M’salmo 37:4 Davide anati, “Sangalala mwa Yehova, ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.” Kusangalala kumeneku, ndiko kukhala wachimwemwe chenicheni, wokhutira ndi chinthu chomwe chimatipatsa chimwemwe choona. Baibulo limatiphunzitsa kuti chimwemwe choonachi chimapezeka mwa Mulungu yekha. Tikamasangalala mwa Iye, mavuto athu ndi zovuta zathu zimachepa, podziwa kuti Iye ndiye wolamulira wa miyoyo yathu.
Tikamasangalala mwa Mulungu, ubwenzi wathu ndi Iye umalimba, timamuyandikira kwambiri, ndipo timaphunzira kudalira malonjezo ake. Kusangalala mwa Iye kumatithandizanso kukhala oyamikira, podziwa kuti madalitso athu onse amachokera ku chikondi chake ndi chisamaliro chake pa ife.
Koma kusangalala mwa Mulungu sikutanthauza kunyalanyaza maudindo athu a tsiku ndi tsiku kapena kuthawa mavuto. M’malomwake, kumatanthauza kupeza mphamvu ndi nzeru mwa Iye kuti tithe kuthana ndi mavutowo molimba mtima komanso modalira.
Kumbukira kuti kusangalala mwa Mulungu kumatipatsa moyo wabwino komanso watanthauzo. Kumatithandiza kupeza chikhutiro choona ndi kudziwa cholinga chimene Iye ali nacho pa moyo wathu.
Pakati pa zovuta ndi zosokoneza za dziko lino, tikumbukire kuti mwa Mulungu yekha ndi komwe tingapeze chimwemwe chimene mitima yathu imakhumba.
Nditamva mau anu, ndidaŵalandira bwino, mauwo adandipatsa chimwemwe ndi chisangalalo. Paja Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndimadziŵika ndi dzina lanu.
Amati, “Unkadalira Chauta, Chauta yemweyo akupulumutse. Akulanditsetu tsono, popeza kuti amakukonda.”
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Ndimakonda kuchita zimene mumafuna, Inu Mulungu wanga, malamulo anu ali mumtima mwanga.”
koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.
Hana adapemphera nati, “Mtima wanga ukukondwa chifukwa cha zimene Chauta wandichitira, Ndikuyenda ndi mdidi chifukwa cha Chauta. Pakamwa panga pakula nkuseka adani anga monyodola. Ndakondwa kwambiri chifukwa mwandipulumutsa.
Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”
Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.
Motero adagonjetsa mizinda yamalinga nalanda dziko lachonde, nyumba zodzaza ndi zinthu zabwino, zitsime zokumbakumba, minda yamphesa, minda yaolivi ndiponso mitengo yazipatso yochuluka kwambiri. Choncho iwowo ankadya, namakhuta, mpaka kumanenepa, ndipo ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu, Inu Chauta.
Mukatero ndiye kuti mudzakondwa mwa Ine, Chauta, ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi. Mudzadyerera dziko limene ndidapatsa Yakobe kholo lanu. Ine Chauta ndalankhula zimenezi ndi pakamwa panga.”
Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.
Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona.
Chauta akunena za anthu ameneŵa kuti, “Amakonda kuyendayenda kumene afuna, ndipo sangathe kudziletsa. Nchifukwa chake Ine Chauta sindingakondwere nawo, ndipo tsopano ndidzakumbukira kuipa kwao, ndidzaŵalanga chifukwa cha machimo ao.”
Nthaŵiyo nkuti ndili pambalipa ngati mmisiri wake, ndikumkondweretsa tsiku ndi tsiku, ndikusangalala pamaso pake nthaŵi zonse. Ndinkasangalala m'dziko lake lokhalamo anthu, ndi kumakondwa nawo ana a anthu.
Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika.
Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka.
“Ndakuuzani zimenezi kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.
Inu Chauta, mwandisangalatsa ndi ntchito zanu. Motero ndikufuula ndi chimwemwe chifukwa cha zimene Inu mwachita.
Paja Chauta amakondwera ndi anthu ake, amaŵalemekeza anthu odzichepetsa poŵagonjetsera adani ao.
Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.
Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse.
Sangalalani ndi kukondwa inu nonse okonda Mulungu, chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani. Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Mudzandikhutitsa ndi zonona, ndipo ndidzakutamandani ndi mau osangalala. Ndikagona pabedi panga ndimalingalira za Inu, usiku wonse ndimasinkhasinkha za Inu.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.” Mudzakondwera pokatunga madzi m'zitsime za chipulumutso.
komabe kwanga nkukondwerera mwa Chauta, kwanga nkusangalala chifukwa cha Mulungu Mpulumutsi wanga.
Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano.
Abale anga, potsiriza ndikuti, “Muzikondwa mwa Ambuye.” Kukulemberaninso mau omwewo sikondilemetsa, ndipo mauwo ngokuthandizani kukhala osakayika.
Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa ndinu a chikondi chosasinthika. Mwaona masautso anga, mwazindikira mavuto anga kuti ndi aakulu.
Inu ndi anthu a Chauta, kondwerani mwa iye, ndipo mumthokoze potchula dzina lake loyera.
Zoonadi, mwaisandutsa yodala kopambana mpaka muyaya. Mwaisangalatsa ndi chimwemwe, chifukwa muli nayo.
Inu Chauta, ife timatsata njira ya malamulo anu, ndipo timakhulupirira Inu. Mtima wathu umangolakalaka kukumbukira ndi kulemekeza dzina lanu.
Monga momwe mbaŵala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga umakhumbira Inu Mulungu wanga.
Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Kukhala tsiku limodzi m'mabwalo anu nkwabwino kwambiri kupambana kukhala masiku ambiri kwina kulikonse. Nkadakonda kukhala wapakhomo wa Nyumba ya Mulungu wanga kupambana kukhala m'nyumba za anthu oipa.
Komabe musakondwere chifukwa choti mizimu yoipa ikukugonjerani, koma muzikondwera kuti maina anu adalembedwa Kumwamba.”
Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero, amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta. Iwowo amakondwa masiku onse chifukwa cha Inu, ndipo amatamanda kulungama kwanu.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga.
kuti ndiwone zokoma za osankhidwa anu, kuti ndigaŵane nawo chisangalalo cha mtundu wanu, kuti ndipeze ulemerero pamodzi ndi anthu anu.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Mpaka tsopano simunapemphe kanthu potchula dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.”
Chauta amapha ludzu la munthu womva ludzu, amamudyetsa zinthu zabwino munthu womva njala.
Pakamwa panga padzafuula ndi chimwemwe, pamene ndikukuimbirani nyimbo zotamanda. Nawonso mtima wanga umene mwauwombola, udzaimba moyamika.
Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.
Ngodala anthu olandira madalitso ameneŵa. Ngodala anthu amene Mulungu wao ndi Chauta.
Chauta ndiye Mfumu, anthu a pa dziko lapansi akondwere, anthu onse a m'mbali mwa nyanja asangalale.
Amene Chauta adaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya, chifukwa cha zimene ndidzalenga. Ndidzalengadi Yerusalemu watsopano wodzaza ndi chimwemwe, ndipo anthu ake adzakhala okondwa. Mwiniwakene ndidzakhala wokondwa kwambiri chifukwa cha Yerusalemu, ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu ake. Kumeneko sikudzamvekanso kulira kapena kudandaula.
Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina, mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo.
Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
Mudandidziŵitsa njira zopita ku moyo, ndipo mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’
Ndidzatonthoza mtima Ziyoni, ndidzaŵatonthoza mtima okhala ku mabwinja ake. Ngakhale dziko lake ndi chipululu, ndidzalisandutsa ngati Edeni. Ngakhale dziko lake ndi thengo, ndidzalisandutsa ngati munda wa Chauta. Kumeneko anthu adzakondwa ndi kusangalala, adzaimba nyimbo zondilemekeza ndi zondithokoza.
Mumaŵadyetsa zonona m'nyumba mwanu, ndipo mumaŵamwetsa madzi a mu mtsinje wa madalitso anu.
Mosakayika konse ndikudziŵa kuti ndidzakhalapobe. Ndidzapitiriza kukhala nanu nonsenu, kuthandiza kuti chikhulupiriro chanu chizikula, ndipo chikupatseni chimwemwe koposa kale.
Munthu wovomera malangizo, zinthu zidzamuyendera bwino, ndi wodala amene amadalira Chauta.
Tsono ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu, kwa Mulungu amene amandipatsa chimwemwe chopambana. Ndipo ndidzakutamandani ndi pangwe, Inu Mulungu, Mulungu wanga.
Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse. Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa.
Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.
Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu, mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu. Iwo akukondwa pamaso panu monga m'mene anthu amakondwera nthaŵi ya masika, monganso m'mene anthu amakondwera pogaŵana zofunkha.
Tidzazeni m'maŵa mulimonse ndi chikondi chanu chosasinthika, kuti tizikondwa ndi kusangalala masiku athu onse.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
Malamulo a pakamwa panu amandikomera kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva.
Ngwodala munthu amene Inu mumamsankha nkubwera naye kudzakhala m'mabwalo anu. Mutikhutitse ndi zinthu zabwino za m'Nyumba yanu, Nyumba yanu yoyera.
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa. Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.” Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo. Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi.
Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta. Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe ndi mtima wanga wonse.
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.