Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


118 Mau a m'Baibulo Oletsa Kuweruza

118 Mau a m'Baibulo Oletsa Kuweruza

Tanthauzo la kuweruza m'Baibulo ndi kupanga chigamulo kapena maganizo pa chinthu kapena munthu wina. Tikamadzipanga oweluza ena, timadzikweza tokha pamwamba pa ena, zomwe sizikugwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.

Koma si kuweruza konse koipa; chomwe chili choipa ndi chinyengo. “Nanga iwe, uziona bwanji kachitsotso kali m’diso la m’bale wako, koma suzindira mtanda uli m’diso lako mwini? Kapena, unganene bwanji kwa m’bale wako, ‘Ndikulole ndikuchotse kachitsotsoko m’diso lako,’ pamene mtanda uli m’diso lako mwini? Wonyenga iwe! Choyamba chotsa mtanda m’diso lako mwini, ndipo pamenepo udzatha kuona bwino kuti uchotse kachitsotso m’diso la m’bale wako.” (Mateyu 7:3-5). Yesu amatsutsa chinyengo, akutiyeni tiyang'ane kaye mtima wathu tisanayambe kuweruza ena. Tifunikira kuchotsa mtanda m'maso mwathu tisanayambe kuchotsa kachitsotso m'maso mwa mnzathu.

Kodi njira yoyenera yoweruzira ndi iti? Choyamba, chilungamo n'chofunika kwambiri. Yesu anatiphunzitsa kuti: “Musamaweruze anthu potengera maonekedwe awo, koma weruzani mwachilungamo.” (Yohane 7:24).

Chachiwiri, ngati tikuweruza ena, tizichita zimenezi mwachikondi, popanda chinyengo, ndi kuwaitana kuti alape.




Mateyu 7:1-5

“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Kapena atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha? Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa. “Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka. “Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa. Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu? Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai. Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto. M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu. Choncho mudzaŵadziŵira zochita zao. “Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna. Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’ Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’ “Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba. Koma aliyense wongomva mau angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adaamanga nyumba yake pa mchenga. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo, ndipo idagwa. Kugwa kwake kunali koopsa.” Yesu atatsiriza kunena zimenezi, anthu onse aja adadabwa ndi kaphunzitsidwe kake, chifukwa ankaŵaphunzitsa monga munthu waulamuliro osati monga m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo. Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene m'maso mwako momwe muli chimtengo? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:31

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 11:3

Ndipo kuwopa Chauta ndiye chidzakhale chinthu chomkondweretsa. Sadzaweruza potsata zooneka pamaso, kapena kugamula mlandu potsata zakumva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:1-2

“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Kapena atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha? Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa. “Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka. “Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa. Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu? Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai. Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto. M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:37

“Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:16

Wina aliyense asakuzengeni mlandu pa nkhani yokhudza zakudya kapena zakumwa, kapena pa zokhudza masiku a chikondwerero, kapena a mwezi wokhala chatsopano, kapena pa zokhudza tsiku la Sabata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:10

Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:1-4

Abale anga, popeza kuti mumakhulupirira Ambuye athu Yesu Khristu, Ambuye aulemerero, musamakondera. Pajatu munthu wotsata Malamulo onse, akangophonyapo ngakhale pa mfundo imodzi yokha, ndiye kuti wachimwira Malamulo onsewo. Pakuti Mulungu amene adanena kuti, “Usachite chigololo”, adanenanso kuti, “Usaphe”. Ngati inu chigololo simuchita, koma kupha mumapha, ndiye kutitu mwachimwira Malamulo onse. Tsono muzilankhula ndi kuchita zinthu monga anthu oti Mulungu adzaŵaweruza potsata lamulo loŵapatsa ufulu. Paja munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso Mulungu adzamuweruza mopanda chifundo. Koma wochita chifundo alibe chifukwa choopera chiweruzo cha Mulungu. Abale anga, pali phindu lanji, ngati munthu anena kuti, “Ndili ndi chikhulupiriro,” koma popanda chimene akuchitapo? Kodi chikhulupiriro chotere chingampulumutse? Mwachitsanzo: mbale wina kapena mlongo ali ndi usiŵa, ndipo masiku onse alibe chakudya chokwanira. Tsono wina mwa inu angoŵauza kuti. “Pitani ndi mtendere, mukafundidwe ndipo mukakhute”, koma osaŵapatsa zimene akusoŵazo, pamenepo phindu lake nchiyani? Choncho, chikhulupiriro pachokha, chopanda ntchito zake, nchakufa basi. Koma kapena wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro, ineyo ndili ndi ntchito zabwino.” Pamenepo ine nkumuyankha kuti, “Uyesetse kundiwonetsa chikhulupiriro chako chopanda ntchito zakecho, ine ndi ntchito zanga ndikuwonetsa chikhulupiriro changa.” Inu mumakhulupirira kuti Mulungu ndi mmodzi yekha. Ai chabwino, mumakhoza, komatu ndi mizimu yoipa yomwe imakhulupirira zimenezi, imachitanso kunjenjemera. Mwachitsanzo: munthu wina aloŵa mumsonkhano mwanu atavala mphete zagolide m'manja, alinso ndi zovala zokongola. Winanso nkuloŵa, koma ali mmphaŵi, nsanza zili wirawira. Wopusawe, kodi ukufuna umboni wotsimikiza kuti chikhulupiriro chopanda ntchito zake nchachabe? Nanga Abrahamu, kholo lathu, suja adakhala wolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito yomwe adachita, muja adaapereka mwana wake Isaki pa guwa lansembe? Waona tsono kuti chikhulupiriro chake ndi zochita zake zidachitikira pamodzi. Zochita zake zidasandutsa chikhulupiriro chake kuti chifike pake penipeni. Motero zidachitikadi zimene Malembo adaanena, kuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, nchifukwa chake Mulungu adamuwona kuti ngwolungama;” mwakuti ankatchedwa bwenzi la Mulungu. Mukuwonatu kuti zochita zake za munthu ndizo zimamsandutsa wolungama pamaso pa Mulungu, osati chikhulupiriro chokha. Kodi suja zidaateronso ndi Rahabu, mkazi wadama uja? Iye adaalandira azondi aja, nkuŵabweza kwao poŵadzeretsa njira ina, ndipo adapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha zimene adaachitazo. Paja monga momwe thupi lopanda mzimu limakhala lakufa, moteronso chikhulupiriro chopanda ntchito zake nchakufa. Tsono inu pofuna kusamala kwambiri wovala zokongolayo, mumuuza kuti, “Khalani apa pabwinopa”, mmphaŵi uja nkumuuza kuti, “Iwe, kaimirire apo, kapena dzakhale pansi kumapazi kwangaku.” Limenelotu ndi tsankho pakati pa inu nokhanokha, ndipo inuyo mwasanduka oweruza a maganizo oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:11-12

Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza. Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:1-3

Tsono woweruza enawe, kaya ndiwe yani, ulibe pozembera. Pakutitu pamene ukuweruza mnzako, ukudzitsutsa wekha, popeza kuti iweyo woweruzawe umachita zokhazokhazo. Koma Mulungu adzaŵapatsa ulemerero, ulemu ndi mtendere onse ochita zabwino, poyamba Ayuda, kenaka anthu a mitundu inanso. Pajatu Mulungu alibe tsankho. Anthu onse amene adachimwa osadziŵa Malamulo, iwonso adzaonongeka ngakhale sadaŵadziŵe Malamulowo. Ndipo onse amene adachimwa atadziŵa Malamulo, adzaweruzidwa potsata Malamulowo. Pakuti amene ali olungama pamaso pa Mulungu si amene amangomva Malamulo chabe ai. Koma okhawo amene amachitadi zonenedwa m'Malamulo ndiwo amene Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama. Anthu amene sali Ayuda alibe Malamulo, koma pamene mwa iwo okha amachita zimene Malamulowo anena, amaonetsa kuti ali nawo malamulo mumtima mwao, ngakhale alibe Malamulo a Mose. Ntchito zaozo zimatsimikiza kuti Malamulowo ndi olembedwa m'mitima mwao. Mitima yao yomwe imatsimikiza kuti ndi momwemodi, popeza kuti maganizo ao m'chikatikati mwina amaŵatsutsa, mwina amaŵavomereza. Monga unenera Uthenga Wabwino umene ndimalalika, zidzateronso pa tsiku lija limene Mulungu mwa Khristu Yesu adzaweruza zinsinsi za m'mitima mwa anthu. Koma tsono iweyo amene umati ndiwe Myuda, umadalira Malamulo, ndipo umanyadira Mulungu wako. Ukudziŵa zimene Mulungu afuna kuti uchite, ndipo chifukwa udaphunzira Malamulowo, umadziŵanso kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa. Umakhulupirira kuti ndiwe mtsogoleri wa anthu akhungu, nyale younikira anthu amene ali mu mdima, Tikudziŵa kuti Mulungu salakwa akamaweruza anthu ochita zotere. mlangizi wa anthu opusa, ndiponso mphunzitsi wa anthu osadziŵa. Umatsimikiza kuti m'Malamulowo umapezamo nzeru zonse ndi zoona zonse. Tsono iwe wophunzitsa ena, bwanji sukudziphunzitsa wekha? Iwe wolalika kuti, “Osamaba,” bwanji iwenso umaba? Nanga iwe wonena kuti, “Osamachita chigololo,” bwanji iwenso umachita chigololo? Iwe amene umanyansidwa ndi mafano, bwanji umaba za m'nyumba zopembedzeramo mafanowo? Iwe wonyadira Malamulo a Mulungu, bwanji umachititsa Mulungu manyazi pakuphwanya Malamulowo? Ndi monga Malembo anenera kuti, “Anthu akunja amanyoza Mulungu chifukwa cha inu Ayudanu.” Kuumbala kwako nkopindulitsa ngati utsata Malamulo a Mulungu. Koma ngati suŵatsata Malamulowo, ukadayenera kungokhala wosaumbalatu basi. Koma ngati munthu wosaumbala atsata zimene Malamulowo anena, kodi iyeyu pamaso pa Mulungu sadzakhala ngati munthu woumbala, ngakhale ndi wosaumbala m'thupi? Nchifukwa chake wosaumbalayo amene amatsata Malamulo ndiye adzakutsutsa iwe amene uli woumbala, ndipo uli ndi Malamulo olembedwa, koma umaŵaphwanya. Myuda weniweni si amene amangooneka chabe ngati Myuda pamaso pa anthu. Ndipo kuumbala kwenikweni si kumene kumachitika m'thupi nkuwonekera ku anthu ai. Myuda weniwenitu ndi amene ali Myuda mumtima mwake, ndipo kuumbala kwenikweni ndi kwa mtima, kochitika ndi Mzimu Woyera, osati ndi Malamulo olembedwa ai. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ai. Tsono mnzangawe amene umaweruza ena ochita zimenezi, pamene iwenso umachita zomwezo, kodi ukuganiza kuti chidzakuphonya chiweruzo cha Mulungu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:37-42

“Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani. Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.” Yesu adaŵapheranso fanizo, adati, “Kodi wakhungu nkutsogolera wakhungu mnzake? Nanga onse aŵiri sadzagwa m'dzenje kodi? Suja adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, natenga buledi woperekedwa kwa Mulungu, naadya, nkupatsakonso anzake aja? Chonsecho nkosaloledwa kuti buledi ameneyo wina aliyense nkumudya kupatula ansembe okha.” Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense pamene watsiriza maphunziro ake, adzafanafana ndi mphunzitsi wake. “Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Mbale wanga, taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene iweyo sukuchiwona chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:12-13

Nanga kuweruza anthu amene adakali kunja, ndi ntchito yanga ngati? Si koma amene ali mu mpingo ndiwo muyenera kuŵaweruza? Ndi Mulungu amene amaweruza anthu akunjawo. Paja mau a Mulungu akuti, “Munthu woipayo mumchotse pakati panu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:3-5

Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene m'maso mwako momwe muli chimtengo? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:1-6

Ngati wina ali ndi mlandu ndi mkhristu mnzake, angathe bwanji kukauzengetsa kwa oweruza amene ali akunja, osati kwa akhristu anzake? mbala, aumbombo, zidakwa, augogodi, kapena achifwamba, ameneŵa sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu. Enanu munali otere kale, koma mudayeretsedwa, mudasanduka anthu a Mulungu, ndipo mudapezeka olungama pamaso pake. Zimenezi zidachitika m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndiponso mwa Mzimu wa Mulungu wathu. Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse. Chakudya, kwake nkuloŵa m'mimba, ndipo mimba, kwake nkulandira chakudya. Koma Mulungu adzaononga ziŵiri zonsezo. Thupi la munthu si lochitira dama, koma ndi la Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo mwiniwake thupilo. Mulungu adaukitsa Ambuye kwa akufa, ndipo mwa mphamvu yake adzatiwukitsa ifenso. Kodi inu simudziŵa kuti matupi anu ndi ziwalo za Khristu? Monga tsono ine nkutenga ziwalo za Khristu nkuzisandutsa ziwalo za mkazi wadama? Chosatheka! Kaya simudziŵa kuti munthu amene amadzipereka kwa mkazi wadama, iyeyo ndi mkaziyo amasanduka thupi limodzi? Paja Malembo akuti, “Aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.” Koma amene amadzipereka kwa Ambuye, iyeyo ndi Ambuye amakhala mzimu umodzi. Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe. Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu. Kodi simukudziŵa kuti tidzaweruza angelo? Nanji zinthu za moyo wapansipano? Tsono ngati muli ndi milandu pa zinthu zotere, bwanji mumaika anthu amene mpingo suŵayesa kanthu kuti aiweruze? Ndikunena zimenezi kuti ndikuchititseni manyazi. Kodi mwa inu palibe ndi mmodzi yemwe wanzeru, amene angathe kuweruza mlandu pakati pa akhristu anzake? Bwanji mkhristu akuimba mlandu mkhristu mnzake, mlanduwo nkuupereka kwa anthu akunja kuti auzenge?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:1

Tsono woweruza enawe, kaya ndiwe yani, ulibe pozembera. Pakutitu pamene ukuweruza mnzako, ukudzitsutsa wekha, popeza kuti iweyo woweruzawe umachita zokhazokhazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:29

M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:5

Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:7

Popeza kuti iwo adaapitirirabe kumufunsa, Yesu adaŵeramuka naŵauza kuti, “Pakati panupa amene sadachimwepo konse, ayambe ndiye kumponya mwala maiyu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:14-15

“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso. Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:26

Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:14

Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:17

Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:15

Munthu amene ali ndi Mzimu Woyera angathe kuzindikira khalidwe la zonse, ndipo palibe wina amene angathe kutsutsapo ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 7:24

Musamaweruza poyang'ana maonekedwe chabe, koma muziweruza molungama.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:15-16

Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu aliyense. Koma ndikati ndiweruze, ndimaweruza molungama, pakuti sindili ndekha ai, palinso Atate amene adandituma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:41-42

“Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Mbale wanga, taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene iweyo sukuchiwona chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 16:18-20

M'fuko lililonse mudzasankhe anthu oweruza ndiponso akuluakulu ena mu mzinda uliwonse umene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatseni. Anthu ameneŵa azidzaweruza anzao mosakondera. Asadzachite zinthu mopanda chilungamo kapena kuweruza milandu mokondera. Asadzalandire chiphuphu, chifukwa ziphuphu zimadetsa m'maso ngakhale anthu anzeru ndipo zimalakwitsa anthu olungama poweruza. Muzipereka nsembe za chikondwerero cha Paska kwa Chauta, Mulungu wanu. Muphe nkhosa kapena ng'ombe pa malo amene Chauta adzasankhule kuti anthu azidzapembedzerapo. Mukonde osati china ai, koma chilungamo chokha basi, kuti mudzalandiredi dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani ngati choloŵa chanu, ndi kukhazikikamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:6-7

“Ngati mmodzi mwa anthu ako osauka aimbidwa mlandu, umuweruze molungama ndithu. Ulewe zabodza, zosinjirira. Usaphe munthu wosalakwa ndi wosapalamula, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 1:16-17

Pa nthaŵi imene ija, ndidaŵalangiza aweruzi anuwo kuti, “Mumve milandu imene ili pakati pa anthu anu. Mlandu uliwonse muuweruze bwino, kaya ndi wa anthu a mtundu wanu, kapena wa alendo amene amakhala nao pakati panu. Musamakondere poweruza. Aliyense, munthu wamba kapena wamkulu, mumuweruze chimodzimodzi. Musamaopa wina aliyense, chifukwa chiweruzo chonse ndi cha Mulungu. Mlandu wina ukakulakani, mubwere nawo kwa ine, ndipo ndidzaugamula ndine.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:7

Ngodala anthu ochitira anzao chifundo, pakuti iwonso Mulungu adzaŵachitira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:20

Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:2

Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:13

Tsono tiyeni tileke kumaweruzana. Makamaka mutsimikize kuti musachite kanthu kalikonse kophunthwitsa mbale wanu, kapena komchimwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:13

Paja munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso Mulungu adzamuweruza mopanda chifundo. Koma wochita chifundo alibe chifukwa choopera chiweruzo cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36-37

Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula. Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:23-24

Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:12

Pali ena amene amadziyesa oyera mtima, koma sadachotse zoipa zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:13

Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:30

Paja tikumdziŵa kale amene adati, “Kulipsira nkwanga, ndidzakhaulitsa ndine.” Adatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:1

Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:20

Ndithudi, pa dziko lapansi palibe munthu amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:2

Ntchito zake za munthu zimakhala zolungama pamaso pake, koma Chauta amaweruza zamumtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:7

Tsono muzilandirana monga momwe Khristu adakulandirirani inu, kuti Mulungu alemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:11

Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:4

Ndachimwira Inu, Inu nokha, ndachita choipa pamaso panu. Motero mwakhoza ponditchula wolakwa, simudalakwe pogamula mlandu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:23

popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:10

Pajatu Mwana wa Munthu adabwera kudzafunafuna ndi kudzapulumutsa amene adatayika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:21-22

Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:15

Aŵa ndi mau otsimikizika, oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse, akuti Khristu Yesu adabwera pansi pano kuti adzapulumutse anthu ochimwa. Ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwa koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:12-13

Yesu atamva zimenezo, adaŵayankha kuti, “Anthu amene ali bwino sasoŵa sing'anga ai, koma amene akudwala. Kamvetsetseni tanthauzo la mau a Mulungu aja akuti, ‘Ndimafuna chifundo, osati nsembe ai.’ Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:3

Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:15

Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 130:3-4

Inu Chauta, mukadaŵerengera machimo, ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye? Koma inu mumakhululukira, nchifukwa chake timakulemekezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:3

Ngati munthu adziyesa kanthu, pamene chikhalirecho sali kanthu konse, amangodzinyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:16-17

Wina aliyense asakuzengeni mlandu pa nkhani yokhudza zakudya kapena zakumwa, kapena pa zokhudza masiku a chikondwerero, kapena a mwezi wokhala chatsopano, kapena pa zokhudza tsiku la Sabata. Zonsezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zenizeni zimene zilikudza, koma zenizenizo ndi Khristu amene.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:46-48

Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungalandire mphotho yanji? Kodi suja ngakhale okhometsa msonkho amachita chimodzimodzi? Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okha, mwachitapo chiyani pamenepo choposa ena? Kodi suja ngakhale akunja amachita chimodzimodzi? Nchifukwa chake monga Atate anu akumwamba ali abwino kotheratu, inunso mukhale abwino kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:35

Iyai, inu muzikonda adani anu, muzichita zabwino, ndipo muzikongoza osayembekeza kulandirapo kanthu. Mukatero mudzalandira mphotho yaikulu, ndiye kuti mudzakhala ana a Mulungu Wopambanazonse. Pajatu Iye amachitira zabwino anthu osayamika ndi oipa omwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:6

Koma amatikomera mtima koposa. Nchifukwa chake Malembo akuti, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma odzichepetsa amaŵakomera mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 43:1

Inu Mulungu, onetsani kuti ine ndine wosalakwa, munditchinjirize pa mlandu wanga kwa anthu osasamala za Mulungu. Mundipulumutse kwa anthu onyenga ndi opanda chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:19

Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:1

“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:6

Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:8

usafulumire kupita nazo ku bwalo lamilandu, chifukwa udzatani nanga pambuyo pake, ngati mnzako akuchititsa manyazi pokutsutsa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:8

Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:10

Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:2

Mundiyang'anitsitse, Inu Chauta, ndi kundiyesa. Muwone mtima wanga pamodzi ndi maganizo anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:15

koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:20

Iye sadzatsiriza bango lothyoka, nyale yofuka sadzaizimitsa, mpaka atapambanitsa chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:12

Tsono amene akuganiza kuti waimirira molimba, achenjere kuti angagwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:32

Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:2

Akutame ndi wina, osati pakamwa pako pomwe, wosadziŵana naye akakutamanda, apo ndipo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17

Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:24-25

Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto. Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:1-2

Usamavutika ndi anthu oipa. Usamakhumbira kukhala ngati ochita zoipa, Kanthaŵi pang'ono ndipo munthu woipa sadzakhalaponso, ngakhale muyang'ane bwino pamalo pamene analiri, simudzampezapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka. Munthu woipa amachitira upo mnzake wabwino, namamtuzulira maso mwachidani. Koma Chauta amamseka munthu woipayo, poti amaona kuti tsiku lake la kuwonongeka likubwera. Anthu oipa amasolola lupanga, ndipo amakoka mauta, kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa, amene amayenda molungama. Koma lupanga lao lidzalasa mitima ya eniake omwewo, ndipo mauta ao adzaŵathyokera m'manja. Nkwabwino kukhala m'chilungamo ndi kusauka, kupambana kukhala nazo zokoma zambiri zimene munthu woipa ali nazo. Pakuti Chauta adzathetsa mphamvu za anthu oipa, koma adzalimbikitsa anthu onse abwino. Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya. Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka. pakuti mosachedwa amanyala ngati udzu, ndipo amafota ngati masamba aaŵisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:12

Kuchita zoipa kumanyansa mafumu, pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:14

Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3-4

Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:104

Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:7

Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:17

Amene amayamba kufotokoza mlandu wake amaoneka ngati wokhoza ndiye, mpaka mnzake atabwera nadzamufunsitsa bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:17

Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Mulungu adzaŵaweruza onse, abwino ndi oipa omwe, pakuti adaika nthaŵi yochitikira chinthu chilichonse ndiponso ntchito iliyonse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:9

Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-13

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:4

Aliyense aziyesa yekha ntchito zake m'mene ziliri. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, osati chifukwa zapambana ntchito za mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:33-34

Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni. Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:23

Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:19-20

Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso. Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:50

Yesu adamuuza kuti, “Bwenzi langa, chita zimene wadzera.” Apo anthu aja adabwera namugwira Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:13

Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:4

Mphotho ya munthu wodzichepetsa ndi woopa Chauta, ndi chuma, ulemu ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:16

Nchifukwa chake kuyambira tsopano ife sitiganiziranso za munthu aliyense potsata nzeru za anthu chabe. Ngakhale kale tinkaganiza za Khristu potsata nzeru za anthu chabe, koma tsopano sitiganizanso za Iye motero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:5

Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:8

Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga, ndipo mwa ife mulibe choona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:15-16

Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:59

Ndikamalingalira njira zanga, ndimatembenuka kuti nditsate malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:5

Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:10-11

Tsono pamene Yesu ankadya m'nyumba, kudabwera anthu ambiri okhometsa msonkho, ndi anthu ochimwa, kudzadya nao ndi Yesuyo ndi ophunzira ake. Pamene Afarisi adaona zimenezi, adafunsa ophunzira a Yesu kuti, “Bwanji aphunzitsi anu akudya pamodzi ndi okhometsa msonkho ndiponso ndi anthu ochimwa?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:20

Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:1

Inu ana anga, ndikukulemberani zimenezi kuti musamachimwa. Komabe wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, ndiye Yesu Khristu amene ali wolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13

Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:18

Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:12

Chidani chimautsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:12

Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:7

Mukadadziŵa tanthauzo la mau a Mulungu aja akuti, ‘Ndimafuna chifundo, osati nsembe ai,’ sibwenzi mutaweruza kuti ndi olakwa anthu amene sadalakwe konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:1-2

Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha. Akutinso, “Inu anthu a mitundu ina, kondwani pamodzi ndi anthu ake a Mulungu.” Ndiponso akuti, “Inu nonse a mitundu ina, tamandani Ambuye, anthu a mitundu yonse amtamande.” Nayenso mneneri Yesaya akuti, “Mmodzi mwa zidzukulu za Yese adzabwera. Iye adzadzambatuka kuti alamule anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzaika chikhulupiriro chao pa Iyeyo.” Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana. Komabe m'kalata ino zina ndakulemberani mopanda mantha konse, kuti ndikukumbutseni zimenezo. Ndalemba motere popeza kuti Mulungu adandikomera mtima pakundipatula kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Adandipatsa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu ngati wansembe, kuti anthuwo akhale ngati nsembe yokomera Iye ndi yoperekedwa mwa Mzimu Woyera. Tsono pokhala ndine wake wa Khristu Yesu, ndikunyadira ntchito imene ndikugwirira Mulungu. Sindidzalimba mtima kulankhula za kanthu kena ai, koma zokhazo zimene ndimachita kudzera mwa Khristu, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kumvera. Zimenezi ndidazichita ndi mau anga ndi ntchito zanga, ndi zizindikiro ndi zozizwitsa zamphamvu zochitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Motero Uthenga Wabwino wonena za Khristu ndidaulalika kwathunthu ku Yerusalemu ndi ku dziko lozungulira mpaka ku Iliriko. Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:14

Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:3-5

Kunena za ine ndekha, ndilibe nazo kanthu ngati ndiweruzidwa ndi inu, kapenanso ndi bwalo lina lililonse la anthu. Ndiponsotu ngakhale mwiniwakene sindidziweruza ndekha ai. Ndilibe kanthu konditsutsa mumtima mwanga, komabe ngakhale chimenechi si chitsimikizo chakuti ndine wolungama. Ondiweruza ndi Ambuye basi. Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:3

Kuchita zolungama ndi zokhulupirika kumakondweretsa Chauta koposa kupereka nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:155

Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa, pakuti safunafuna malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:1-2

Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye. M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse. Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu. Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika. Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Mulungu ndi wokhulupirika ndipo chikondi chake chachikulu chimakhala kosatha, nthawi zonse wawonetsa chifundo chake kwa ana ake onse ndipo malonjezo ake sazengereza kuwakwaniritsa. Ndimalemekeza dzina la Wamphamvuyonse ndipo moyo wanga umamutambasira, pamaso pake pali chisangalalo chokwanira, ndimalowa molimba mtima m'malo anu opatulika ndipo ndimagwadira mapazi anu kuti ndikupatseni ulemerero wonse, inu nokha Ambuye wanga ndinu woyenera, chifukwa ndinu wangwiro ndi wolungama pa zonse zomwe mumachita, chifukwa njira zanu ndi zolungama ndipo mulibe kuipa kapena chinyengo, ndimapembedza iye amene wakhala pampando wachifumu, maso ake ali pa chilengedwe chonse ndipo iye ndiye woweruza dziko lonse lapansi, iye yekha ndiye angaweruze komanso kupulumutsa, palibe wina wofanana ndi Mulungu wanga, pamaso pake mdima umathawira, iye ndi Yehova woopsa ndi wosagonjetseka, ndimakhulupirira ziweruzo zanu zolungama, inu ndinu wanzeru Ambuye ndipo palibe wina woposa inu kukhala woweruza padziko lapansi, landirani ulemerero ndipo ulemu wonse ukhale kwa inu, m'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa