Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, kumwetera kumaso ndi mtima wonse, komanso kupangitsa ena kuseka, kungakhale chinthu chabwino kwambiri, ngati tachita pa nthawi yoyenera ndi pamalo oyenera. Chofunika ndi kuona kumwetera kumaso ngati chinthu chabwino m'moyo, chomwe chingathandize ena.
Zoona, kuchita zinthu mopitirira muyeso sikuli bwino. Pakati pa kukhala munthu wosasangalala nthawi zonse ndi kumwetera kumaso kopanda tanthauzo, pali malo pakati, pakati penipeni, pamene nzeru ndi chimwemwe zingagwirizane bwino, komanso kukhala chete ndi kumwetera kumaso. Chilichonse chili ndi nthawi yake ndi malo ake.
Kuseka ndi chizindikiro cha ufulu umene Khristu anatipatsa kudzera mu nsembe yake yachikondi, ndipo kumwetera kumaso kochokera pansi pa mtima kungachiritse mtima wopweteka. Kumwetera kumaso pakati pa ululu ndi kusangalala ndi Mlengi wako ndi chimene Mulungu amafuna kuti uzichita nthawi zonse.
Sindikudziwa kuti muli pa vati liti panopa, koma ndikukulimbikitsani kuti mupukute misozi yanu, muwone mmwamba, ndi kuyambanso kumwetera, chifukwa muli ndi zifukwa zambiri zokondwerera mwa Yesu.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
“Ndakuuzani zimenezi kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Pamenepo tidasekera kwambiri, ndipo tidalulutira ndi chimwemwe. Tsono mitundu ina ya anthu inkanena kuti, “Chauta waŵachitira zazikulu.”
Pali nthaŵi yomva chisoni ndi nthaŵi yosangalala, nthaŵi yolira maliro ndi nthaŵi yovina.
Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Tsono Sara adati, “Mulungu wandikondweretsa ndi kundiseketsa. Aliyense amene adzamve zimenezi, adzakondwera nane.”
Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina, mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo.
Kuseka kwa zitsiru kuli ngati kuthetheka kwa moto kunsi kwa mbiya. Zimenezinso nzachabechabe.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Koma anthu anu Mulungu, akondwere, asangalale pamaso panu, inde, asekere ndi chimwemwe.
Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu, azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu.”
Tidzazeni m'maŵa mulimonse ndi chikondi chanu chosasinthika, kuti tizikondwa ndi kusangalala masiku athu onse.
Inu Chauta, mwandisangalatsa ndi ntchito zanu. Motero ndikufuula ndi chimwemwe chifukwa cha zimene Inu mwachita.
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa. Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.” Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo. Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Amaŵalira anthu amene amamumvera, ndipo anthuwo amakhaladi ndi chimwemwe. Inu ndi anthu a Chauta, kondwerani mwa iye, ndipo mumthokoze potchula dzina lake loyera.
Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.
Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe. Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri.
Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake. Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.
Ngodala anthu olandira madalitso ameneŵa. Ngodala anthu amene Mulungu wao ndi Chauta.
Chiyembekezo cha wokhulupirira chimapezetsa chimwemwe, koma zimene woipa amayembekezera, zimafera m'mazira.
Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.
Kuŵala kwa anthu a Mulungu kumachita kuti ngwee, koma nyale ya anthu oipa mtima siidzalephera kuzima.
Munthu wozunzika masiku ake onse amakhala oipa, koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthaŵi zonse.
Munthu wovomera malangizo, zinthu zidzamuyendera bwino, ndi wodala amene amadalira Chauta.
Pajatu munthu wokondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamsandutsa waluntha, wanzeru ndi wosangalala. Koma wochimwa amampatsa ntchito yokunkha ndi younjika zinthu, kenaka zonsezo nkuzipatsa munthu wokondwetsa Mulungu. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
Ndikudziŵa kuti kwa anthu palibe chabwino china choposa kukhala osangalala ndi kumadzikondweretsa nthaŵi yonse ya moyo wao. Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa.
Choncho ndidaona kuti palibe chinthu chabwino kuposa kuti munthu azikondwerera ntchito yake, pakuti chake chenicheni nchimenechi. Ndani angathe kudziŵa chimene chidzamchitikire iye atafa?”
Mwina Mulungu amamlemeretsa munthu pakumpatsa chuma ndi zabwino zina, namlola kuti akondwerere zonsezo. Munthuyo azilandire zimenezo ndi kumakondwerera ntchito zake zonse zolemetsa. Imeneyi ndi mphatso yochokeradi kwa Mulungu.
Uzikondwa mwai ukakufikira, ndipo tsoka likakugwera uzilingalirapo bwino pamenepo. Udziŵe kuti ndi Mulungu yemwe amene amatumiza mwai ndi tsoka. Amatero kuti munthu asadziŵiretu zimene zidzachitike m'tsogolo.
Ndiye iwe usaope, uzidya chakudya chako mokondwa, uzimwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, pakuti Mulungu wavomereza kale zochita zakozo.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.” Mudzakondwera pokatunga madzi m'zitsime za chipulumutso.
Amene Chauta adaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
Amene mudaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa. Chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pankhope pao. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chisangalalo. Chisoni ndi kubuula zidzatha.
“Inu anthu anga, mudzachoka ku Babiloni mokondwa, adzakutulutsani mumzindamo mwamtendere. Inu mukufika, mapiri ndi magomo adzakuimbirani nyimbo. Nayonso mitengo yonse yam'thengo idzakuwomberani m'manja.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya, chifukwa cha zimene ndidzalenga. Ndidzalengadi Yerusalemu watsopano wodzaza ndi chimwemwe, ndipo anthu ake adzakhala okondwa. Mwiniwakene ndidzakhala wokondwa kwambiri chifukwa cha Yerusalemu, ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu ake. Kumeneko sikudzamvekanso kulira kapena kudandaula.
Nditamva mau anu, ndidaŵalandira bwino, mauwo adandipatsa chimwemwe ndi chisangalalo. Paja Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndimadziŵika ndi dzina lanu.
Anamwali adzavina mokondwa, achinyamata ndi okalamba omwe adzasangalala. Kulira kwao kuja ndidzakusandutsa chimwemwe. Ndidzaŵasangalatsa, ndidzaŵakondwetsa, nkuchotsa chisoni chao.
Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.
Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.
“Pamene mukusala zakudya, musamaonetsa nkhope zachisoni monga amachitira anthu achiphamaso aja. Iwo amaipitsa nkhope kuti anthu aone kuti akusala zakudya. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe, pamene ukusala zakudya, samba m'maso nkudzola mafuta kumutu, kuti anthu asadziŵe kuti ukusala zakudya. Koma Atate ako amene ali osaoneka ndiwo adziŵe. Ndipo Atate akowo amene amaona zobisika, adzakupatsa mphotho.
Kumeneko anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu wa ziwalo zakufa ali chigonere pa machira. Poona chikhulupiriro chao, Yesu adauza munthu wa ziwalo zakufayo kuti, “Limba mtima, mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”
Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’
Apo azimaiwo adachoka kumandako msanga, ali ndi mantha komanso ndi chimwemwe chachikulu, nathamanga kukauza ophunzira ake aja.
“Ndinu odala, inu amene mukumva njala tsopano, chifukwa mudzakhuta. “Ndinu odala, inu amene mukulira tsopano, chifukwa mudzakondwa.
Komabe musakondwere chifukwa choti mizimu yoipa ikukugonjerani, koma muzikondwera kuti maina anu adalembedwa Kumwamba.”
Yesu adapitiriza mau kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima.”
Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
Ndithu ndikunenetsa kuti inu mudzalira ndi kukhuza, koma anthu odalira zapansi pano adzakondwa. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasanduka chimwemwe.
Chomwecho inunso mukuvutika tsopano, koma ndidzakuwonaninso. Pamenepo mtima wanu udzakondwa, ndipo palibe munthu amene adzakulandani chimwemwe chanucho.
“Tsopano ndilikudza kwa Inu. Ndikulankhula zimenezi pamene ndili pansi pano, kuti chimwemwe changa chikhalenso chodzaza mwa iwowo.
Mudandidziŵitsa njira zopita ku moyo, ndipo mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’
Ndipo ophunzira a ku Antiokeya adadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo adakhala ndi chimwemwe chachikulu.
Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu. Mulungu adapereka Malamulo kuti anthu azindikire kuchuluka kwa machimo ao. Koma pamene uchimo udachuluka, kukoma mtima kwa Mulungu kudachuluka koposa. Choncho monga uchimo unkalamulira anthu ndi kudzetsa imfa pa iwo, momwemonso kunali koyenera kuti kukoma mtima kwa Mulungu kulamulire pakudzetsa chilungamo kwa anthu, ndi kuŵafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira,
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Ndimakukhulupirirani kwambiri, ndipo ndimakunyadirani kwenikweni. Zondilimbitsa mtima zandichulukira, ndipo m'zovuta zathu zonse ndakondwa kopambana.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Abale anga, potsiriza ndikuti, “Muzikondwa mwa Ambuye.” Kukulemberaninso mau omwewo sikondilemetsa, ndipo mauwo ngokuthandizani kukhala osakayika.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yaulemerero, kuti muzipirira zonse ndi mitima yoleza ndi yosangalala.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Inu mwakhala mukutsata chitsanzo chathu ndi cha Ambuye. Ngakhale mudapeza masautso ambiri, mudalandira mau athu mwa chimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera.
Ndikamakumbukira misozi yako, ndimafunitsitsa kukuwona, kuti ndikhale ndi chimwemwe chodzaza.
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu. Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani. Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena. Paja munthu amene amangomva chabe mau, osachita zimene wamvazo, ali ngati munthu woyang'anira nkhope yake yachibadwa m'galasi. Tsono amati akadzipenya, amachokapo, posachedwa nkuiŵalako m'mene akuwonekera. Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse. Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga. Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi. Paja mukudziŵa kuti mukamayesedwa m'chikhulupiriro chanu, mumasanduka olimbika.
Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.
Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka.
Koma kondwerani popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu.
Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu.
Sangalalani ndi kukondwa inu nonse okonda Mulungu, chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani. Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe.
Chauta ndiye Mfumu, anthu a pa dziko lapansi akondwere, anthu onse a m'mbali mwa nyanja asangalale.
Tamandani Chauta. Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Munthu woipa amakodwa ndi zolakwa zake, koma wochita chilungamo amakhala wokondwa ndi womasuka.
Nchifukwa chake ndikuti munthu azikondwerera moyo, pakuti munthu alibe chinthu chinanso chabwino pansi pano choposa kudya, kumwa ndi kumadzikondweretsa. Akamatero, munthuyo adzakhala ndi chimwemwe pa ntchito yake masiku onse a moyo wake, amene Mulungu wampatsa pansi pano.
Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu, mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu. Iwo akukondwa pamaso panu monga m'mene anthu amakondwera nthaŵi ya masika, monganso m'mene anthu amakondwera pogaŵana zofunkha.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.