Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, kufunika kwa mawu athu, monga mmene Baibulo limatiuzira. Tikamalankhula mwaulemu komanso m’chikhulupiriro, tidzalandira madalitso ochokera kwa Mulungu. Koma tikalankhula mosakhulupirika komanso ndi kuipa, tidzatsatiridwa ndi matemberero ndi zinthu zoipa.
Mawu athu ali ndi mphamvu yopatsa moyo kapena kubweretsa imfa. Chifukwa chake, chilichonse chimene tichilankhula kuti chikhale dalitso chidzaonekera, ndipo chilichonse chimene tichilankhula kuti chikhale temberero sichikondweretsa Mulungu.
Tiyenera kukhala chitsanzo cha madalitso nthawi zonse, kupewa matemberero ndipo nthawi zonse kufunafuna madalitso pa ife eni. Izi tizitha kuzichita mwa kusinkhasinkha mawu a Mulungu ndikumvetsa ntchito yathu padziko lapansi monga gawo la thupi la Khristu.
Monga ana a kuunika, mawu athu ayenera kuwonetsa maganizo a Atate wathu wakumwamba, kukhala chitsanzo cha mawu oona nthawi zonse. Pakati pa mavuto a dziko lapansi, tibweretse madalitso a Mulungu padziko lapansi, kufesa mtendere, mgwirizano, dongosolo ndi chikondi.
Deuteronomo 28:2 imatiuza kuti madalitso onsewa adzatifikira ngati timvera Ambuye Mulungu wathu.
“Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndidzatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.”
Madalitso kwa inu, mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndikukupatsani leroŵa.
Inu mabanja a Yuda ndi Israele, kale munali chizindikiro cha matemberero pakati pa mitundu ina ya anthu. Koma tsopano ndidzakupulumutsani ndipo mudzakhala chizindikiro cha madalitso. Musaope, limbani mtima.
Tsono Yoswa adaŵerenga mau onse a malamulo momveka bwino, pamodzi ndi madalitso ndiponso matemberero, monga momwe zidalembedwera m'buku la malamulo a Mose.
Pakamwa pomwe pamatuluka mayamiko pomweponso pamatuluka matemberero. Abale anga, zoterezi siziyenera kumachitika.
Ndi lilime lomwelo timayamika Ambuye, amenenso ndi Atate, komanso ndi lilime lomwelo timatemberera anthu anzathu amene Mulungu adaŵalenga ofanafana naye.
Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.”
Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa.
Paja ameneŵa sadapite kukakomana ndi ana a Aisraele, kuti akaŵapatse buledi ndi madzi. M'malo mwake adalemba Balamu kuti aŵatemberere. Komabe Mulungu wathu matembererowo adaŵasandutsa madalitso.”
Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Tsono anthu onse a pa dziko lonse lapansi adzaona kuti Chauta, Mulungu wanu, wakusankhani inu kuti mukhale anthu akeake, ndipo azidzakuwopani. Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani. Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense. Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika. Choncho pa mau ndikukuuzani leroŵa, musapatuke kumanja kapena kumanzere, pakutsata milungu ina ndi kumaitumikira. Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa: Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu. Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu. Chauta adzakutembererani pokupatsani ana oŵerengeka, zokolola zochepa, ndiponso ng'ombe ndi zoŵeta zina pang'ono chabe. Chauta adzatemberera ntchito zanu zonse. Mverani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalandira madalitso onse aŵa:
Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa:
Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo, Tsono inuyo ndi zidzukulu zanu mudzabwerera kwa Chauta, ndipo mau ake amene ndikukupatsani leroŵa mudzaŵamvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. mukonde Chauta, Mulungu wanu, muzimvera mau ake ndi kukhala okhulupirika kwa Iye, kuti inu ndi zidzukulu zanu mudzakhalitsemo m'dziko limene adalonjeza kuti adzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
Anthu amene Chauta adaŵadalitsa, adzalandira dziko kuti likhale lao, koma amene Chauta adaŵatemberera adzaonongeka.
Pamene adzakufikirani madalitso ndi matemberero amene ndatchula aja, mudzaŵakumbukira muli pakati pa mitundu ina kumaiko kumene Chauta, Mulungu wanu, adakumwazirani.
Tikugwira ntchito kolimba ndi manja athu kuti tidzisunge. Anthu akamatichita chipongwe, timapempha kuti Mulungu aŵadalitse. Anthu akamatizunza, timangopirira.
Lero ndikukupatsani zinthu ziŵiri kuti musankhepo, madalitso kapena matemberero. Madalitso kwa inu, mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndikukupatsani leroŵa. Koma matemberero kwa inu, mukapanda kumvera malamulo ameneŵa, nkusiya njira imene ndikukulamulani lero, kuti mutembenukire kwa milungu ina ndi kumaipembedza, milungu imene nkale lonse simudaipembedzepo.
Kenaka Mulungu adauza Adamu kuti, “Iwe unamvera mkazi wako, wadya zipatso zija zimene ndidaakuuza kuti usadye. Nthaka idzatembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi. Udzayenera kugwira ntchito yathukuta nthaŵi ya moyo wako wonse, kuti upeze chakudya chokwanira.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo,
Cholinga chao nchongofuna kumtsitsa pa malo ake aulemu. Amakonda kulankhula zonama. Amadalitsa ndi pakamwa pao, koma mumtima mwao amatemberera.
Bwerani tsono muŵatemberere anthu ameneŵa m'malo mwanga, poti ngamphamvu kopambana ine. Mwina mwake ndidzatha kuŵagonjetsa ndi kuŵapirikitsa m'dziko mwanga. Pakuti ndikudziŵa kuti amene inu mumamdalitsa, amadalitsidwa, ndipo amene mumamtemberera, amatembereredwa.”
Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi, pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.
Munthu aliyense wotemberera bambo wake ndi mai wake ayenera kuphedwa. Munthu ameneyo watemberera bambo wake ndi mai wake, tsono magazi ake akhale pa iyeyo.
Mukapanda kundimvera, mukapanda kulemekeza dzina langa, ndidzakutembererani. Zabwino zimene mumazilandira nazonso ndidzazitemberera. Ndithu, ndazitemberera kale chifukwa simudamvere ndi mtima wonse.
Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.”
Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku. Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.
Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai.
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.” Khristu adachita zimenezi, kuti dalitso limene Mulungu adaalonjeza Abrahamu, lipatsidwe kwa anthu a mitundu yonse kudzera mwa Khristu Yesu, ndipo kuti pakukhulupirira tilandire Mzimu Woyera amene Mulungu adaatilonjeza.
Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake. Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse. Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala. Banja lake lidzakhala lachuma ndi lolemera, ndipo kulungama kwake kudzakhala kwamuyaya.
Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Tsono anthu onse a pa dziko lonse lapansi adzaona kuti Chauta, Mulungu wanu, wakusankhani inu kuti mukhale anthu akeake, ndipo azidzakuwopani. Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani. Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense. Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika. Choncho pa mau ndikukuuzani leroŵa, musapatuke kumanja kapena kumanzere, pakutsata milungu ina ndi kumaitumikira.
Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.
Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.
Adzaŵalanga chifukwa cha machimo ao, adzaŵaononga chifukwa cha kuipa kwao, zoonadi, Chauta, Mulungu wathu, ndiye amene adzaŵafafanize.
Adati, “M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche, namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche, Chauta ndiye adapatsa, Chauta ndiyenso walanda. Litamandike dzina la Chauta.”
Pakamwa pomwe pamatuluka mayamiko pomweponso pamatuluka matemberero. Abale anga, zoterezi siziyenera kumachitika. Kodi kasupe amatulutsa madzi omweka ndi oŵaŵa pa dzenje limodzimodzi? Abale anga, kodi mkuyu ungathe kubala zipatso za olivi, kapena mpesa kubala nkhuyu? Momwemonso kasupe wa madzi amchere sangathe kupereka madzi omweka.
Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.
Ngwodala munthu amene Inu mumamsankha nkubwera naye kudzakhala m'mabwalo anu. Mutikhutitse ndi zinthu zabwino za m'Nyumba yanu, Nyumba yanu yoyera.
Tsono Iyeyo ngati Mfumu adzauza a ku dzanja lamanjawo kuti, ‘Bwerani kuno inu odalitsidwa a Atate anga. Loŵani mu ufumu umene adakukonzerani chilengedwere dziko lapansi.
Chifukwa cha madalitso a Chauta, anthuwo adachuluka kwambiri, Chauta sadalole kuti zoŵeta za anthuwo zichepe.
Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse. Palibe mkazi amene adzapititse padera m'dziko mwanumo, ndipo wosabala sadzaoneka. Ndidzakupatsani moyo wautali.
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”
Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake. Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Isaki adapemphera ana ake, Yakobe ndi Esau, madalitso am'tsogolo.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Madalitso olandira anthu olungama amakweza mzinda, koma pakamwa pa anthu oipa mtima pamapasula mzindawo.
Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa.
aliyense mwa inu pa zokolola zonse zoyamba zimene adazipeza m'dziko limene Chauta akukupatsanilo, atengeko zina ndi kuziika m'dengu, ndipo apite nazo ku malo amene Chauta, Mulungu wanu, adasankhula kuti anthu azidzapembedzerako.
Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.
Chauta ndiye chuma changa ndi choloŵa changa. Tsogolo langa lili m'manja mwanu. Malire a malo anga andikhalira mwabwino. Inde, ndalandira madalitso abwino ndithu.
Motero wopempha madalitso m'dzikomo, adzachita zimenezo kwa Mulungu wolankhula zoona. Ndipo wochita malumbiro m'dzikomo, adzalumbira m'dzina la Mulungu wolankhula zoona, chifukwa choti mavuto akale aiŵalika ndipo achotsedwa pamaso panga.”
“Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.”
Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena. Farao adalamula anthu ake, ndipo iwowo adatulutsa Abramu ndi mkazi wake m'dzikomo, pamodzi ndi zonse zimene anali nazo. “Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndidzatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.”