Chimwemwe cha Mulungu chingathe kuchotsa chisoni chanu chonse ndi kudzaza mtima wanu ndi chikondwerero. Sichi chimwemwe chomwe chimadalira momwe mukumvera, koma chomwe mumachimanga tsiku ndi tsiku mu mpanda wa Mzimu Woyera.
Ubwenzi wanu ndi Iye ndi womwe ungakutsogolereni kumudziwa bwino, ndipo mukamudziwa bwino, mudzatha kumulambira mozama mpaka mumtima mwanu mutuluke mitsinje ya chitamando mukaona ukulu wa Mpulumutsi wanu.
Mudzazindikira ubwino wake pa moyo wanu ndipo pakamwa panu padzadzaza kuseka. Pamenepo ndiye mudzazindikira kuti chimwemwe cha dziko lino chikhazikika pa zinthu zosatha, koma chimwemwe chomwe Yesu amaika mu mzimu chimakhala kwamuyaya.
Mulungu nthawi ino akufuna kuti ana ake adzipulumutse mwa Iye, ndipo pakati pa misozi, apeze nyimbo yotamanda. Mukagwada pa mapazi ake, mudzalandira kudzazidwa kwake ndi kutonthozedwa.
Choncho, m'masautso, m'njira ndi m'mayesero, chimwemwe cha Ambuye chidzakhala mphamvu yanu, ndipo simudzataya udindo wanu. Mwa chisomo cha Mulungu, chimwemwe chake chidzakuthandizani ndi kukupatsani mphamvu zopirira vuto lililonse.
Ambuye ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa; mwa Iye mtima wanga umakhulupirira, ndipo ndimalandira thandizo; chifukwa cha ichi mtima wanga ukondwera, ndipo ndidzamuthokozera ndi nyimbo yanga (Masalmo 28:7).
Alimi onse amatengako dzinthu dzam'minda, koma ndi mfumu yokha imene imaona phindu lake la mindayo.
Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Choncho, Mulungu akalola, ndidzafika kwanuko ndili wokondwa, ndipo ndidzasanguluka pocheza nanu.
Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga.
“Ndakuuzani zimenezi kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.
Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse.
Uzikondwa mwai ukakufikira, ndipo tsoka likakugwera uzilingalirapo bwino pamenepo. Udziŵe kuti ndi Mulungu yemwe amene amatumiza mwai ndi tsoka. Amatero kuti munthu asadziŵiretu zimene zidzachitike m'tsogolo.
Amatiyesa achisoni, komabe ndife okondwa masiku onse. Amatiyesa amphaŵi, komabe timalemeretsa anthu ambiri. Amatiyesa opanda kanthu, komabe tili ndi zonse.
Komabe musakondwere chifukwa choti mizimu yoipa ikukugonjerani, koma muzikondwera kuti maina anu adalembedwa Kumwamba.”
Yesu adapitiriza mau kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima.”
Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda. Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe, lizani pangwe ndi nyimbo zokoma. Imbirani Chauta Mfumu, imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete.
Tsono ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu, kwa Mulungu amene amandipatsa chimwemwe chopambana. Ndipo ndidzakutamandani ndi pangwe, Inu Mulungu, Mulungu wanga.
Malo amene mumakhalamo, Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndi okoma kwambiri. Kukhala tsiku limodzi m'mabwalo anu nkwabwino kwambiri kupambana kukhala masiku ambiri kwina kulikonse. Nkadakonda kukhala wapakhomo wa Nyumba ya Mulungu wanga kupambana kukhala m'nyumba za anthu oipa. Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama. Inu Chauta Wamphamvuzonse, ngwodala munthu woika chikhulupiriro chake pa Inu. Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta. Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe ndi mtima wanga wonse.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Inu ndi anthu a Chauta, kondwerani mwa iye, ndipo mumthokoze potchula dzina lake loyera.
Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Koma ine ndili ngati mtengo wauŵisi wa olivi m'Nyumba ya Mulungu. Ndimaika mtima nthaŵi zonse pa chikondi chosasinthika cha Mulungu. Ndidzakuthokozani Inu Mulungu mpaka muyaya, chifukwa cha zimene mwachita. Ndidzatamanda dzina lanu pamaso pa anthu okukondani, pakuti ndinu abwino.
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse. Tumikirani Chauta mosangalala. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
Zoonadi, mwaisandutsa yodala kopambana mpaka muyaya. Mwaisangalatsa ndi chimwemwe, chifukwa muli nayo.
Koma anthu anu Mulungu, akondwere, asangalale pamaso panu, inde, asekere ndi chimwemwe.
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima.
Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.
Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa, ndipo m'katikati mwangamu ndikusangalala. Thupi langanso lidzakhala pabwino,
“Inu anthu anga, mudzachoka ku Babiloni mokondwa, adzakutulutsani mumzindamo mwamtendere. Inu mukufika, mapiri ndi magomo adzakuimbirani nyimbo. Nayonso mitengo yonse yam'thengo idzakuwomberani m'manja.
Inu Chauta, mwandisangalatsa ndi ntchito zanu. Motero ndikufuula ndi chimwemwe chifukwa cha zimene Inu mwachita.
Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona. Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta, mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira.
Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero, amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta.
Maso onse amayang'anira kwa Inu, ndipo mumaŵapatsa chakudya pa nthaŵi yake. Mumafumbatula dzanja lanu, ndipo mumapatsa chamoyo chilichonse zofuna zake.
Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu. Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani. Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena. Paja munthu amene amangomva chabe mau, osachita zimene wamvazo, ali ngati munthu woyang'anira nkhope yake yachibadwa m'galasi. Tsono amati akadzipenya, amachokapo, posachedwa nkuiŵalako m'mene akuwonekera. Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse. Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga. Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi. Paja mukudziŵa kuti mukamayesedwa m'chikhulupiriro chanu, mumasanduka olimbika.
Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’
Nchifukwa chake Chauta wandipatsa mphotho molingana ndi ntchito zanga zabwino, monga momwe akuwonera kuti ndilibe mlandu.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.
Tamandani Chauta. Ndidzathokoza Chauta ndi mtima wanga wonse pa msonkhano wa anthu olungama mtima.
Mtima wa munthu umatha kupirira matenda, koma munthu akataya mtima, ndani angathe kumlimbitsanso?
Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Sangalalani ndi kukondwa inu nonse okonda Mulungu, chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani. Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe.
Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka, ndithu, mtima wanga wakonzekadi! Ndidzaimba nyimbo, nyimbo yake yotamanda. Lumpha, iwe mtima wanga.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Pakamwa panga padzafuula ndi chimwemwe, pamene ndikukuimbirani nyimbo zotamanda. Nawonso mtima wanga umene mwauwombola, udzaimba moyamika.
Chibwere ndithu chipulumutso cha Israele kuchokera ku Ziyoni. Chauta akadzaŵabwezera ufulu anthu ake, Yakobe adzakondwera, Israele adzasangalala kwambiri.
Abale anga, potsiriza ndikuti, “Muzikondwa mwa Ambuye.” Kukulemberaninso mau omwewo sikondilemetsa, ndipo mauwo ngokuthandizani kukhala osakayika.
Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, ndipo chikondi chake nchamuyaya. Adani a mitundu yonse adandizinga, koma ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta. Adandizinga, inde adandizinga pa mbali zonse, koma ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta. Adandizinga ngati njuchi, koma adatha msanga ngati moto wapaminga. Ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta. Adandikankha kwambiri, kotero kuti ndinali pafupi kugwa, koma Chauta adandithandiza. Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga. Ndiye mpulumutsi wanga. Mverani nyimbo m'mahema mwa anthu a Mulungu, nyimbo zokondwerera kupambana, zakuti, “Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu, dzanja lamanja la Chauta lapambana, dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.” Sindidzafa, ndidzakhala moyo, ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta. Chauta wandilanga koopsa, koma sadandisiye kuti ndife. Tsekulireni zipata za Nyumba ya Mulungu, kuti ndifike ku malo ake achilungamo, ndikathokoze Chauta. Aisraele anene kuti, “Chikondi chake nchamuyaya.”
Amene Chauta adaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
Tsono anthu adakondwa chifukwa chakuti akulu aowo ankapereka mwaufulu ndiponso ndi mtima wao wonse. Nayenso mfumu Davide adakondwa kwambiri.
Ndidzasinkhasinkha za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu, ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.
Mverani nyimbo m'mahema mwa anthu a Mulungu, nyimbo zokondwerera kupambana, zakuti, “Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu,
Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!”
Tsiku limenelo aliyense adzati, “Uyu ndiye Mulungu wathu! Tidamkhulupirira kuti adzatipulumutsa. Iyeyu ndiye Chauta. Tidamkhulupirira, tsopano tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa choti watipulumutsadi.”
Okhulupirika akondwerere chigonjetso chopambanachi, aziimba mokondwa ali gone pa mabedi.
Kunena za oyera mtima amene ali pansi pano, ameneŵa ndi olemekezeka, ndipo ndimakondwera nawo.
Koma chonsecho ndili ndi Inu nthaŵi zonse. Inu mumandigwira dzanja lamanja. Mumandiwongolera ndi malangizo anu, pambuyo pake mudzandilandira ku ulemerero.
Pamene Chauta adabwezera akapolo ku Ziyoni, tinali ngati anthu amene akulota. Pamenepo tidasekera kwambiri, ndipo tidalulutira ndi chimwemwe. Tsono mitundu ina ya anthu inkanena kuti, “Chauta waŵachitira zazikulu.”
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
Pambuyo pake Davide adalamulanso atsogoleri a Alevi kuti asankhe ena mwa abale ao, kuti aziimba ndi kuliza mwamphamvu zipangizo zoimbira monga azeze, apangwe, ndiponso ziwaya zamalipenga, kuti mau achimwemwe amveke bwino.
Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga, monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere. Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga.
Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse. Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa.
Chiyembekezo cha wokhulupirira chimapezetsa chimwemwe, koma zimene woipa amayembekezera, zimafera m'mazira.
Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa.
“Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m'munda. Munthu wina atachitumba, amachibisanso. Kenaka mokondwa amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula munda uja.
Nawonso ana ndi makanda omwe amauimbira. Mwamanga linga chifukwa cha adani anu, kuti mugonjetse onse okuukirani.
Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta. Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe ndi mtima wanga wonse.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Pamene ndinali m'mavuto ndidapemphera kwa Chauta, ndipo Iye adandichotsera mavutowo. Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani?
Mosakayika konse ndikudziŵa kuti ndidzakhalapobe. Ndidzapitiriza kukhala nanu nonsenu, kuthandiza kuti chikhulupiriro chanu chizikula, ndipo chikupatseni chimwemwe koposa kale.
Ndi waukulu ubwino wanu umene mwaŵasungira anthu okumverani, umene mwaŵachitira anthu othaŵira kwa Inu, aliyense waona zimenezi.
Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”
Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu. Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.
Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa ndinu a chikondi chosasinthika. Mwaona masautso anga, mwazindikira mavuto anga kuti ndi aakulu.
Munthu wozunzika masiku ake onse amakhala oipa, koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthaŵi zonse.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.” Mudzakondwera pokatunga madzi m'zitsime za chipulumutso.
Amene mudaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa. Chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pankhope pao. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chisangalalo. Chisoni ndi kubuula zidzatha.
Mpaka tsopano simunapemphe kanthu potchula dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.”
Mudandidziŵitsa njira zopita ku moyo, ndipo mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.