Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


97 Mau a m'Baibulo Okhudza Kuseka

97 Mau a m'Baibulo Okhudza Kuseka

Mulungu wanga wasandutsa kulira kwanga kukhala kuseka. Wapukuta misozi yanga, wandipatsa chimwemwe. Ndikudziwa kuti mavuto sadzatha, koma ndikukuuzani, ndi mwayi wodalira Mulungu, kumudziwa, ndi kukhala mokhulupirira mphamvu ya chikondi chake.

Sekani, tawani, ndipo muonetse mdani wanu kuti ndinu wopambana mwa Khristu. Lolani chimwemwe chidzaze mtima mwanu chifukwa cha zimene Ambuye adzachita m'moyo mwanu. Musayang'ane pamavuto anu a tsopano, chifukwa chimwemwe cha chipulumutso chanu chidzabwezeretsedwa ndipo mudzatha kuseka mtsogolo, chifukwa mukuyembekezera Ambuye, amene amakulimbikitsani, amakusamalirani, ndipo sakusiyani.

Sekani, ngakhale muli nokha, lolani kuseka kwanu kumveke ndi kusokoneza adani anu, ngakhale mukuvutika, chifukwa Mlengi wanu sakusiyani pansi, adzakutulutsani ndi kumenyera nkhondo yanu, adzakupatsani chipambano ndipo adzakuthandizani kumasuka ku ululu ndi mantha.

Pakamwa panu padzadzazidwa ndi kuseka, mudzalambira ukulu wake nthawi zonse ndipo maso anu adzapitiriza kuona ubwino wake pakati pa dziko la amoyo.




Yobu 8:21

Koma adzadzaza m'kamwa mwako ndi kuseka, ndi milomo yako kufuula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 2:2

Ndinati, Kuseka ndi masala; ndi chimwemwe kodi chichita chiyani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 2:4

Wokhala m'mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 5:22

Chipasuko ndi njala udzaziseka; ngakhale zilombo za padziko osaziopa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 41:29

Zibonga ziyesedwa chiputu, iseka kuthikuza kwake kwa nthungo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:13

Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:9

Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:2

Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati mwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 59:8

Koma Inu, Yehova, mudzawaseka; mudzalalatira amitundu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 18:12-15

ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba? Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba? Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna. Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; chifukwa anaopa. Ndipo anati, Iai; koma unaseka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:21

Odala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; chifukwa mudzaseka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:4

mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakuvina;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:26

Inetu ndidzachitira chiphwete tsoka lanu, ndidzatonyola pakudza mantha anu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:3

Chisoni chiposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 52:6

Ndipo olungama adzachiona, nadzaopa, nadzamseka, ndi kuti,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:13

Ngakhale m'kuseka mtima uwawa; ndipo matsiriziro a chiphwete ndi chisoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 21:6

Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:6

Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:22

Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:25

Avala mphamvu ndi ulemu; nangoseka nthawi ya m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:11

Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:5

Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:12

Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:15

Odala anthu akuona zotere; odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 4:7

Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga, chakuposa chao m'nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:6

Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 2:24

Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m'ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:19-20

Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu. Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka. Pakuti sadzakumbukira masiku a moyo wake kwambiri; chifukwa Mulungu amvomereza m'chimwemwe cha mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 8:15

Pompo ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m'vuto lake masiku onse a moyo wake umene Mulungu wampatsa pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 9:7-9

Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako. Zovala zako zikhale zoyera masiku onse; mutu wako usasowe mafuta. Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:3

ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 65:18-19

Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala kunthawi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ake okondwa. Ndipo ndidzasangalala m'Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akufuula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zefaniya 3:17

Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:11

Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chidzale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:24

Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:13

Koma tsopano ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m'dziko lapansi, kuti akhale nacho chimwemwe changa chokwaniridwa mwa iwo okha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:12

Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu; ndipo mzimu wakulola undigwirizize.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:25

Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu; koma mau abwino aukondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 28:7

Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:11

Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:11-12

Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero, kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:12

Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:21

Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:15

Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17

Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:13

Mtima wokondwa usekeretsa nkhope; koma moyo umasweka ndi zowawa za m'mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:15

Masiku onse a wosauka ali oipa; koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:30

Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima; ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:15

Kuchita chiweruzo kukondweretsa wolungama; koma kuwaononga akuchita mphulupulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:6

M'kulakwa kwa woipa muli msampha; koma wolungama aimba, nakondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:4

Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:16

Kondwerani nthawi zonse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 97:1

Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere; zisumbu zambiri zikondwerere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:24

Tsiku ili ndilo adaliika Yehova; tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:2

Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:28

Chiyembekezo cha olungama ndicho chimwemwe; koma chidikiro cha oipa chidzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 12:3

Chifukwa chake mudzakondwera pakutunga madzi m'zitsime za chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:3

Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 15:16

Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:3

Koma olungama akondwere; atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu; ndipo asekere nacho chikondwerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:4

Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu, ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 15:7

Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 15:10

Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:23

Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi chimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikulu Kumwamba; pakuti makolo ao anawachitira aneneri zonga zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:8

amene mungakhale simunamuona mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:4

ndipo izi tilemba ife, kuti chimwemwe chathu chikwaniridwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:17-18

Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse; momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 149:2

Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga; ana a Ziyoni asekere mwa mfumu yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:15

Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:2

Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:14

Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:20

Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa m'Mwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:46

Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi m'Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 7:4

Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:10

Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Ine wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:13

Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:21

Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye, chifukwa takhulupirira dzina lake loyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 35:9

Ndipo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova; udzasekera mwa chipulumutso chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:111

Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:1-3

Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota. Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati mwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu. Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:20

Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzachita chisoni inu, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:24

Mau okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m'moyo ndi olamitsa mafupa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 51:11

Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni; ndi nyimbo ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; adzakhala m'kusangalala ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:52

Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:10

monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:17

Usakondwere pakugwa mdani wako; mtima wako usasekere pokhumudwa iye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 6:14-16

Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta. Chomwecho Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anakwera nalo likasa la Yehova, ndi chimwemwe ndi kulira kwa malipenga. Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:25

Tsoka inu okhuta tsopano! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, akuseka tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 60:5

Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 8:10

Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:7

Pakuti munakhala mthandizi wanga; ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:7

Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 35:10

ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 22:26

Pakuti pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuyonse, ndi kuweramutsa nkhope yako kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 5:11

Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu, afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira; nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:19-20

ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino. ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga, dzina lanu ndi lopatulika ndi loopsa, palibe chofanana ndi chiyero chanu. Atate Woyera, ndikubwera kwa inu ndikukuthokozani chifukwa tsiku lililonse mumandipatsa mwayi wosangalala ndi ubwino wanu ndipo ndimatha kupumula m'manja mwanu ndikuyembekezera mawu anu chifukwa mudalonjeza kuti mudzadzaza pakamwa panga ndi kuseka ndi milomo yanga ndi chimwemwe. Ambuye, zikomo chifukwa chimwemwe changa sichichokera ku malingaliro kapena zochitika, koma kudzera mwa inu. Ndithandizeni nthawi zonse kuonetsa zipatso za Mzimu wanu Woyera kuti ndisadalire zomwe maso anga akuwona, chifukwa inu mwanenadi kuti: "Ndidzaseka chiwonongeko ndi njala, Sindiwopa zilombo za kuthengo". Ndiyese tsiku lililonse kulimbitsa chikhulupiriro changa m'mawu anu kotero kuti kukhalapo kwanu kukhale patsogolo pa moyo wanga ndipo motero ndipatse chimwemwe kwa omwe ali pafupi nane, ndikumvetsa kuti ndinu amene mumalimbana nkhondo zanga ndikugonjetsa adani anga, pakuti mawu anu amati: "Iye amene amakhala kumwamba adzaseka; Ambuye adzawaseka". M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa