Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


110 Mau a m'Baibulo a Chiweruzo Chomaliza

110 Mau a m'Baibulo a Chiweruzo Chomaliza

Ndikuwuza iwe mnzanga, Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, adzatiweruza tonse. Baibulo limatiuza kuti tidzaweruzidwa malinga ndi zochita zathu. Bukhu la Chivumbulutso 20:12 limati: “Ndipo ndinaona akufa, ang’onoang’ono ndi akuluakulu, ali chilili pamaso pa mpando wachifumu, ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo buku la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa monga mwa zolembedwa m’mabukumo, monga mwa ntchito zawo.”

Aliyense wosakhulupirira adzaweruzidwa ndi Khristu ndi kulandira chilango choyenera machimo ake. Malemba amatsimikizira izi. Aroma 2:5 imatiuza momveka bwino kuti osakhulupirira akusunga mkwiyo wa Mulungu pa iwo eni: “Koma chifukwa cha kuuma mtima kwako, ndi mtima wosalapa, ukudzisonkhanitsira wekha mkwiyo tsiku la mkwiyo ndi la kuwululidwa kwa chiweruzo cholungama cha Mulungu.”




Mateyu 12:36

Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:27

Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:16

tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 7:26

Koma woweruza mlandu adzakhalako, ndipo adzachotsa ulamuliro wake, kuutha ndi kuuononga kufikira chimaliziro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:6

Angelonso amene sanasunga chikhalidwe chao choyamba, komatu anasiya pokhala paopao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:30

Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:41-42

Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika, ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:12

chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:31-32

Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:4

Pakuti ngati Mulungu sanalekerera angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika kumaenje a mdima, asungike akaweruzidwe;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:17

Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:15

Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mudzi umenewo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:31

chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:10-12

Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira kumpando wakuweruza wa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malilime onse adzavomereza Mulungu. Chotero munthu aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:11-15

Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwa malo ao. Ndipo ndinaona akufa, akulu ndi ang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao. Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi dziko la akufa zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake. Ndipo imfa ndi dziko la akufa zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto. Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:10

Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:21-23

Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:8

Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 96:13

Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36-37

Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7-8

Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:17

Ndipo mukamuitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 12:14

Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:46

Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:12

Taonani, ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndili nayo yakupatsa yense monga mwa ntchito yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:13-15

ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani. Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho. Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:7-8

Koma Yehova akhala chikhalire, anakonzeratu mpando wachifumu wake kuti aweruze. Ndipo Iyeyu adzaweruza dziko lapansi m'chilungamo, nadzaweruza anthu molunjika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:5-6

Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu; amene adzabwezera munthu aliyense kolingana ndi ntchito zake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:36-44

Koma za tsiku ili ndi nthawi yake sadziwa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha. Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu. Pakuti monga m'masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'chingalawa, Ndipo iwo sanadziwe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu. Pomwepo adzakhala awiri m'munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa: awiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake lakufika Ambuye wanu. Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe. Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthawi m'mene simuganizira, Mwana wa Munthu adzadza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:19-31

Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; Ndipo anamuitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao. ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake. Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda. Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake. Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto. Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kuchokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso. Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume kunyumba ya atate wanga; pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo. Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo. Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwake, Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitao? Kulima ndilibe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi. Koma anati, Iai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa kufa adzasandulika mtima. Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:12

Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:15-16

Pakuti taonani, Yehova adzafika m'moto, ndi magaleta ake adzafanana ndi kamvulumvulu; kubwezera mkwiyo wake ndi ukali, ndi kudzudzula ndi malawi amoto. Pakuti Yehova adzatsutsana ndi moto, ndi lupanga lake, ndi anthu onse; ndi ophedwa a Yehova adzakhala ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:10-11

Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa. Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m'mayendedwe opatulika ndi m'chipembedzo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:17

M'menemo chikondi chathu chikhala changwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tili ife m'dziko lino lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1-2

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa. Ndipo ngati Khristu akhala mwa inu, thupilo ndithu lili lakufa chifukwa cha uchimo; koma mzimu uli wamoyo chifukwa cha chilungamo. Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu. Chifukwa chake, abale, ife tili amangawa si ake a thupi ai, kukhala ndi moyo monga mwa thupi; pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo. Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu. Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate! Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye. Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife. Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 75:7-8

Pakuti Mulungu ndiye woweruza; achepsa wina, nakuza wina. Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho; ndi vinyo wake achita thovu; chidzala ndi zosanganizira, ndipo atsanulako. Indedi, oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa nadzagugudiza nsenga zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:27

Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:27

koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:2

Ndipo tidziwa kuti kuweruza kwa Mulungu kuli koona pa iwo akuchita zotere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:12

Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:14-30

Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake. Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye. Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu. Chimodzimodzi uyo wa awiriwo, anapindulapo ena awiri. Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa talente ya mbuye wake. Ndipo itapita nthawi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo wa matalente awiriwo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine matalente awiri; onani, ndapindulapo matalente ena awiri. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo uyonso amene analandira talente imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafesa, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaza; ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi talente yanu: onani, siyi talente yanuyo. Koma mbuye wake anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafesa, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaza; chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake. Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi. Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho. Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengeranso mafuta; Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:8

podziwa kuti chinthu chokoma chilichonse yense achichita, adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:23

Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:19

Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:32

ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:5

Chifukwa chake oipa sadzaimirira pa mlanduwo, kapena ochimwa mu msonkhano wa olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:5

amenewo adzamwerengera Iye wokhala wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:30-31

ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 12:2-3

Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha. Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:48

Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:75

Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova, ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu. kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:10

Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:8-9

koma kwa iwo andeu, ndi osamvera choonadi, koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza, nsautso ndi kuwawa mtima, kwa moyo wa munthu aliyense wakuchita zoipa, kuyambira Myuda, komanso Mgriki;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:16

Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:40

Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:51-52

Taonani, ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika, m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:20-21

Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu; amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:6

Ndipo zakumwamba zionetsera chilungamo chake; pakuti Mulungu mwini wake ndiye woweruza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17-19

Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera. Pakuti iye amene atumikira Khristu mu izi akondweretsa Mulungu, navomerezeka ndi anthu. Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:28

kotero Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 98:9

Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:20

Pakuti ndinena ndi inu, ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:24

Ndipo iwo adzatuluka ndi kuyang'ana mitembo ya anthu amene andilakwira Ine, pakuti mphutsi yao sidzafa, pena moto wao sudzazimidwa; ndipo iwo adzanyansa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:1

Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, m'Mwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:12-27

Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka ananka kudziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako. Ndipo anaitana akapolo ake khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi za mina, nati kwaiwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso. Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nizituma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu. Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pochita malonda. Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye, mina yanu inachita nionjeza mina khumi. Ndipo anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'chaching'onong'ono, khala nao ulamuliro pa midzi khumi. Ndipo anadza wachiwiri, nanena, Mbuye, mina yanu yapindula mina zisanu. Ndipo anati kwa iyenso, Khala iwenso woweruza midzi isanu. Ndipo taonani, mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyo; ndipo iye anali mkulu wa amisonkho, nali wachuma. Ndipo wina anadza, nanena, Mbuye, taonani, siyi mina yanu, ndaisunga m'kansalu; pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula chimene simunachiika pansi, mututa chimene simunachifesa. Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiika, ndi wotuta chimene sindinachifesa; ndipo sunapereka bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadaitenga ndi phindu lake? Ndipo anati kwa iwo akuimirirapo, Mchotsereni minayo, nimuipatse kwa iye wakukhala nazo mina khumi. Ndipo anati kwa iye, Mbuye, ali nazo mina khumi. Ndinena ndi inu, kuti kwa yense wakukhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa. Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:18-20

Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera Kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi m'chosalungama chao; chifukwa chodziwika cha Mulungu chaonekera m'kati mwao; pakuti Mulungu anachionetsera kwa iwo. umene Iye analonjeza kale ndi mau a aneneri ake m'malembo oyera, Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:27

Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:13-14

Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:27

ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:10

Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira kumpando wakuweruza wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:6

Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:12

Chifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:1

Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ake ndi ufumu wake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:28

Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m'Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:14-15

Ndipo iwo adzaitana bwanji pa Iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji Iye amene sanamva za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:137-138

Inu ndinu wolungama, Yehova, ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika. Mboni zanuzo mudazilamulira zili zolungama ndi zokhulupirika ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:10

pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:16

Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:15

Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 49:14-15

Aikidwa m'manda ngati nkhosa; mbusa wao ndi imfa. Ndipo m'mawa mwake oongoka mtima adzakhala mafumu ao; ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda, kuti pokhala pake padzasowa. Koma Mulungu adzaombola moyo wanga kumphamvu ya manda. Pakuti adzandilandira ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:25

Chifukwa chake akanena kwa inu, Onani, Iye ali m'chipululu; musamukeko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:4-5

Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape? Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:9

koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:11

Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:9

Pakuti ochita zoipa adzadulidwa; koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:49-50

Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino, Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhala nalo dothi lakuya. Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera; nadzawataya m'ng'anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:15

Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:32

amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:31

Kugwa m'manja a Mulungu wamoyo nkoopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:1-2

Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri. Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka. Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:25

Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:13

Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:7

Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:11-12

Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m'mayendedwe opatulika ndi m'chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, m'menemo miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam'mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:28

Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:12-13

Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake: ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 24:21-22

Ndipo padzali tsiku limenelo, kuti Yehova adzazonda kumwamba khamu lakumwamba, ndi mafumu a dziko lapansi. Ndipo iwo adzasonkhanitsidwa pamodzi, monga ndende zimasonkhanitsidwa m'dzenje, ndi kutsekeredwa m'kaidi, ndipo atapita masiku ambiri adzawazonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:41-43

Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika, ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:4

Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 3:13

komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:34-35

Ndipo mbuye wake anakwiya, nampereka kwa azunzi, kufikira akambwezere iye mangawa onse. Chomwechonso Atate wanga a Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:27-28

Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino; osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, ndinu Alfa ndi Omega! Atate, Mlengi wa thambo ndi dziko lapansi, ndinu woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi chimaliziro. Mulungu wa ulemerero, m'dzina la Yesu, ndikupemphani kuti mundikonzekere nthawi yomwe ndidzayankha zonse zomwe ndachita ndi zomwe ndalankhula pamene ndinali ndi moyo. Ikani mwa ine, Ambuye, chikhumbo ndi ludzu lofuna kukhala pafupi nanu ndi kuwerenga Mawu anu kuti ndikhale woyera ndi wopanda banga pamene ndidzaima pamaso panu pa chiweruzo chomaliza. Mundipange mwana wanu wakhama ndi wodalirika pa nkhani ya chipulumutso changa, kuti moyo wanga ukhale onunkhira bwino pamaso panu ndipo mapazi anga atsogoleredwe ndi mawu anu. Ndikumvetsa, Atate, kuti ndikufunika kukonzedwanso ndi kusinthidwa kuti ndikapereke umboni padziko lapansi ndi kukhala wokonzeka kukhala kumwamba. Mawu anu amati: "Pakuti nthawi yakwana kuti chiweruzo chiyambe pa nyumba ya Mulungu; ndipo ngati chiyamba pa ife choyamba, chitsiriziro chake chidzakhala chotani kwa iwo amene samvera Uthenga Wabwino wa Mulungu?". Ndithandizeni kukuyembekezerani tsiku lililonse, Yesu, ndi lingaliro lakuti munabwera dzulo ndipo mudzabweranso mawa kuti umbombo ndi chisiriro zisandisokeretse. Musalole, Ambuye, kuti zonyansa, kuipitsidwa kapena kudzikuza kundichotse pamaso panu. Ndithandizeni kuti nthawi zonse ndikhale pa ubwenzi wolimba nanu ndi kukhala nthawi yabwino pamaso panu, ndikudikira ndi kusala nthawi zonse. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa