Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Pakutha pa chaka mumapereka zokolola zambiri mwa ubwino wanu, kulikonse kumene Inu mupita, kumapezeka dzinthu dzambiri.
Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.
Aliyense abwere ndi chachikhumi chathunthu ku Nyumba yanga, kuti m'menemo mukhale chakudya chambiri. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Mundiyese tsono, ndipo muwone ngati sinditsekula zipata zakumwamba ndi kukugwetserani madalitso ochuluka.
Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.
Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo inu mukhale olemera.
Mumaŵadyetsa zonona m'nyumba mwanu, ndipo mumaŵamwetsa madzi a mu mtsinje wa madalitso anu.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”
Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.
Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense.
Wina amatha kupatsako anzake zinthu mwaufulu, komabe amanka nalemereralemerera. Wina nkukhala wakaligwiritsa, nakhalabe wosauka. Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.
Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Inu mudalola kuti adani atikwere pa mutu, tidaloŵa m'moto ndiponso m'madzi, komabe Inu mwatifikitsa ku malo opulumukirako.
Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.
Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Ufa umene uli m'mbiyawo sudzatha, mafutanso amene ali m'nsupawo sadzatha, mpaka tsiku limene Chauta adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ” Tsono maiyo adapita, nakachitadi monga momwe adaanenera Eliya. Maiyo ndi Eliya ndiponso onse a pa banja la maiyo adadya ufawo masiku ambiri. Ufa umene unali m'mbiyamo sudathe, mafuta amene anali m'nsupawo sadathenso, monga momwe Chauta adaalankhulira kudzera mwa Eliya.
Adayenda pamaso pa Mose nanena mokweza kuti, “Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndiponso wokhulupirika kwa anthu ake.
Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo.
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
Popeza kuti mudalandira manyazi, manyozo ndi zotukwana moŵirikiza, tsopano mudzalandira chigawo cha dziko lanu moŵirikizanso. Chimwemwe chanu chidzakhala chamuyaya.”
Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero.
Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”
Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.
Akuti: Unditame mopemba, ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziŵa.
Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale.
Mwina Mulungu amamlemeretsa munthu pakumpatsa chuma ndi zabwino zina, namlola kuti akondwerere zonsezo. Munthuyo azilandire zimenezo ndi kumakondwerera ntchito zake zonse zolemetsa. Imeneyi ndi mphatso yochokeradi kwa Mulungu.
Abramu anali wolemera kwambiri. Anali ndi zoŵeta monga: nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe, ndiponso siliva ndi golide yemwe.
Mulungu mwa mphamvu zake adatipatsa zonse zotithandiza kukhala ndi moyo ndiponso opembedza, pakutidziŵitsa za Iyeyo amene adatiitana ku ulemerero ndi ubwino wake woposa.
Munthu wokhulupirika adzakhala ndi madalitso ambiri, koma wofunitsitsa kulemera msanga sadzalephera kupeza chilango.
Banja lake lidzakhala lachuma ndi lolemera, ndipo kulungama kwake kudzakhala kwamuyaya.
Chauta akunena kuti, “Inu nonse omva ludzu, bwerani, madzi ali pano. Ndipo inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule chakudya, kuti mudye. Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka, osalipira ndalama, osalipira chilichonse. “Mvula ndi chisanu chambee zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko, koma zimathirira nthaka. Zimameretsa ndi kukulitsa zomera, kenaka nkupatsa alimi mbeu ndi chakudya. Ndimonso amachitira mau ochokera m'kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidaŵatumira zidzayenda bwino. “Inu anthu anga, mudzachoka ku Babiloni mokondwa, adzakutulutsani mumzindamo mwamtendere. Inu mukufika, mapiri ndi magomo adzakuimbirani nyimbo. Nayonso mitengo yonse yam'thengo idzakuwomberani m'manja. Kumene tsopano kuli mitengo yaminga kudzamera mitengo ya paini. Kumene tsopano kuli mkandankhuku kudzamera michisu. Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Ine Chauta, ngati chizindikiro chamuyaya chimene sichidzafafanizika konse.” Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona.
Nkhanitu ndi iyi: wobzala pang'ono, adzakololanso pang'ono, wobzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.
“Ndidzadalitsa kwambiri mzinda wa Ziyoni poupatsa zosoŵa zake, anthu ake osauka, ndidzaŵapatsa chakudya chokwanira.
Ndidzakupatsa chuma chosaoneka poyera ndi katundu wa m'malo obisika. Motero udzadziŵa kuti ndine Chauta, Mulungu wa Israele, amene ndikukuitana pokutchula dzina.
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
Abrahamu adaŵatcha malowo kuti Chauta adapatsa. Ndipo mpaka lero lino anthu amati, “Paphiri la Chauta adzapatsa.”
Motero aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ameneyo adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka adzalandira moyo wosatha.
Atatsiriza kulankhula, adauza Simoni kuti, “Sunthirani kozamako, muponye makoka anu kuti muphe nsomba.” Simoni adati, “Aphunzitsi, usiku wonsewu takhalira kugwira ntchito, osapha kanthu, koma chifukwa Inuyo mwatero, chabwino ndiponya makoka.” Tsono iwo adaponyadi makoka, napha nsomba zambirimbiri, kotero kuti makokawo ankayamba kung'ambika.
Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse.
Koma Mulungu adzatitumizira mzimu wake, kuchokera kumwamba, ndipo dziko lachipululu lidzasanduka lachonde, minda yonse idzabereka dzinthu dzambiri.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Udzaona zimenezi, ndipo udzakondwa, mtima wako udzalumpha ndi chimwemwe. Chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe. Chuma cha maiko onse chidzabwera kwa iwe.
Mbiyazo zitadzaza zonse, maiyo adauza mwana wake kuti, “Bwera ndi inanso mbiya.” Koma mwanayo adauza mai wake kuti, “Palibenso ina.” Pomwepo mafuta aja adaleka kutuluka m'kambiya kaja. Tsono mai uja adapita kukafotokozera Elisa, munthu wa Mulungu uja. Ndipo Elisayo adauza maiyo kuti, “Mai, pitani mukagulitse mafutawo, ndipo mukabweze ngongole zanuzo. Tsono ndalama zotsala zikhale zothandizira inu ndi ana anu.”
Nthaka yabereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu watidalitsa. Inde, Mulungu watidalitsa, anthu onse a ku mathero a dziko lapansi apembedze Iye.
Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Pambuyo pake ophunzira aja adatola zotsala nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri.
Panalibe munthu wosoŵa kanthu pakati pao, chifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankazigulitsa, namabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi. Ndipo ndalamazo ankagaŵira munthu aliyense malinga ndi kusoŵa kwake.
Chauta adzakupezetsani bwino pa zochita zanu zonse. Mudzakhala ndi ana ambiri, zoŵeta zambiri, ndipo minda yanu idzakubalirani zokolola zambiri. Adzakondwera nanu kuti mwakhoza chotere, monga momwe adakondwera ndi makolo anu pamene anali okhoza.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Chauta salola kuti munthu womukondweretsa iye, azikhala ndi njala, koma zimene woipa amazilakalaka, Mulungu amam'mana.
Ndiye amene amakupatsa zabwino nthaŵi zonse za moyo wako, choncho umakhalabe wa mphamvu zatsopano ngati mphungu.
Ndidzakhazika anthu anga kufupi ndi phiri langa, ndipo ndidzaŵagwetsera mvula pa nthaŵi yake, mvula yake ya madalitso.
Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.
Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani.
Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha. Nyama zakuthengo zidzandilemekeza, nkhandwe ndi nthiŵatiŵa zidzanditamanda, chifukwa ndidzayendetsa madzi m'chipululu ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma, kuti ndiŵapatse madzi anthu anga osankhidwa.
Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe.
Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.
Kuwonjezera pamenepo, ndikukupatsanso zimene sudapemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti palibe mfumu imene idzalingane nawe pa masiku onse a moyo wako.
Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.
Tsono atayesa ndi muyeso wa malita aŵiri, adaona kuti amene adaatola tambiri, sitidaŵatsalireko, amene adaatola pang'ono, sitidaŵathere. Aliyense adangotola tokwanira.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira, imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota.
Ndili nacho chuma, ndili nawo ulemu, chuma chosatha ndiponso kukhuphuka konkirankira. Zimene mumalandira kwa ine nzokoma kuposa golide, ngakhale golide wosalala. Phindu lochokera mwa ine nloposa siliva wabwino zedi. Nzeru imakhala pa zitunda m'mbali mwa njira, imakaima pa mphambano za miseu. Ndimachita zomwe zili zoyenera, sindipatuka kuchoka m'njira za chilungamo. Ndimaŵapatsa chuma anthu ondikonda, ndi kudzaza nyumba zao zosungiramo chuma.
“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.
“Inu nkhosa zanga, ngakhale muli oŵerengeka, musaope, pakuti kudakomera Atate anu kuti akupatseni Ufumu wake.
Poti inu muli ndi zambiri tsopano, muyenera kumathandiza osoŵa, kuti m'tsogolomo nawonso akadzakhala ndi zochuluka, azidzakuthandizani pa zosoŵa zanu. Motero padzakhala kulingana. Paja Malembo akuti, “Amene adapata zambiri, sizidamchulukire, amene adapata pang'ono, sizidamchepere.”
Chauta wasankhula Ziyoni, akufuna kuti akhale malo ake okhalamo. Akuti, “Ameneŵa ndiwo malo anga opumuliramo mpaka muyaya. Ndidzakhala kuno chifukwa ndakufunitsitsa. “Ndidzadalitsa kwambiri mzinda wa Ziyoni poupatsa zosoŵa zake, anthu ake osauka, ndidzaŵapatsa chakudya chokwanira.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Kukhala wosauka ndimakudziŵa, kukhala wolemera ndimakudziŵanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoŵeratu. Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.
Inu Chauta, dziko lapansi nlodzaza ndi chikondi chanu chosasinthika, phunzitseni malamulo anu.
Tsono makwangwala ankadzampatsa buledi ndi nyama m'maŵa ndi madzulo. Ndipo ankamwa madzi kumtsinjeko.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
Wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ngwokhulupirikanso pa zazikulu. Ndipo wonyenga pa zazing'ono, amanyenganso pa zazikulu. Tsono ngati mwakhala osakhulupirika pa chuma chonyengachi, ndani nanga adzakusungizeni chuma chenicheni? Ndipo ngati mwakhala osakhulupirika ndi za wina, ndani adzakupatseni zimene zili zanuzanu?
Adapulumutsa anthu ake. Adakhazikitsa chipangano chake kuti chikhale chamuyaya. Dzina lake ndi loyera ndi loopsa.
Munthu wochita chilungamo amakhala ndi chuma chambiri, koma zimene woipa amapindula zimamgwetsa m'mavuto.
Pakuti mwa ife tokha mulibe kanthu kamene kangatiganizitse kuti tingathe kuchita ntchitoyi patokha. Amene amatipatsa mphamvu ndi Mulungu kuti tithe kuichita.
Yesu adaŵafunsa kuti, “Nthaŵi ina ndidaakutumani opanda thumba la ndalama, kapena thumba lapaulendo, kapenanso nsapato. Kodi pamene paja mudaasoŵapo kanthu?” Iwo adati, “Iyai.”
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Yabezi adatama Mulungu wa Israele mopemba kuti, “Mundidalitse ine, ndipo dziko langa mulikuze. Dzanja lanu lamphamvu likhale nane, ndipo mundisunge ine, kuti choipa chisandigwere ndi kumandisautsa.” Motero Mulungu adampatsadi zimene adaapemphazo.
Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”
Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.
Amadzetsa mtendere m'malire a dziko lako, amakudyetsa pokupatsa ufa wa tirigu wosalala.
Koma Mulungu ndi wachifundo chachikulukulu, adatikonda ndi chikondi chachikulu kopambana. Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani.
Pambuyo pake Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti agaŵire anthuwo. Anthu onse aja adadya nakhuta. Ndipo ophunzira aja adatola zotsala, nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri.
Chauta amapha ludzu la munthu womva ludzu, amamudyetsa zinthu zabwino munthu womva njala.
Adzakulemeretsani pa zonse, kuti mukhale oolowa manja ndithu, kotero kuti ambiri adzathokoza Mulungu chifukwa cha mphatso yanu imene tiŵatengereko.
Adafesa mbeu m'minda, namaoka mipesa, ndipo adakolola dzinthu dzambiri. Chifukwa cha madalitso a Chauta, anthuwo adachuluka kwambiri, Chauta sadalole kuti zoŵeta za anthuwo zichepe.
Adasonkhanitsa tirigu wochuluka ngati mchenga wakunyanja. Kunali tirigu wochuluka kotero kuti adaaleka nkumuyesa komwe, popeza kuti kunali kosatheka kumuyesa tirigu yenseyo.
Anthu a m'mipingoyo adayesedwa kwambiri ndi masautso, komabe adakondwa kwakukulu, kotero kuti adapereka moolowa manja kwenikweni, ngakhale anali amphaŵi.
Tsiku lathunthu anthu oipa amasirira zinthu, koma omvera Mulungu amapatsa ndipo alibe kaliwumira.
Tsono Inu mumadalitsa dziko lapansi ndi kulithirira, ndipo mumalilemeza kwambiri. Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi, Inu mumaŵapatsa anthu dzinthu, pakuti ndimo m'mene mwalikonzera dzikolo.
Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.”
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Mwa Khristu Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba.
Chauta adzakudalitsani inu monga momwe adalonjezera. Mudzakongoza mitundu yambiri, koma inuyo simudzakongola kwa wina aliyense. Mudzalamulira mitundu yambiri, koma palibe mtundu wina uliwonse umene udzakulamulireni inu.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Pajatu amene ali nkanthu kale, adzampatsanso zina, nadzakhala ndi zochuluka. Koma amene alibe kanthu, adzamlanda ngakhale kakang'onong'ono kamene ali nako.
Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu. Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.
Mukamadzabzala mbeu zanu, Chauta adzakugwetserani mvula kuti zimere, ndipo mudzakolola zambiri. Tsiku limenelo ng'ombe zanu zidzapeza mabusa aakulu.
Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona. Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta, mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.
“Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.”
Chauta adzadalitsa mizinda yanu ndi minda yanu. Mudzafunsira mbeta mtsikana, koma ndi wina amene adzakwatirane naye. Kumanga nyumba mudzamanga ndithu, koma simudzagonamo. Munda wamphesa mudzabzala, koma mphesa zake simudzadyako. Ng'ombe zanu azidzakupherani mukupenya, koma nyama yake simudzadyako. Abulu anu azikaŵalanda mwamphamvu ndi kupita nawo kwina, inu mukupenya, ndipo sadzakubwezerani. Nkhosa zanu adzazipereka kwa adani anu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuthandizeni. Ana anu aamuna ndi aakazi adzatengedwa ukapolo ndi alendo, inu mukupenya. Tsiku ndi tsiku maso anu adzakhala ali psuu kuyang'anira ngati ana anuwo abwere, koma simudzaphulapo kanthu. Mtundu wachilendo udzakulandani zakumunda zanu zonse zimene mudathyoka nazo msana polima, ndipo mudzapsinjidwa ndi kuzunzika mosalekeza. Zimene mudzaziwona ndi maso zidzakupengetsani. Chauta adzabweretsa zilonda zoŵaŵa ndi zosachizika pa maondo ndi pamisongolo panu, ndipo anamkalimbwi azidzakutulukani thupi lonse, kuyambira kuphazi mpaka kumutu. Chauta adzaipirikitsira ku dziko lachilendo mfumu yanu, pamodzi ndi inu nomwe, kumene inuyo ndi makolo anu simudakhaleko nkale lonse. Kumeneko muzikatumikira milungu ina yopanga ndi mitengo ndi miyala. Ku mitundu yonse kumene Chauta adzakumwazireniko, anthu adzadabwa nanu, adzakusekani, adzakupekani nthano yokunyodolani. Mudzabzala zambiri, koma mudzakolola pang'ono chabe, chifukwa dzombe lidzadya zolima zanuzo. Minda yamphesa mudzalimadi, mpaka kuisamala bwino, koma mphesa zake simudzathyola kapena kumwako vinyo wake, chifukwa tizilombo ndito tidzadye mphesazo. Chauta adzadalitsa ana anu ndi zokolola zanu, ndi ana a zoŵeta zanu, ndipo adzakupatsani ng'ombe ndi zoŵeta zina zambiri. Mitengo ya olivi izidzamera paliponse m'dziko mwanumo, koma mafuta a olivi simudzakhala nawo, chifukwa zipatso za olivizo zidzayoyoka. Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi ndithu, koma sadzakhala anu, chifukwa adzatengedwa ukapolo. Mitengo yanu yonse ndi dzinthu dzanu dzam'munda zidzatha ndi tizilombo. Alendo okhala m'dziko mwanu ndiwo amene azidzakwererakwerera, koma inu muzidzatsikiratsikira. Iwowo azidzakukongozani ndalama, koma inu simudzakhala nazo ndi pang'ono pomwe zoŵakongoza, ndipo potsiriza adzakulamulirani. Masoka onseŵa adzakugwerani. Adzakhala pa inu mpaka mutaonongeka, chifukwa choti simudamvere Chauta, Mulungu wanu, ndipo simudatsate malamulo ndi malangizo onse amene Iye adakupatsani. Masoka onseŵa adzakhala mboni yapadera ya chilango cha Mulungu pa inu ndi pa zidzukulu zanu mpaka muyaya. Paja Chauta adakudalitsani pa zonse, komabe inu simudamtumikire mokondwa ndi mitima yachimwemwe. Motero mudzatumikira adani odzalimbana nanu amene Chauta adzakutumizireni. Mudzamva njala ndi ludzu. Zinthu zonse zidzakusoŵani pamodzi ndi zovala zomwe. Chauta adzakuzunzani mwankhanza, mpaka mutaonongeka. Chauta adzaitanitsa mtundu wa anthu ochokera ku malekezero a dziko lapansi, kuti adzamenyane nanu. Anthu a mtundu umenewo amene inu simudziŵa chilankhulo chao, adzakuterani ngati mphungu. Chauta adzadalitsa mbeu zanu ndi chakudya chimene muchikonza kuchokera ku mbeuzo, kuti zichuluke. Anthuwo adzakhala aukali, ndipo sadzachita chifundo ndi aliyense, ngakhale akhale mwana kapena nkhalamba. Adzakudyerani ng'ombe zanu pamodzi ndi zakumunda zanu zomwe, mpaka mudzafa ndi njala. Sadzakusiyiraniko mpang'ono pomwe tirigu, vinyo, mafuta aolivi, ng'ombe kapena nkhosa, ndipo mudzafadi. Adzathira nkhondo mzinda uliwonse, m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo. Ndipo malinga ataliatali amene mukuŵakhulupirirawo adzagwa ponseponse. Adzakuzingani m'mizinda yonse ya m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsanilo. Nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani koopsa, mudzasoŵa chakudya kotheratu, kotero kuti muzidzadya ana anu omwe aamuna ndi aakazi, amene Chauta adakupatsani. Ngakhale munthu amene ali woleredwa bwino ndi wofatsa mtima kwambiri mwa inu, adzamana chakudya mbale wake, mkazi wake wapamtima ndi ana ake omutsalira, mwakuti sadzapatsako ndi mmodzi yemwe nyama ya ana ake amene akuŵadya, chifukwa adzakhala alibiretu chakudya pa nthaŵi imene adani anu azidzakuzingani ndi kukusautsani koopsa. Ngakhale mkazi woleredwa bwino ndi wolobodoka kotero kuti sangayese nkomwe kupondetsa pansi phazi lake, adzamana mwamuna wake wapamtima ndi ana ake onse nyama ya ana ake ongobadwa kumene, pamodzi ndi za matenda ake zomwe zochokera m'mimba mwake, popeza kuti azidzadya zimenezi yekha mobisa, chifukwa cha kusoŵeratu chakudya, nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani kwambiri. Muzimvera mau onse a malamulo aŵa a m'buku muno, ndipo dzina ili lodabwitsa ndi lochititsa mantha la Chauta, Mulungu wanu, muzilitamanda. Mukapanda kutero, inuyo ndi zidzukulu zanu, Chauta adzakugwetserani masautso apadera, mavuto aakulu okhalitsa ndiponso nthenda zoopsa zosamva mankhwala. Chauta adzadalitsa zochita zanu zonse.
Nzoonadi, kupembedza Mulungu kumapindulitsa kwambiri, malinga munthu akakhutira ndi zimene ali nazo. Sitidatenge kanthu poloŵa m'dziko lino lapansi, ndipo sitingathenso kutenga kanthu potulukamo. Tsono ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire.
Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali.
Chauta adamdalitsa kwambiri mbuyanga, ndipo adamkuza kwambiri. Ali ndi nkhosa ndi mbuzi ndi ng'ombe zochuluka. Alinso ndi siliva ndi golide, akapolo aamuna ndi aakazi, ndiponso ngamira ndi abulu ambiri.
Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye, adzatembereredwa kwambiri.
Adati, “M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche, namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche, Chauta ndiye adapatsa, Chauta ndiyenso walanda. Litamandike dzina la Chauta.”
Kenaka Chauta adaŵatulutsa Aisraele atatenga siliva ndi golide, pakati pa mafuko awo panalibe amene adafooka.
Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire?
Uzichita zimene Chauta Mulungu wako akulamula. Uziyenda m'njira za Chauta, uzimvera mau, malangizo ndi malamulo a Mulungu, monga momwe adalembedwera m'malamulo a Mose, kuti zonse zizikuyendera bwino kulikonse kumene ungapite.
Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Muzikondwa mwa Ambuye nthaŵi zonse. Ndikubwerezanso kuti, “Muzikondwa.” Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake! Paja Iye ndi wabwino. Chikondi chake nchamuyaya, kukhulupirika kwake nkosatha.
“Nchifukwa chake musamada nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Tidzadyanji? Tidzamwanji? Tidzavalanji?’ Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu akunja. Atate anu akumwamba amadziŵa kuti mukuzisoŵa zonsezi. Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndakutsekulirani pa khomo, ndipo palibe amene angatsekepo. Ndikudziŵa kuti mphamvu zanu nzochepa, komabe mwasunga mau anga, ndipo simudandikane.