Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


102 Mau a Mulungu Okhudza Kudzozedwa ndi Mafuta

102 Mau a Mulungu Okhudza Kudzozedwa ndi Mafuta

Lembani izi, Mulungu ndiye amatilimbitsa ife pamodzi ndi inu mwa Khristu, ndipo anatipaka mafuta. Iyenso anatisindikiza, natipatsa Mzimu m’mitima yathu monga chikole. 2 Akorinto 1:21-22

Suli pano padziko lapansi mwangozi. Mulungu waika chinthu chapadera mkati mwako, zomwe zikutanthauza kuti pali cholinga chamuyaya chokhala ndi dzina lako, kuyambira kale lomwe dziko lisanakhaleko. N’chifukwa chake, uzikumbukira nthawi zonse kuti amene anakutcha ndiye amakugwira, amene anakudzoza ndiye amakupatsa mphamvu ndi nzeru zochitira zofuna zake.

Kumbukira nthawi zonse kuti kuyitanidwa komwe Mulungu wakupatsa sikungasinthike. Pali chizindikiro pa iwe chosonyeza kuti ndiwe mwana wa Mulungu, wosankhidwa kuonetsa ulemerero wake ndi mphamvu zake. Chifukwa chake, yenda molimba mtima podziwa kuti suli wekha ndipo Mzimu Woyera amakutsogolera nthawi zonse.

Usawope zomwe anthu angakuchitire. Lankhula zomwe Mulungu wakuuza ndipo chita zonse zomwe akulamula, chifukwa kukhalapo kwake kudzakhala nawe.




Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:14

Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:22-25

Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti, Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu ndi sinamoni wonunkhira wa limodzi la magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi nzimbe zonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu, ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi; ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa machitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 1:9

Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa; mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani ndi mafuta a chikondwerero chenicheni koposa anzanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 29:7

Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pake, ndi kumdzoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 6:13

Ndipo anatulutsa ziwanda zambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala, nawachiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 8:10-12

Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza Kachisi, ndi zonse zili m'mwemo, nazipatula. Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake, kuzipatula. Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:14-15

Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:46

Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:27

Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:30

Ndipo udzoze Aroni ndi ana ake amuna, ndi kuwapatula andichitire ntchito ya nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:15

nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andichitire ntchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 8:12

Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 16:13

Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:5

Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 14:8

Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m'manda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 28:41

Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 1:39

Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali m'Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:9

Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao Kachisi, ndi zonse zili m'mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse; ndipo adzakhala wopatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 2:4

Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda. Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndiwo amene anamuika Saulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:10

Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 19:16

ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi akhale mfumu ya Israele; ukadzozenso Elisa mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola akhale mneneri m'malo mwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 8:30

Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala pa guwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake amuna, ndi pa zovala za ana ake amuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake amuna, ndi zovala za ana ake amuna omwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 133:2

Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:3

Pamenepo Maria m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:17

Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 21:10-12

Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ake, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pake, amene anamdzaza dzanja kuti avale zovalazo, asawinde, kapena kung'amba zovala zake. Asafike kuli mtembo; asadzidetse chifukwa cha atate wake, kapena mai wake. Asatuluke m'malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wake; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wake ali pa iye; Ine ndine Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:20

Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 6:15

ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa, timitanda ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi todzoza ndi mafuta, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 29:21

Ndipo utapeko pamwazi uli pa guwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake amuna, ndi pa zovala za ana ake amuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake amuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:8

ndi mafuta akuunikira, ndi zonunkhira za mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:21-22

Koma Iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Khristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu; amenenso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 10:1

Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 45:7

Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa, chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 31:11

ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha zonunkhira zokoma za malo opatulika; azichita monga mwa zonse ndakuuza iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:26-29

Ndipo udzoze nao chihema chokomanako, ndi likasa la mboni, ndi gomelo ndi zipangizo zake zonse, ndi choikapo nyali ndi zipangizo zake, ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate wosambiramo ndi tsinde lake. Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:6

mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za chofukiza cha fungo lokoma;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:13-15

Nuveke Aroni chovala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatula andichitire Ine ntchito ya nsembe. Ndipo ubwere nao ana ake amuna ndi kuwaveka malaya am'kati; nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andichitire ntchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 29:1-2

Ichi ndicho uwachitire kuwapatula, andichitire ntchito ya nsembe: tenga ng'ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro, Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo Aroni ndi ana ake amuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo. Nuphe ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako. Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng'ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi chala chako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe. Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha pa guwa la nsembe. Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo. Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo. Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza pa guwa la nsembe pozungulira. Ndipo upadzule nkhosa yamphongo m'ziwalo zake, ndi kutsuka matumbo ake, ndi miyendo yake, ndi kuziika pa ziwalo zake, ndi pamutu pake. Pamenepo upsereze nkhosa yamphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova. Ndipo utenge nkhosa yamphongo yinayo; ndi Aroni ndi ana ake amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo. ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 35:25

ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere kumudzi wake wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 9:6

Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pake, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisraele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:15-18

ndipo wansembe atengeko muyeso uja wa mafuta, nawathire pa chikhato cha dzanja lake lamanzere la iye mwini; ndipo wansembe aviike chala chake cha dzanja lake lamanja cha iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lake lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi chala chake pamaso pa Yehova; ndipo wansembe apakeko mafuta okhala m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yopalamula; natsitsitize mafuta otsala m'dzanja lake la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 39:37

choikapo nyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:31-33

Nulankhule ndi ana a Israele, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu. Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ake; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika. Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 19:15-16

Ndipo Yehova anati kwa iye, Bwerera ulendo wako, udzere kuchipululu kunka ku Damasiko, ndipo utafikako udzoze Hazaele akhale mfumu ya Aramu; ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi akhale mfumu ya Israele; ukadzozenso Elisa mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola akhale mneneri m'malo mwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 9:16

Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:28

ndi zonunkhira, ndi mafuta akuunikira, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza za fungo lokoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 2:1

Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo lubani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:24-25

ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi; ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa machitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 4:16

Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa Kachisi opatulika, ndi zipangizo zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 105:15

Ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:7

anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa ya alabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m'mene Iye analikukhala pachakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 7:12

akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 6:17

naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 28:15

Nanyamuka amuna otchulidwa maina, natenga andende, naveka ausiwa onse mwa iwo ndi zofunkhazo, nawapatsa zovala, ndi nsapato, nawadyetsa ndi kuwamwetsa, nawadzoza, nasenza ofooka ao onse pa abulu, nafika nao ku Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kwa abale ao; nabwerera iwo kunka ku Samariya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:6

Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake; adzamvomereza m'Mwamba mwake moyera ndi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 4:14

Pamenepo anati, Awa ndi ana amuna awiri a mafuta oimirira pamaso pa Mbuye wa dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:20

Ndapeza Davide mtumiki wanga; ndamdzoza mafuta anga oyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 10:27

Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wake adzachoka pa phewa lako, ndi goli lake pakhosi pako; ndipo goli lidzathedwa chifukwa cha kudzoza mafuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 141:5

Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 27:20

Ndipo uuze ana a Israele akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 39:38

ndi guwa la nsembe lagolide, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:10-11

Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulika kwambiri. Udzozenso mkhate ndi tsinde lake, ndi kuupatula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:26-29

ndipo wansembe athireko mafuta aja m'chikhato chake chamanzere cha iye mwini; ndipo wansembe awazeko mafuta aja ali m'dzanja lake lamanzere ndi chala chake cha dzanja lamanja, kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova; ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa nsembe yopalamula; ndipo mafuta otsala m'dzanja la wansembe atsitsitize pa mutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumchitira chomtetezera pamaso pa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:16

Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 28:3

Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 8:1-2

Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza Kachisi, ndi zonse zili m'mwemo, nazipatula. Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake, kuzipatula. Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula. Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawaveka malaya a m'kati, nawamanga m'chuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adzauza Mose. Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pa mutu wa ng'ombe ya nsembe yauchimo. Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi chala chake pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde pa guwa la nsembe, nalipatula, kuti alichitire cholitetezera. Ndipo anatenga mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndipo Mose anazitentha pa guwa la nsembe. Koma ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi nyama yake, ndi chipwidza chake, anazitentha ndi moto kunja kwa chigono; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo. Ndipo anaipha; ndi Mose anawaza mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira. Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 1:39-40

Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali m'Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo. Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwa. Ndipo anthu onse anakwera namtsata, naliza zitoliro, nakondwera ndi kukondwera kwakukulu, kotero kuti pansi panang'ambika ndi phokoso lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:12

Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake amuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 28:18

Yakobo ndipo anauka m'mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pa mutu wake, nauimiritsa, nathira mafuta pamtu pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:25-28

ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa machitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika. Ndipo udzoze nao chihema chokomanako, ndi likasa la mboni, ndi gomelo ndi zipangizo zake zonse, ndi choikapo nyali ndi zipangizo zake, ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate wosambiramo ndi tsinde lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:15-16

ndipo wansembe atengeko muyeso uja wa mafuta, nawathire pa chikhato cha dzanja lake lamanzere la iye mwini; ndipo wansembe aviike chala chake cha dzanja lake lamanja cha iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lake lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi chala chake pamaso pa Yehova;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:3-4

Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengeranso mafuta; Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere. Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi: pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine; wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine. Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani? Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani? Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu? koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 37:29

Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosanganiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 39:37-38

choikapo nyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira; ndi guwa la nsembe lagolide, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:29-30

ndipo mafuta otsala m'dzanja la wansembe atsitsitize pa mutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumchitira chomtetezera pamaso pa Yehova. ndipo wansembe atuluke kunka kunja kwa chigono; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nthenda yakhate yapola pa wakhateyo; Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:10

Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:8-9

ndi mafuta akuunikira, ndi zonunkhira za mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma; ndi miyala yasohamu, ndi miyala yoika ya efodi, ndi ya chapachifuwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 7:10

Ndipo nsembe zonse zaufa zosanganiza ndi mafuta, kapena zouma zikhale za ana onse a Aroni, alandireko onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:27-29

ndipo wansembe awazeko mafuta aja ali m'dzanja lake lamanzere ndi chala chake cha dzanja lamanja, kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova; ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa nsembe yopalamula; ndipo mafuta otsala m'dzanja la wansembe atsitsitize pa mutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumchitira chomtetezera pamaso pa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:28

ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa nsembe yopalamula;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:23-24

Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu ndi sinamoni wonunkhira wa limodzi la magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi nzimbe zonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu, ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 18:8

Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israele; chifukwa cha kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna, likhale lemba losatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:10-13

Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta. Ndipo wansembe amene amyeretsayo, amuike munthu uja wakuti ayeretsedwe, ndi zinthu zija, pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako; ndipo wansembe atenge mwanawankhosa mmodzi wamwamuna, nabwere naye akhale nsembe yopalamula, pamodzi ndi muyeso uja wa mafuta, naziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. Ndipo akaphere mwanawankhosa wamwamuna paja amapherapo nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, pa malo popatulika; pakuti monga nsembe yauchimo momwemo nsembe yopalamula nja wansembe; ndiyo yopatulika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 133:1-2

Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi! Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:19-20

Ndipo wansembe apereke nsembe yauchimo, namchitire chomtetezera amene akuti ayeretsedwe, chifukwa cha kudetsedwa kwake; ndipo atatero aphe nsembe yopsereza; Chilamulo cha wakhate tsiku la kumyeretsa kwake ndi ichi: azidza naye kwa wansembe; ndipo wansembe atenthe nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa pa guwa la nsembe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala iye woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:3

ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 18:8-9

Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israele; chifukwa cha kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna, likhale lemba losatha. Izi ndi zako pa zinthu zopatulika kwambiri, zosafika kumoto; zopereka zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zauchimo, ndi nsembe zao zonse zopalamula, zimene andibwezera Ine, zikhale zopatulika kwambiri za iwe ndi za ana ako amuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:10-12

Ndipo abwere yense wa mtima waluso mwa inu, napange zonse zimene Yehova anauza; Kachisi, hema wake, ndi chophimba chake, zokowera zake, ndi matabwa ake, mitanda yake, mizati, nsanamira, ndi nsichi zake, ndi makamwa ao; likasa, ndi mphiko zake, chotetezerapo, ndi nsalu yotchinga yotseka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:6-8

mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za chofukiza cha fungo lokoma; miyala yaberulo, ndi miyala yoika paefodi, ndi pachapachifuwa. Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:34

nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 14:21-24

Ndipo akakhala waumphawi chosafikana chuma chake azitenga mwanawankhosa mmodzi wamwamuna akhale nsembe yopalamula, aiweyule kumchitira chomtetezera, ndi limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndi muyeso umodzi magawo atatu wa mafuta; ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yauchimo, ndi linzake la nsembe yopsereza. Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu abwere nao kwa wansembe, ku khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kuti ayeretsedwe. Ndipo wansembe atenge mwanawankhosa wa nsembe yopalamula, ndi muyeso uja wa mafuta, ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:1-3

Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulika kwambiri. Udzozenso mkhate ndi tsinde lake, ndi kuupatula. Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake amuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi. Nuveke Aroni chovala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatula andichitire Ine ntchito ya nsembe. Ndipo ubwere nao ana ake amuna ndi kuwaveka malaya am'kati; nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andichitire ntchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao. Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita. Ndipo kunali, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa Kachisi, ndipo Mose anautsa Kachisi, nakhazika makamwa ake, naimika matabwa ake, namangapo mitanda yake, nautsa mizati ndi nsanamira zake. Ndipo anayalika hema pamwamba pa Kachisi, naika chophimba cha chihema pamwamba pake; monga Yehova adamuuza Mose. Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse Kachisi wa chihema chokomanako. Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa; nalowa nalo likasa m'Kachisi, napachika nsalu yotchinga, natchinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anaika gomelo m'chihema chokomanako, pa mbali ya kumpoto ya Kachisi, kunja kwa nsalu yotchinga. Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anaika choikapo nyali m'chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi. Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anaika guwa la nsembe lagolide m'chihema chokomanako chakuno cha nsalu yotchinga; nafukizapo chofukiza cha fungo lokoma; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anapachika ku Kachisi nsalu yotsekera pakhomo. Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nuchinge likasalo ndi nsalu yotchingayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:1-3

Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa. Koma ansembe aakulu anapangana kuti akaphe Lazaronso; pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu. M'mawa mwake khamu lalikulu la anthu amene adadza kuchikondwerero, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu, anatenga makwata a kanjedza, natuluka kukakomana ndi Iye, nafuula, Hosana; wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye, ndiye mfumu ya Israele. Koma Yesu, m'mene adapeza kabulu anakhala pamenepo; monga mulembedwa: Usaope, mwana wamkazi wa Ziyoni; taona mfumu yako idza wokhala pa mwana wa bulu. Izi sanazidziwa ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi. Pamenepo khamulo limene linali pamodzi ndi Iye, m'mene anaitana Lazaro kutuluka kumanda, namuukitsa kwa akufa, anachita umboni. Chifukwa cha ichinso khamulo linadza kudzakomana ndi Iye, chifukwa anamva kuti Iye adachita chizindikiro ichi. Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye. Ndipo anamkonzera Iye chakudya komweko; ndipo Marita anatumikira; koma Lazaro anali mmodzi wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye. Koma panali Agriki ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira pachikondwerero. Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa m'Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu. Filipo anadza nanena kwa Andrea; nadza Andrea ndi Filipo, nanena ndi Yesu. Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa Munthu alemekezedwe. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri. Iye wokonda moyo wake adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wake m'dziko lino lapansi adzausungira kumoyo wosatha. Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu. Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi. Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ochokera Kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso. Chifukwa chake khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi Iye. Pamenepo Maria m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:6-7

mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za chofukiza cha fungo lokoma; miyala yaberulo, ndi miyala yoika paefodi, ndi pachapachifuwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 2:10

Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 2:2-3

Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi lubani wake wonse; ndipo wansembeyo aitenthe chikumbutso chake pa guwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova. Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:29-30

Amuna ndi akazi onse a ana a Israele amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova anauza ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chaufulu, kuchipereka kwa Yehova. Musamasonkha moto m'nyumba zanu zilizonse tsiku la Sabata. Ndipo Mose anati kwa ana a Israele, Taonani, Yehova anaitana, ndi kumtchula dzina lake, Bezalele, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:22

ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:5-6

Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka. Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Yesu, ndimakukondani ndi mtima wanga wonse, ndimakutamandani chifukwa cha ukulu ndi kukongola kwanu. Ndinu Mulungu wanga, kuyambira m'mimba mwa mayi wanga munandisankha ndipo munaika cholinga chosatha mwa ine. Ndingaleke bwanji kukudalitsani? Mzimu wanga umakondwerera ukulu wanu chifukwa cha chikondi chanu chomwe mwandionetsa, ndipo m'mawa uliwonse mumandikomera mtima. Mzimu Woyera, ndimadzigonjera pansi pa mapazi anu ndipo ndikuvomereza kuti zonse zomwe ndili nazo ndi chifukwa cha inu. Palibe chomwe ndingadzitamandire nacho; ulemerero wonse ndi wanu. Lero ndikupemphani kuti mundithandize kukhala wolimba m'maitanidwe anu. Musandilole kupatuka ku chifuniro chanu. Ndikufuna kukhala mwa inu kuti ndikwaniritse ntchito yomwe munandipatsa, chifukwa munandipaka mafuta kuti ndilalikire uthenga wanu ndikulimbitsa thupi lanu. Mundipatse nzeru zanu ndi luntha lanu, ndipo mundionetse njira yoyenera kutsata. Zikomo chifukwa cha zonse, chifukwa cha chisomo ndi chiyanjo chanu. Ndimakutamandani chifukwa cha amene muli ndi zonse zomwe mwatichitira. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa