Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


110 Mau a m'Baibulo a Chiweruzo Chomaliza

110 Mau a m'Baibulo a Chiweruzo Chomaliza

Ndikuwuza iwe mnzanga, Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, adzatiweruza tonse. Baibulo limatiuza kuti tidzaweruzidwa malinga ndi zochita zathu. Bukhu la Chivumbulutso 20:12 limati: “Ndipo ndinaona akufa, ang’onoang’ono ndi akuluakulu, ali chilili pamaso pa mpando wachifumu, ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo buku la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa monga mwa zolembedwa m’mabukumo, monga mwa ntchito zawo.”

Aliyense wosakhulupirira adzaweruzidwa ndi Khristu ndi kulandira chilango choyenera machimo ake. Malemba amatsimikizira izi. Aroma 2:5 imatiuza momveka bwino kuti osakhulupirira akusunga mkwiyo wa Mulungu pa iwo eni: “Koma chifukwa cha kuuma mtima kwako, ndi mtima wosalapa, ukudzisonkhanitsira wekha mkwiyo tsiku la mkwiyo ndi la kuwululidwa kwa chiweruzo cholungama cha Mulungu.”




Mateyu 12:36

Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:27

Munthu aliyense amafa kamodzi kokha, pambuyo pake nkumaweruzidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:16

Monga unenera Uthenga Wabwino umene ndimalalika, zidzateronso pa tsiku lija limene Mulungu mwa Khristu Yesu adzaweruza zinsinsi za m'mitima mwa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:6

Mukumbukire angelo amene sadakhutire ndi ulamuliro wao, koma adasiya malo amene Mulungu adaaŵapatsa. Mulungu adaŵamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuŵasunga m'malo amdima mpaka tsiku lalikulu lija pamene adzaŵaweruza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:30

Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:41-42

Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake kudzachotsa mu Ufumu wake anthu onse ochimwitsa anzao, ndi ena onse ochita zoipa, nadzaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:12

Chopetera chake chili m'manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m'nkhokwe, koma mankhusu adzaŵatentha m'moto wosazimika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:31-32

“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera ndi ulemerero wake, pamodzi ndi angelo onse, adzachita kukhalira pa mpando wake wachifumu. Adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse pamaso pake, ndipo adzaŵalekanitsa monga momwe mbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:4

Pakuti Mulungu sadaŵalekerere angelo amene adachimwa aja, koma adaŵaponya m'ng'anjo yamoto, m'maenje amdima momwe ali omangidwa kudikira chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:17

Nthaŵi ndiye yafika yoti Mulungu ayambe kuweruza anthu ake. Tsono ngati chiweruzocho chiyambira pa ife, nanga podzafika pa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, ndiye kuti chidzakhala chotani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:15

Ndithu ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga mudzi wa Sodomu ndi wa Gomora, koma osati polanga mudzi umenewo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:31

Chifukwa adaika tsiku pamene Iye adzaweruza anthu a pa dziko lonse lapansi molungama kudzera mwa Munthu amene Iye adamsankha. Adatsimikizira anthu onse zimenezi pakuukitsa Munthuyo kwa akufa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:10-12

Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze. Paja Malembo akunena kuti, “Ambuye akuti, ‘Pali Ine ndemwe, anthu onse adzandigwadira ndi kuvomereza kuti ndine Mulungu.’ ” Motero aliyense mwa ife adzadzifotokozera yekha kwa Mulungu zimene adazichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:11-15

Pambuyo pake ndidaona mpando wachifumu woyera, waukulu, ndiponso amene amakhalapo. Dziko lapansi ndi thambo zidathaŵa pamaso pake, ndipo sizidapezekenso konse. Ndidaonanso anthu akufa, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja, ndipo mabuku adafutukulidwa. Adafutukula buku linanso, limene lili buku la amoyo. Tsono anthu akufawo adaweruzidwa poyang'anira ntchito zao monga momwe zidaalembedwera m'mabukumo. Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake. Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zidaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri. Aliyense wopezeka kuti dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo lija, adaponyedwa m'nyanja yamotoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:10

Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:21-23

“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna. Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’ Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:8

Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 96:13

pamaso pa Chauta, pamene zabwera kudzalamulira dziko lapansi. Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo, adzalamulira anthu a mitundu yonse moona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36-37

Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula. Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7-8

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:17

Mulungu alibe tsankho. Amaweruza aliyense molingana ndi zochita zake. Ngati mumutcha Atate pamene mukupemphera, mchitireni ulemu nthaŵi yonse muli alendo pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 12:14

Pajatu Mulungu adzaweruza zonse zimene timachita, zabwino kapena zoipa, ngakhale ndi zam'chinsinsi zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:46

Pamenepo iwowo adzachoka kumapita ku chilango chosatha, olungama aja nkumapita ku moyo wosatha.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:12

Yesu akuti, “Mvetsetsani, ndikubwera posachedwa. Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense molingana ndi zimene adachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:13-15

Koma ntchito za munthu aliyense zidzaonekera poyera, pamene tsiku la chiweruzo lidzaziwonetsa. Pakuti tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito za munthu aliyense. Zimene munthu adamanga pamazikopo zikadzakhalapobe, mwiniwakeyo adzalandira mphotho. Koma zikadzanyeka ndi moto, sadzalandira mphotho. Inde mwiniwakeyo adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wangopulumuka m'moto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:7-8

Koma Chauta amakhala pa mpando wake waufumu nthaŵi zonse, adakhazika mpando wake kuti aziweruza. Iye amaweruza dziko lapansi molungama, amagamula milandu ya anthu mosakondera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:5-6

Koma chifukwa ndiwe wa mtima wokanika ndi wosafuna kutembenuka, ukudzisungira chilango cha Mulungu. Chilangocho chidzakugwera pa tsiku limene adzaonetse mkwiyo wake ndiponso kuweruza kwake kolungama. Iye adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:36-44

“Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa; amadziŵa ndi Atate okha basi. Kudza kwa Mwana wa Munthu kudzakhala monga momwe zinthu zidaayendera pa nthaŵi ya Nowa. Masiku amenewo, chisanafike chigumula, anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Sadazindikire kanthu mpaka chigumula chidafika nkuŵaononga onse. Zidzateronso pamene Mwana wa Munthu adzabwera. Yesu adaŵayankha kuti, “Chenjerani kuti wina aliyense asadzakusokezeni. Pa nthaŵi imeneyo anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. Azimai aŵiri adzakhala akusinja, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. “Nanunso tsono, khalani maso, chifukwa simudziŵa tsiku limene Ambuye anu adzabwere. Koma dziŵani kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi yofika mbala, bwenzi atakhala maso, osalola kuti mbala imuthyolere nyumba. Choncho inunso muzikhala okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene inu simukuyembekeza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:19-31

“Panali munthu wina wachuma, amene ankavala zovala zamtengowapatali, ndipo ankasangalala ndi kudyerera masiku onse. Tsono mbuye wakeyo adamuitana, namufunsa kuti, ‘Nchiyani chimene ndikumva za iwe? Undifotokozere za ukapitao wako, pakuti sungakhalenso kapitao ai.’ Panalinso munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadzagona pa khomo la munthu wachuma uja. Iyeyu anali ndi zilonda m'thupi lonse. Ankalakalaka kudya nyenyeswa zimene zinkagwa pansi kuchokera pa tebulo la wachuma uja. Koma si pokhapo, ngakhale agalu ankabwera kumadzanyambita zilonda zake. “Munthu wosauka uja adamwalira, angelo nkumunyamula, nakamtula m'manja mwa Abrahamu. Munthu wachuma uja nayenso adamwalira, naikidwa m'manda. Pamene ankazunzika ku Malo a anthu akufa, wachuma uja adayang'ana kumwamba naona Abrahamu ali patali, ndi Lazaro ali pambali pakepa. Pamenepo adanena mokweza mau kuti, ‘Atate Abrahamu, mundichitire chifundo. Tumani Lazaro aviike nsonga ya chala chake m'madzi kuti adzaziziritseko lilime langa, pakuti ndikuzunzika koopsa m'moto muno.’ Koma Abrahamu adati, ‘Mwana wanga, kumbukira kuti udalaandiriratu zokondweretsa ukadali ndi moyo, pamene Lazaro adaalandira zoŵaŵa. Koma tsopano iye akusangalala kuno, pamene iwe ukuzunzika kwambiri. Ndiponso pakati pa ife ndi inu pali chiphompho, kotero kuti ofuna kuchoka kuno kuwolokera kwanuko, sangathe ai. Chimodzimodzinso kuchoka kwanuko kuwolokera kuno.’ “Apo wachuma uja adati, ‘Ndipotu ndikukupemphani atate, kuti mumtume Lazaroyo apite ku nyumba ya bambo wanga. Kumeneko ndili ndi abale anga asanu. Akaŵachenjeze, kuwopa kuti iwonso angabwere ku malo ano amazunzo.’ Koma Abrahamu adati, ‘Iwo ali ndi mabuku a Mose ndi a aneneri. Amvere zam'menemo.’ Apo kapitaoyo adayamba kuganiza mumtima mwake kuti, ‘Ndichite chiyani, popeza kuti mbuye wanga akundilanda ukapitao? Kulima, ai, ndilibe mphamvu. Kupemphapempha, ainso, kukundichititsa manyazi. Iye adati, ‘Iyai, atate Abrahamu, koma wina atauka kwa akufa nkupita kwa iwo, apo adzatembenuka mtima.’ Koma Abrahamu adamuuza kuti, ‘Ngatitu iwo samvera Mose ndi aneneri, sangathekenso ngakhale wina auke kwa akufa.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:12

chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:15-16

“Pajatu Chauta adzabwera ndi moto. Ndipo magaleta ake adzafika ngati mkuntho. Iye adzaonetsa poyera ukali wake, ndipo adzalanga adani ake ndi malaŵi a moto. Adzalanga anthu onse a pa dziko lapansi ndi moto ndi lupanga. Alipo ambiri amene Chauta adzaŵapha.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:10-11

Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikulo zakumwamba zidzatha ndi phokoso loopsa. Zinthu zonse zidzayaka moto nkusungunuka, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili m'menemo zidzapseratu. Popeza kuti zonsezi zidzasungunuka motero, nanga simuyenera kukhala anthu angwiro m'makhalidwe anu ndiponso osamala za Mulungu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:17

Pamene chikondi chafikira pake penipeni mwa ife ndi apa pakuti moyo wathu pansi pano uli wonga moyo wa Khristu, kotero kuti tingathe kukhala olimba mtima pa tsiku la chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1-2

Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu. Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufaŵa. Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake. Pakuti ngati m'moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo. Onse amene Mzimu wa Mulungu amaŵatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!” Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye. Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno. Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera. Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 75:7-8

Koma ndi Mulungu yekha amene amagamula milandu, amatsitsa wina, nakweza wina. M'manja mwa Chauta mulitu chikho cha vinyo wofanizira chilango chake, vinyo wotutuma ndi wothirako dzoŵaŵa. Adzatsanyula vinyoyo, ndipo oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa, nadzagugudiza mpaka ndungundungu zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:27

Ndipotu Mwana wa Munthu adzabwera ndi angelo ake ali ndi ulemerero wa Atate ake. Pamenepo adzabwezera aliyense molingana ndi zochita zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:27

Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:2

Tikudziŵa kuti Mulungu salakwa akamaweruza anthu ochita zotere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:12

Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:14-30

“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake. Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adapita nakachita nazo malonda nkupindula ndalama zinanso zisanu. Chimodzimodzinso amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adapindula ndalama zinanso ziŵiri. Koma amene adaalandira ndalama imodzi uja, adapita nakaikumbira pansi ndalama ya mbuye wake ija. “Patapita nthaŵi yaitali, mbuye wao uja adabwerako naŵaitana antchito ake aja kuti amufotokozere za zimene adaachita ndi ndalama zija. Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ Nayenso wantchito amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adabwera nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama ziŵiri. Onani, ndidapindula ziŵiri zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ “Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu. Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu? Tsonotu udaayenera kukaiika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake. Mlandeni ndalamayi, muipereke kwa amene ali ndi ndalama khumiyo. Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera. Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:8

Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:23

Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:19

Onse amene ndimaŵakonda, ndimaŵadzudzula ndi kuŵalanga motero. Tsono chitani khama, mutembenuke mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:32

Adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse pamaso pake, ndipo adzaŵalekanitsa monga momwe mbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:5

Nchifukwa chake anthu ochimwa, Mulungu adzaŵazenga mlandu, adzaŵachotsa iwo pakati pa anthu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:5

Koma iwo adzayenera kufotokoza okha mlandu wao kwa Mulungu amene ali wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:30-31

Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka ku thambo. Anthu a mitundu yonse ya pansi pano adzayamba kulira, ndipo adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Kudzamveka lipenga lamphamvu, ndipo Iye adzatuma angelo ake, kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:48

Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:75

Inu Chauta, ndikudziŵa kuti kuweruza kwanu nkolungama, ndipo mwandilanga potsata kukhulupirika kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:10

Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:8-9

Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira. Masautso ndi zoŵaŵa zidzaŵagwera onse ochita zoipa, poyamba Ayuda, kenaka anthu a mitundu ina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:16

Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:40

Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:51-52

Mvetsetsani, ndikuuzeni chinsinsi. Sikuti tonse tidzamwalira, komabe tonse tidzasandulika. Zidzachitika mwadzidzidzi, pa kamphindi ngati kuphethira kwa diso, pamene lipenga lotsiriza lidzalira. Likadzaliratu lipengalo, akufa adzauka ndi matupi amene sangaole, ndipo ife tidzasandulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:20-21

Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu. Iyeyo adzasandutsa matupi athu achabeŵa kuti akhale ofanafana ndi thupi lake laulemerero. Adzachita zimenezi ndi mphamvu zake zomwe zija zimene angathenso kugonjetsa nazo zinthu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:6

Zamumlengalenga zikulalika chilungamo cha Mulungu, pakuti Iye mwini ndiye muweruzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17-19

Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka. Aliyense wotumikira Khristu motere, amakondweretsa Mulungu, ndipo amakhala wovomerezeka kwa anthu. Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:28

Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 98:9

pamene Chauta akufika, popeza kuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo, adzaweruza mitundu yonse mosakondera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:20

Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti ngati kukhulupirika kwanu sikuposa kukhulupirika kwa aphunzitsi a Malamulo ndi kwa Afarisi, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:24

“Akamachoka, adzaona mitembo ya anthu amene adandipandukira. Mphutsi zimene zidzaŵadya sizidzafa, ndipo moto umene udzaŵatentha sudzazima. Anthu a mitundu yonse poŵaona adzanyansidwa nawo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:1

Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziŵa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:12-27

Adati, “Munthu wina, wa fuko lomveka, adapita ku dziko lakutali kukalandira ufumu kuti pambuyo pake abwerenso kwao. Adaitana khumi mwa antchito ake naŵapatsa ndalama zasiliva khumi, aliyense yakeyake. Adaŵauza kuti, ‘Bachita nazoni malonda mpaka nditabwera.’ Koma anthu ake ankadana naye, choncho m'mbuyo muno adatuma nthumwi kuti zipite ku dziko lomwelo nkukanena kuti, ‘Ife sitikufuna konse kuti munthu ameneyu akhale mfumu yathu.’ “Komabe iye adalandira ufumu uja. Tsono atabwerera kwao, adaitanitsa antchito aja adaaŵapatsa ndalamaŵa kuti adziŵe zimene adapindula. Woyamba adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi khumi.’ Mbuye wake adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zochepa kwambiri, udzalamulira midzi khumi.’ Wachiŵiri adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi asanu.’ Iyenso mbuye wake adamuuza kuti, ‘Iwe udzalamulira midzi isanu.’ Kudafika munthu wina, dzina lake Zakeyo. Iyeyo anali mkulu wa okhometsa msonkho, ndipo anali wolemera. Koma wina adadza nati, ‘Ambuye, nayi ndalama yanu ija. Ndidaaimanga pa kansalu. Ndinkakuwopani, popeza kuti ndinu munthu wankhwidzi. Mumalonjerera zimene simudaikize, ndiponso mumakolola zimene simudabzale.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa, ndikutsutsa ndi mau ako omwe. Kani unkadziŵa kuti ndine munthu wankhwidzi, amene ndimalonjerera zimene sindidaikize, ndipo ndimakolola zimene sindidabzale. Nanga bwanji osaiika ku banki ndalama yangayo, kuti ine pobwera ndiilandire pamodzi ndi chiwongoladzanja chake?’ Atatero adauza anthu amene anali pomwepo kuti, ‘Mlandeni ndalamayi muipereke kwa amene ali ndi ndalama makumi khumiyo.’ “Iwo adamuyankha kuti, ‘Pepani, ambuye, ameneyu ali kale ndi ndalama makumi khumi.’ Koma iye adati, ‘Ndikunenetsa kuti aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. Koma adani angaŵa, aja ankakana kuti ndikhale mfumu yaoŵa, bwera nawoni kuno, muŵaphe ine ndikuwona.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:18-20

Mkwiyo wa Mulungu ukuwoneka kuchokera Kumwamba. Amakwiyira anthu chifukwa cha kusalungama kwao konse ndi kusamchitira ulemu. Kusalungama kwaoko kumaŵalepheretsa kudziŵa zoona. Mulungu amaŵakwiyira, chifukwa zimene munthu angathe kudziŵa zokhudza Mulungu iwo akuzidziŵa bwino lomwe, popeza kuti Mulungu mwini ndiye adaŵaululira zimenezi. Uthengawu Iye adaulonjeza kale kudzera mwa aneneri ake ndipo udalembedwa m'Malembo Oyera. Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:27

Anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Chauta, mabanja a mitundu ina ya anthu adzampembedza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:13-14

“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:27

Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:10

Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:6

Kulungama kwanu kumaonekera ngati mapiri aatali, kuweruza kwanu nkozama ngati nyanja yakuya, Inu Chauta, mumasamalira anthu ndi nyama zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:12

Chauta Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku, pamene adzatsitsa onse onyada ndi odzitama, ndipo adzagonjetsa onse amphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:1

Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza anthu onse, amoyo ndi akufa omwe, ndipo potamanda kubwera kwake ndi ufumu wake wa Khristuyo ndikukulamula ndithu kuti

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:28

Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:14-15

Kodi anthu angatame Mulungu bwanji mopemba ngati sadamkhulupirire? Ndipo angamkhulupirire bwanji ngati sadamve za Iye? Ndipo angamve za Iye bwanji ngati palibe wina wolalika? Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:137-138

Ndinu olungama Chauta, ndipo kuweruza kwanu nkolungama. Malamulo amene mwatipatsa, ndi olungama ndi okhulupirika ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:10

Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:16

Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:15

Aliyense wopezeka kuti dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo lija, adaponyedwa m'nyanja yamotoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 49:14-15

Ayenera kupita ku dziko la akufa ngati nkhosa, ndipo imfa idzakhala mbusa wao. Anthu olungama adzaŵapambana. Adzatsika kulunjika ku manda, matupi ao adzaola, kwao kudzakhala kumanda. Koma Mulungu adzaombola moyo wanga ku ulamuliro wa manda, sindidzaopa, pakuti Iye adzandilandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:25

Mvetsetsani, Ine ndiye ndakuuziranitu zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:4-5

Kodi kapena ukupeputsa chifundo chachikulu cha Mulungu, kuleza mtima kwake, ndi kupirira kwake? Kodi sukudziŵa kuti Mulungu akukuchitira chifundo chifukwa afuna kuti utembenuke mtima? Koma chifukwa ndiwe wa mtima wokanika ndi wosafuna kutembenuka, ukudzisungira chilango cha Mulungu. Chilangocho chidzakugwera pa tsiku limene adzaonetse mkwiyo wake ndiponso kuweruza kwake kolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:9

Ndithu m'mitima mwathu tinkangoganiza kuti basi talandira chilango chokaphedwa. Zimenezi zidachitika kuti tisamadzikhulupirire, koma kuti tizikhulupirira Mulungu amene amaukitsa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:11

Atatha mazunzo akewo, adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzasenza machimo a anthu onse kuti iwo ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:9

Pajatu anthu oipa adzaonongeka, koma okhulupirira Chauta adzalandira dziko kuti likhale lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:49-50

Zidzateronso pa kutha kwa dziko lino lapansi. Angelo adzabwera nadzachotsa anthu ochimwa pakati pa anthu olungama, Mbeu zina zidagwera pa nthaka yamiyala, pamene panalibe dothi lambiri. Zidamera msanga chifukwa nthakayo inali yosazama. nkumaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:15

Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:32

Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:31

Kugwa m'manja mwa Mulungu wamoyo ndi chinthu choopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:1-2

“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Kapena atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha? Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa. “Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka. “Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa. Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu? Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai. Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto. M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:25

Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake kapena kuuwononga?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:13

Paja chikondi chanu chosasinthika kwa ine nchachikulu, Mwandipulumutsa ku malo akuya a anthu akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:7

Musakumbukire machimo a unyamata wanga ndi mphulupulu zanga. Koma mundikomere mtima, Inu Chauta, chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:11-12

Popeza kuti zonsezi zidzasungunuka motero, nanga simuyenera kukhala anthu angwiro m'makhalidwe anu ndiponso osamala za Mulungu? Muziyembekeza tsiku la Ambuye ndi kugwira ntchito zofulumizitsa kudza kwake. Pa tsikulo zakumwamba zidzayaka moto ndi kusungunuka, ndipo zinthu zonse nazonso zidzasungunukira m'motomo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:28

Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu akadzakonzanso zinthu zonse, Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake wachifumu ndi waulemerero. Tsono inunso amene mudanditsatanu, mudzakhala pa mipando yachifumu khumi ndi iŵiri mukuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:12-13

Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake. Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 24:21-22

Tsiku limenelo Chauta adzalanga kumwamba zamphamvu zakumwamba, ndipo pansi pano mafumu a pansi pano. Mulungu adzasonkhanitsa mafumu onse pamodzi, ngati am'ndende amene ali m'dzenje. Adzaŵatsekera m'ndende, ndipo patapita nthaŵi yaitali, adzalangidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:41-43

Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake kudzachotsa mu Ufumu wake anthu onse ochimwitsa anzao, ndi ena onse ochita zoipa, nadzaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano. Tsono anthu olungama adzaŵala ngati dzuŵa mu Ufumu wa Atate ao. Amene ali ndi makutu, amve!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:4

Mfumu idzateteza anthu osauka, idzapulumutsa anthu osoŵa, koma idzaononga anthu ozunza anzao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 3:13

Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:34-35

Motero mbuye wakeyo adapsa mtima kwambiri, nampereka kuti akamzunze mpaka atabweza ngongole yonse ija. “Inunsotu Atate anga akumwamba adzakuchitani zomwezo, aliyense mwa inu akapanda kukhululukira mbale wake ndi mtima wonse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:27-28

Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino, osalola kuti adani anu azikuwopsezani pa kanthu kalikonse. Zimenezi zidzaŵatsimikizira kuti iwowo adzaonongeka, koma inu mudzapulumuka. Mulungu ndiye amene adzakuchitirani zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, ndinu Alfa ndi Omega! Atate, Mlengi wa thambo ndi dziko lapansi, ndinu woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi chimaliziro. Mulungu wa ulemerero, m'dzina la Yesu, ndikupemphani kuti mundikonzekere nthawi yomwe ndidzayankha zonse zomwe ndachita ndi zomwe ndalankhula pamene ndinali ndi moyo. Ikani mwa ine, Ambuye, chikhumbo ndi ludzu lofuna kukhala pafupi nanu ndi kuwerenga Mawu anu kuti ndikhale woyera ndi wopanda banga pamene ndidzaima pamaso panu pa chiweruzo chomaliza. Mundipange mwana wanu wakhama ndi wodalirika pa nkhani ya chipulumutso changa, kuti moyo wanga ukhale onunkhira bwino pamaso panu ndipo mapazi anga atsogoleredwe ndi mawu anu. Ndikumvetsa, Atate, kuti ndikufunika kukonzedwanso ndi kusinthidwa kuti ndikapereke umboni padziko lapansi ndi kukhala wokonzeka kukhala kumwamba. Mawu anu amati: "Pakuti nthawi yakwana kuti chiweruzo chiyambe pa nyumba ya Mulungu; ndipo ngati chiyamba pa ife choyamba, chitsiriziro chake chidzakhala chotani kwa iwo amene samvera Uthenga Wabwino wa Mulungu?". Ndithandizeni kukuyembekezerani tsiku lililonse, Yesu, ndi lingaliro lakuti munabwera dzulo ndipo mudzabweranso mawa kuti umbombo ndi chisiriro zisandisokeretse. Musalole, Ambuye, kuti zonyansa, kuipitsidwa kapena kudzikuza kundichotse pamaso panu. Ndithandizeni kuti nthawi zonse ndikhale pa ubwenzi wolimba nanu ndi kukhala nthawi yabwino pamaso panu, ndikudikira ndi kusala nthawi zonse. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa