti samkonda, koma amene amakonda mwana wake, sazengereza kumlanga.
“Munthu akachimwa pochita mosadziŵa zimene Chauta amaletsa, ndi wopalamulabe ndithu ameneyo, ndipo ndi woyenera kumlanga.
Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.”
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni.
Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.
Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.
Kupusa kumakhala mumtima mwa mwana, koma ndodo yomlangira mwanayo idzachotsa kupusako.
“Ndi wodala munthu amene Mulungu amamdzudzula. Nchifukwa chake usamanyoze chilango cha Mphambe.
Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Akamadzandichimwira, ndizidzamulanga monga m'mene bambo amalangira ana ake.
“Usatchule pachabe dzina la Chauta, Mulungu wako, chifukwa Chauta adzamlanga aliyense wotchula pachabe dzina lakelo.
“ndidzaŵalanga ndi ndodo, chifukwa cha zolakwa zao, ndidzaŵakwapula ndi zikoti chifukwa cha machimo ao. Koma Davide sindidzamchotsera chikondi changa chosasinthika, sindidzakhala wosakhulupirika kwa iye.
Dziŵani kuti Chauta, Mulungu wanu, amakulangani monga momwe bambo amalangira ana ake.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.
uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.
Chauta adalola kuti mumve mau ake kuchokera kumwamba, kuti pakutero akuphunzitseni. Pa dziko lapansi pano Chauta adakuwonetsani moto waukulu, ndipo mudamva akulankhula nanu kuchokera m'motomo.
Mukapanda kundimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanunkaŵiri chifukwa cha machimo anu. Ndidzaononga nyonga zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale youma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuŵa.
“Mwina Mulungu amalanganso munthu ndi matenda kuti akonzeke, nthaŵiyo thupi lake lonse limangophwanya.
Inu Chauta, ngwodala munthu amene mumamlangiza, amene mumamphunzitsa ndi malamulo anu. Mumampumitsa pa nthaŵi yamavuto, mpaka woipa ataloŵa m'dzenje.
Usamaleka kumpatsa mwambo mwana, ukamkwapula ndi tsatsa sadzafa. Ngati umkwapula ndi tsatsa, udzapulumutsa moyo wake ku imfa.
Onse amene ndimaŵakonda, ndimaŵadzudzula ndi kuŵalanga motero. Tsono chitani khama, mutembenuke mtima.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Mkwiyo wa Mulungu ukuwoneka kuchokera Kumwamba. Amakwiyira anthu chifukwa cha kusalungama kwao konse ndi kusamchitira ulemu. Kusalungama kwaoko kumaŵalepheretsa kudziŵa zoona.
Amaonetsa chikondi chake kwa anthu zikwi zambirimbiri, ndipo amaŵakhululukira mphulupulu zao, zoipa zao, ndi machimo ao. Koma sadzalekerera ochimwa, ndipo adzalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha zoipa za atate ao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.”
‘Chauta ndi wosakwiya msanga, ndi wodzaza ndi chifundo chosasinthika, ndi wokhululukira ochimwa ndi opalamula. Koma sadzaleka kulanga ochimwa, amalanga ana a mbadwo wachitatu ndi wachinai chifukwa cha kuchimwa kwa makolo ao.’
Chauta akubwera kuchokera kumene amakhala, akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo ao. Magazi okhetsedwa pa dziko lapansi adzaululuka, mitembo ya anthu ophedwa sidzabisikanso.
Pakamwa pa munthu womvetsa zinthu pamatuluka zanzeru, koma pamsana pa munthu wopanda nzeru sipachoka tsatsa.
Adzalanga anthu onse a pa dziko lapansi ndi moto ndi lupanga. Alipo ambiri amene Chauta adzaŵapha.”
Musadabwe nazo zimenezi, pakuti ikudza nthaŵi pamene anthu onse amene ali m'manda adzamva mau ake nadzatuluka. Anthu amene adachita zabwino, adzauka kuti akhale ndi moyo, koma amene adachita zoipa, adzauka kuti azengedwe mlandu.”
Adzabwera ndi moto woyaka, nadzalanga anthu amene sadziŵa Mulungu, ndi amene sadamvere Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu. Chilango chao nchakuti adzaonongedwa kwamuyaya, sadzaona konse nkhope ya Ambuye kapena ulemerero wa mphamvu zake,
Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena.
Koma ndikunenetsa kuti pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Tiro ndi Sidoni, koposa polanga inu.
Nthaŵi ndiye yafika yoti Mulungu ayambe kuweruza anthu ake. Tsono ngati chiweruzocho chiyambira pa ife, nanga podzafika pa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, ndiye kuti chidzakhala chotani?
Koma Ambuye amatilanga, kuti tiphunzirepo nzeru, kuwopa kuti tingaimbidwe mlandu pamodzi ndi anthu odalira zapansipano.
Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”
Kulipsira nkwanga, kubwezera zoyenerera nkwanganso, nthaŵi yoti agwe idzakwana. Tsiku la masoka ao layandikira, chiwonongeko chao chikudza mofulumira.
“Koma ngati ana ake asiya lamulo langa, ndipo satsata malangizo anga, ngati aphwanya malamulo anga, ndipo sasunga malangizo anga, “ndidzaŵalanga ndi ndodo, chifukwa cha zolakwa zao, ndidzaŵakwapula ndi zikoti chifukwa cha machimo ao.
“Wantchito amene akudziŵa zimene mbuye wake amafuna, koma osakonzekera kuzichita, adzamkwapula kwambiri. Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.”
Ine ndili nanu, ndipo ndidzakupulumutsani,” akuterotu Chauta. “Ndidzaononga mitundu yonse ya anthu kumene ndidakubalalitsani, koma inu sindidzakuwonongani kotheratu. Ndidzakulangani potsata chilungamo, sindingakulekerereni osakulangani konse.”
Munthu wokhulupirira Mwanayo, ali ndi moyo wosatha. Koma wokana kukhulupirira Mwanayo, sadzaona moyo, chifukwa chilango cha Mulungu chili pa iye.”
Motero mbuye wakeyo adapsa mtima kwambiri, nampereka kuti akamzunze mpaka atabweza ngongole yonse ija. “Inunsotu Atate anga akumwamba adzakuchitani zomwezo, aliyense mwa inu akapanda kukhululukira mbale wake ndi mtima wonse.”
Koma maiyo akampweteka, chilango chake chidzakhala chotere: moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi, kutentha ndi moto kulipa kutentha ndi moto, bala kulipa bala, ndipo mkwingwirima kulipa mkwingwirima.
Ngati wolakwayo ayenera kukwapulidwa, muweruziyo amlamule kuti agone pansi ndipo akwapulidwe mikwapulo yolingana ndi kulakwa kwake. Angathe kumkwapula mpaka mikwapulo makumi anai, koma osapitirira pamenepo. Zikapitirira pamenepo, ndiye kuti zidzamchititsa manyazi mbale wanuyo.
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni. Tayani zoipa zanu zonse zakale zimene mudachimwira Ine. Mukhale ndi mtima watsopano ndi nzeru zatsopano. Nanga muferenji, inu anthu a ku Israele? Sindikondwera nayo imfa ya munthu wina aliyense. Nchifukwa chake lapani, kuti mukhale ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
“Ndi wodala munthu amene Mulungu amamdzudzula. Nchifukwa chake usamanyoze chilango cha Mphambe. Pakuti ndiye amene amavulaza namangaponso mabala. Amakantha, komanso manja ake amachiritsa.
Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.
Pakuti Mulungu sadaŵalekerere angelo amene adachimwa aja, koma adaŵaponya m'ng'anjo yamoto, m'maenje amdima momwe ali omangidwa kudikira chiweruzo.
pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga.
Tsopano chimalizo chili pa iwe Israele. Mkwiyo wanga ndidzauthira pa iwe. Ndidzagamula mlandu wako potsata mayendedwe ako, ndipo ndidzakulanga chifukwa cha zonyansa zako. Sindidzakumvera chifundo kapena kukuleka. Ndidzakulanga chifukwa cha machitidwe ako ndiponso chifukwa cha zonyansa zimene zili pakati pako. Pamenepo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
Munthu wina aliyense wamoyo angadandaulirenji pamene alangidwa chifukwa cha machimo ake?
“Ndidaŵakwiyira chifukwa anali okonda chuma dziŵi. Tsono ndidaŵalanga, ndi kuŵafulatira mokwiya. Koma iwowo adakhalabe ouma mitu, ndipo adapitirira kuchita ntchito zao zoipa. “Ndidaona m'mene ankachitira, komabe ndidzaŵachiritsa. Ndidzaŵatsogolera ndi kuŵatonthoza. Anthu olira nao adzandiyamika ndi milomo yao.
Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa: Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu.
“Koma mukapanda kundimvera ndi kutsata malamulo anga onseŵa, mukamanyoza malamulo anga, ndipo mtima wanu ukamadana ndi zimene ndikulamulani, mpaka kusamvera malamulo anga onse ndi kuswa chipangano changa, ndidzakuchitani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi, chifuwa chachikulu choondetsa ndiponso malungo oononga maso ndi ofooketsa moyo. Mudzabzala mbeu zanu, koma osakololapo kanthu, chifukwa choti adani anu adzazidya.
Anthu akunena kuti, “Tiyeni, tibwerere kwa Chauta. Watikadzula, komabe adzatichiritsa. Watikantha, komabe adzamanga mabala athu.
“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
Oweruza akamachedwetsa chilango cha anthu opalamula, anthu ena amalimba mtima nkumafuna kuti ayambe kuchita zoipa nawonso.
Koma tsoka kwa anthu oipa! Zinthu zidzaŵaipira. Zimene akhala akuchitira anzao zomwezo zidzaŵabwerera.
Zakonzeka kale kuti mlandu uŵagwere anthu onyoza, mkwapulo ndi wokonzakonza kuti akwapulire pamsana pa zitsiru.
Anthu amene adachita zabwino, adzauka kuti akhale ndi moyo, koma amene adachita zoipa, adzauka kuti azengedwe mlandu.”
Chauta akuti, “Ndiye ndingapande kuŵalanga chifukwa cha zimenezi? Monga ndisaulipsire mtundu wochita zotere?”
Mikwingwirima ndiye mankhwala ochotsa zoipa. Mikwapulo imachiza zam'katikati mwa munthu.
Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa.
Ndidaonanso anthu akufa, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja, ndipo mabuku adafutukulidwa. Adafutukula buku linanso, limene lili buku la amoyo. Tsono anthu akufawo adaweruzidwa poyang'anira ntchito zao monga momwe zidaalembedwera m'mabukumo. Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake.
Abwenzi anu onse akuiŵalani, sakulabadiraninso. Ndakulangani mwankhanza, poti mlandu wanu ndi waukulu, machimo anu ndi ambiri.
Iye adaŵapsinja ndi ntchito yakalavulagaga, motero iwo adagwa pansi, popanda mmodzi woŵathandiza.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Koma chifukwa ndiwe wa mtima wokanika ndi wosafuna kutembenuka, ukudzisungira chilango cha Mulungu. Chilangocho chidzakugwera pa tsiku limene adzaonetse mkwiyo wake ndiponso kuweruza kwake kolungama.
Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu. Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika. Musandipirikitse pamaso panu, musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera. Pamenepo ochimwa ndidzaŵaphunzitsa njira zanu, ndipo iwo adzabwerera kwa Inu. Mundikhululukire mlandu wanga wokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu Mpulumutsi wanga, ndipo ndidzakweza mau poimba za chipulumutso chanu. Ambuye, tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu. Si nsembe wamba imene Inu imakusangalatsani. Ndikadapereka nsembe yopsereza, sibwenzi Inu mutakondwera nayo. Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza. Muŵachitire zabwino anthu a ku Ziyoni, chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Mumangenso kachiŵiri makoma a Yerusalemu. Pamenepo mudzakondwera ndi nsembe zoyenera, nsembe zootcha ndi zopsereza kwathunthu. Choncho adzapereka ng'ombe zamphongo pa guwa lanu lansembe. Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga, mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.
Zoonadi, tsiku la Chauta likudza, tsiku lopanda chisoni, laukali ndi lamkwiyo. Chauta akubwera kuti asandutse dziko lapansi chipululu ndi kuwononga anthu ochimwa am'menemo.
Koma ndidavomera tchimo langa kwa Inu, sindidabise kuipa kwanga. Ndidati, “Ndidzaulula machimo anga kwa Chauta,” pomwepo Inu mudakhululukiradi mlandu wa machimo anga.
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku likubwera pamene anthu onse odzikuza ndi ochita zoipa adzapsa ngati chiputu m'ng'anjo. Tsiku limenelo adzapserereratu osatsalako muzu kapena nthambi. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
Chauta adzalanga adani a anthu ake molingana ndi zochita zao: adzaonetsa ukali kwa omuukira, ndipo adzalipsira adani ake. Adzalanga ngakhale okhala m'maiko akutali.
munthuyo mumpereke kwa Satana, kuti thupi lake liwonongedwe, ndipo pakutero mzimu wake udzapulumutsidwe pa tsiku la Ambuye.
Moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa mwana ndi wanga, wa bambo ndi wanganso. Munthu amene wachimwa, ndiye amene adzafe.
Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula.
Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa.
Pa zimenezi munthu asachimwire mbale wake kapena kumpezera. Monga tidakuuzani kale monenetsa, Ambuye adzalanga anthu onse ochita zotere.
Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”
Chauta akuti, “Chifukwa anthuwo adandichimwira, ndidzaŵasautsa koopsa, kotero kuti azidzayenda ngati akhungu. Magazi ao adzachita kuti mwaa ngati fumbi, matupi adzangoti vuu, nkumaola ngati ndoŵe. Ngakhale siliva wao kapena golide wao sadzatha kuŵaombola, tsiku la mkwiyo wa Chautalo. Ukali wake wotentha ngati moto, udzapsereza dziko lonse, ndipo mwadzidzidzi adzathetsa onse okhala m'menemo.”
Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
Usagwadire fano lililonse kapena kulipembedza, chifukwa Ine, Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, sindilola kuti wina apikisane nane. Ndimalanga amene adana nane. Ndimalanganso zidzukulu zao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.
“Pajatu Chauta adzabwera ndi moto. Ndipo magaleta ake adzafika ngati mkuntho. Iye adzaonetsa poyera ukali wake, ndipo adzalanga adani ake ndi malaŵi a moto. Adzalanga anthu onse a pa dziko lapansi ndi moto ndi lupanga. Alipo ambiri amene Chauta adzaŵapha.”
Onani mphepo yamkuntho yochokera kwa Chauta! Onani ukali wake woomba ngati namondwe, udzaomba pa mitu ya anthu oipa.
Muzimvera mau onse a malamulo aŵa a m'buku muno, ndipo dzina ili lodabwitsa ndi lochititsa mantha la Chauta, Mulungu wanu, muzilitamanda. Mukapanda kutero, inuyo ndi zidzukulu zanu, Chauta adzakugwetserani masautso apadera, mavuto aakulu okhalitsa ndiponso nthenda zoopsa zosamva mankhwala.
Kudzikuza kwa anthu kudzatha, kudzitama kwa anthu kudzaonongedwa. Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo. Chauta Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku, pamene adzatsitsa onse onyada ndi odzitama, ndipo adzagonjetsa onse amphamvu.
nayenso adzamwako vinyo wa ukali wa Mulungu. Vinyo wake adzathiridwa, popanda kanthu kochepetsa mphamvu yake, m'chikho cha mkwiyo wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto ndi miyala yasulufure yoyaka. Zimenezi zidzachitikira pamaso pa angelo a Mulungu, ndi Mwanawankhosa uja. Utsi wa moto woŵazunzawo umakwera kumwamba mpaka muyaya. Anthu amene adapembedza chilombo chija ndi fano lake, ndiponso amene adalembedwa chizindikiro cha dzina lake chija, sapeza mpumulo usana kapena usiku.
Chauta akunena kuti, “Iwe Yakobe, mtumiki wanga, usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe. Ndidzaonongeratu mitundu yonse ya anthu a kumaiko kumene ndidakupirikitsira. Koma iweyo sindidzakuwononga kotheratu ai. Kulanga ndidzakulanga monga m'mene kuyenera, sindingakulekelere osakulanga konse.”
Iye adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. Anthu amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pakuchita ntchito zabwino molimbikira, Mulungu adzaŵapatsa moyo wosatha. Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira.
Paja tikumdziŵa kale amene adati, “Kulipsira nkwanga, ndidzakhaulitsa ndine.” Adatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” Kugwa m'manja mwa Mulungu wamoyo ndi chinthu choopsa.
Paja Mulungu mwa chilungamo chake, adzaŵalanga ndi masautso anthu amene amakusautsani inu. Koma inu amene mukusauka tsopano, adzakupatsani mpumulo pamodzi ndi ife tomwe. Adzachita zimenezi, Ambuye Yesu akadzabwera kuchokera Kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu.
Koma amphaŵi adzaŵaweruza mwachilungamo, ndipo anthu otsika a pa dziko lapansi adzaŵagamulira mlandu wao mosakondera. Mau ochokera m'kamwa mwake adzakhala ngati ndodo yokanthira ochimwa, atalamula iyeyo anthu oipa adzaphedwa.
Chauta ndi Mulungu wansanje ndiponso wolipsira. Chauta amalanga, ndipo ndi wamkali. Chauta amalipsira amaliwongo ake amakwiyira adani ake. Chauta ndi wamphamvu zedi. Ndi wosakwiya msanga, komabe sadzalola kuti munthu wochimwa akhale wosalangidwa. Pamene amayenda pamachitika kamvulumvulu ndi mphepo yamkuntho, mitambo ndiye fumbi limene mapazi ake amachititsa.
Ndidzaŵalipsira koopsa ndi kuŵalanga mwaukali kwambiri. Ndikadzaŵalanga choncho, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”