Paja Chauta ndi wolungama, amakonda ntchito zolungama, ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.
Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Chauta ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro, njira zake zonse ndi zolungama, ndi Mulungu wokhulupirika ndi wosaipa konse, wachilungamo ndi wosalakwa.
Koma Chauta amakhala pa mpando wake waufumu nthaŵi zonse, adakhazika mpando wake kuti aziweruza. Iye amaweruza dziko lapansi molungama, amagamula milandu ya anthu mosakondera.
Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”
“Ine Chauta ndimakonda chilungamo, ndimadana ndi zakuba ndi zoipa. Anthu anga ndidzaŵapatsa mphotho mokhulupirika, ndidzapangana nawo chipangano chosatha.
Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera. Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.
Iye adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. Anthu amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pakuchita ntchito zabwino molimbikira, Mulungu adzaŵapatsa moyo wosatha. Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira.
Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Maziko a ufumu wanu ndiwo kulungama ndi kuweruza mosakondera. Mumaonetsa chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika pa zonse zimene mumachita.
Paja Mulungu mwa chilungamo chake, adzaŵalanga ndi masautso anthu amene amakusautsani inu.
Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”
Koma ngati wina afuna kunyadira, anyadire ichi chakuti amamvetsa za Ine, ndipo amandidziŵa. Amadziŵa kuti Ine ndine Chauta wokonda chifundo, chilungamo, ndi ungwiro pa dziko lapansi. Ndithudi, pazimenezi ndipo pali mtima wanga.”
Koma Chauta Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chilungamo chake, Mulungu Woyera adzaonetsa kuyera kwake pochita zaungwiro.
Mukonde osati china ai, koma chilungamo chokha basi, kuti mudzalandiredi dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani ngati choloŵa chanu, ndi kukhazikikamo.
Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi. “Landitsani ofooka ndi osoŵa. Apulumutseni kwa anthu oipa.”
Pakuti Chauta ndiye muweruzi wathu. Chauta ndiye wotilamula, Chauta ndiye mfumu yathu, ndiye amene adzatipulumutsa.
Mitambo ndi mdima waukulu zamzinga Chauta. Amalamulira molungama, mu ufumu wake mulibe tsankho.
Ukanena kuti, “Ife sitidazidziŵe zimenezi,” kodi iye amene amayesa mtima, zimenezi saziwona? Kodi amene amayang'anira moyo wako sazidziŵa? Kodi sadzambwezera munthu potsata ntchito zake?
Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene ndidzaphukitsira Davide nthambi yoongoka imene idzakhala mfumu yanzeru ndi yoweruza m'dzikomo mwachilungamo ndi mosakondera.
Mtima wanga wonse umalakalaka Inu usiku, mzimu wanga m'kati mwa ine umakufunafunani. Pamene muweruza dziko lapansi, anthu onse okhalamo amaphunzira chilungamo.
Koma tsopano wapereka Yesu pofuna kutsimikiza chilungamo chake, kuti anthu adziŵe kuti Iye mwini ngwolungama, adziŵenso kuti aliyense wokhulupirira Yesu amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu.
Kulungama kwanu kumaonekera ngati mapiri aatali, kuweruza kwanu nkozama ngati nyanja yakuya, Inu Chauta, mumasamalira anthu ndi nyama zomwe.
Amaonetsa chikondi chake kwa anthu zikwi zambirimbiri, ndipo amaŵakhululukira mphulupulu zao, zoipa zao, ndi machimo ao. Koma sadzalekerera ochimwa, ndipo adzalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha zoipa za atate ao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.”
Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Mulungu adzaŵaweruza onse, abwino ndi oipa omwe, pakuti adaika nthaŵi yochitikira chinthu chilichonse ndiponso ntchito iliyonse.”
pamene Chauta akufika, popeza kuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo, adzaweruza mitundu yonse mosakondera.
Pamenepo tinganene chiyani tsono? Kodi tinganene kuti Mulungu ngwosalungama? Iyai, sitingatero. Pajatu Iye adaauza Mose kuti, “Ndidzachitira chifundo amene ndifuna kumchitira chifundo, ndidzamvera chisoni amene ndifuna kumumvera chisoni.”
Amateteza ana amasiye ndi akazi amasiye. Amakonda anthu achilendo amene amakhala pakati panu, ndipo amaŵapatsa chakudya ndi zovala zomwe.
Munthu wokoma mtima amasamalira zoyenerera osauka, koma munthu woipa salabadako za zimenezo.
“Mverani, inu anthu anga, tcherani khutu, inu mtundu wanga. Malamulo adzachokera kwa Ine, ndipo chilungamo changa chidzaunikira anthu onse. Ndidzabwera mofulumira kudzaombola anthu anga, nthaŵi yanga ya kuŵapulumutsa ili pafupi. Ine mwiniwakene ndidzalamulira mitundu ya anthu onse. Maiko akutali akundidikira kuti ndibwere, akundiyembekeza ndi chikhulupiriro kuti ndidzaŵapulumutse.
Tsono khalani anthu oopa Chauta. Muzisamala zimene mukuchita, pakuti Chauta, Mulungu wathu, sapotoza chiweruzo, kapena kukondera, kapenanso kulandira ziphuphu.”
Amaitana zamumlengalenga ndi za pansi pano, kuti zichite umboni pamene akuweruza anthu ake. Iye akuti, “Sonkhanitsani pamaso panga, anthu anga okhulupirika, amene adachita chipangano ndi Ine popereka nsembe.”
Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.
Paja tikumdziŵa kale amene adati, “Kulipsira nkwanga, ndidzakhaulitsa ndine.” Adatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.”
Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Chauta, mumamva zimene odzichepetsa amapempha. Mudzalimbitsa mitima yao, mudzaŵatchera khutu. Potero mudzaŵateteza amasiye ndi opsinjidwa, kuti anthu amene ali a pansi pano, asadzathe kuwopsezanso.
Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sadabwezere chipongwe. Pamene ankazunzika, Iye sadaopseze, koma adapereka zonse kwa Mulungu amene amaweruza molungama.
Sadzafookera kapena kutaya mtima, mpaka atakhazikitsa chilungamocho pa dziko lapansi. Maiko akutali akuyembekeza malamulo ake.”
Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera.
Ndani angaŵaimbe mlandu anthu amene Mulungu adaŵasankha? Mulungu mwiniwake amaŵaona kuti ngolungama pamaso pake. Tsono palibe amene angaŵaweruze kuti ngopalamula. Khristu Yesu amene adafa, kaya tinene kuti amene adauka kwa akufa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndiye amene akutinenera kwa Mulunguyo.
Kulipsira nkwanga, kubwezera zoyenerera nkwanganso, nthaŵi yoti agwe idzakwana. Tsiku la masoka ao layandikira, chiwonongeko chao chikudza mofulumira.
Chauta ndi wolungama, adzaombola Ziyoni. Chauta ndi waungwiro, adzaombolanso anthu olapa amumzindamo.
Nanga Mulungu, angaleke kuŵaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku? Kodi adzangoŵalekerera? Iyai, kunena zoona adzaŵaweruzira mlandu wao msanga. Komabe Mwana wa Munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?”
Koma kuweruza kwanu kwangwiro kuziyenda kosalekeza ngati madzi, kulungama kwanu kukhale ngati mtsinje wosaphwa.
Yang'anani mlengalenga, yang'anani dziko lapansi. Mlengalenga udzazimirira ngati utsi, dziko lapansi lidzatha ngati chovala, ndipo anthu ake onse adzafa ngati ntchentche. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, ndipo kuwombola kwanga kudzakhala kwa nthaŵi zonse.
Chautatu akuti uziweruza molungama ndi mosakondera. Munthu amene adambera zake uzimpulumutsa kwa womsautsa. Usavutitse mlendo, mwana wamasiye kapena mkazi wamasiye. Usakhetse magazi a anthu osachimwa pa malo ano.
Pamaso pa Mulungu palibe kanthu kobisika, zonse zili poyera ndipo nzovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.
“Nayu mtumiki wanga amene ndamsankha. Ndimamkonda, ndipo mtima wanga umasangalala naye kwambiri. Ndidzaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzalalika za chilungamo kwa anthu a mitundu ina. Iye sadzachita makani, kapena kufuula. Palibe munthu wodzamva mau ake m'miseu ya m'mizinda. Pamene Afarisi adaona zimenezi, adauza Yesu kuti, “Taonani, ophunzira anu akuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata.” Iye sadzatsiriza bango lothyoka, nyale yofuka sadzaizimitsa, mpaka atapambanitsa chilungamo. Ndipo anthu akunja adzamdalira.”
Chauta, Mulungu wanga, chifukwa cha kulungama kwanu, onetsani kuti ine ndine wosalakwa, ndipo musalole kuti adani anga akondwere chifukwa cha mavuto anga.
pamenepo Inu mumve kumwambako, ndipo muchitepo kanthu ndi kuŵaweruza atumiki anuwo. Wochimwa mugamule kuti ngwolakwa ndipo mumlange molingana ndi zolakwa zakezo. Koma wosachimwayo mugamule kuti ngwopanda mlandu, ndipo mumpatse mphotho zoyenera makhalidwe akewo.
Mphambe sitingathe kumufika pafupi, ndi woopsa pa ulamuliro ndi pa mphamvu. Ndi wolungamadi kwambiri, sangazunze anthu.
Koma ngati kuipa mtima kwathu kuwonetsa kuti Mulungu ngwolungama, tinganene chiyani? Kodi tinganene kuti Mulungu ngwosalungama pamene atilanga? (Ndikulankhulatu monga momwe anthu ena amalankhulira). Mpang'ono pomwe. Mulungu akadakhala wosalungama, akadatha bwanji kukhala woweruza anthu onse?
Nthaŵi ina kudzakhala mfumu ina yolamulira mwaungwiro, ndiponso nduna zina zoweruza mwachilungamo.
Tsoka kwa amene amapanga malamulo opanda chilungamo, ndi kwa alembi amene amalemba zongovutitsa anzao. Ine ndidakantha mafumu a anthu opembedza mafano, amene mafano ao ndi aakulu kupambana a ku Yerusalemu ndi a ku Samariya. Ndiye ndingalephere kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake omwe, monga momwe ndidachitira Samariya ndi mafano ake?” Ambuye atamaliza ntchito yao yolanga onse pa phiri la Ziyoni ndiponso ku Yerusalemu, adzalanganso mfumu ya ku Asiriya, chifukwa cha kudzitama kwake ndi kunyada kwake. Pakuti mfumuyo ikuti, “Ndachita zimenezi ndi mphamvu zanga ndiponso ndi nzeru zanga, pakuti kumvetsa nkwanga. Ndachotsa malire a mitundu ya anthu, ndipo ndafunkha chuma chao. Ndaŵatsitsa amene anali pa mipando yaufumu. Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu, monga momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame. Monga momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, ndimo m'mene Ine ndidasonkhanitsira dziko lonse lapansi. Ndipo panalibe mbalame ndi imodzi yomwe yoti mapiko phephere-phephere, kapena yoti kukamwa yasa kapena yolira kuti psepsepse.” Koma Chauta akuti: “Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Kodi sowo ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti mkwapulo ukuzunguza munthu, kapena ndodo yanyamula munthu!” Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzatumiza matenda oondetsa kwa ankhondo amphamvu a mfumu ya ku Asiriya. Ndipo mfumuyo kunyada kwake kudzapsa ndi moto wosazimika. Mulungu, Kuŵala kwa Israele, adzakhala ngati moto. Mulungu, Woyera Uja wa Israele, adzakhala ngati malaŵi a moto. Motowo udzaŵatentha ndi kuŵapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi. Adzaononga nkhalango yaikulu ndi nthaka yachonde. Zidzaonongeka m'kati ndi kunja kwake, ndipo zidzakhala ngati munthu wodwala amene akuwonda. Mitengo yotsalira yam'nkhalangomo idzakhala yochepa kwambiri, yoti ndi mwana yemwe nkuiŵerenga. Pakutero amapotoza malamulo poweruza amphaŵi mosalungama. Amaŵalanda zoŵayenerera anthu anga osauka, amafunkha za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye!
Woweruza munthu woipa mtima kuti ndi wosalakwa, amanyansa Chauta, nayenso wopasa mlandu munthu wosalakwa amaipira Chauta.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula. Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira.
“Koma Ine Chauta ndimafufuza maganizo ndi kuuyesa mtimawo. Ndimamchitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndiponso moyenerera ntchito zake.”
“Tiyese kuti pali munthu wabwino amene amatsata malamulo ndi kuchita zabwino. Iyeyo sadyera nao ku zitunda zachipembedzo. Sapembedza mafano a ku Israele. Saipitsa mkazi wa munthu wina. Sakhudza mkazi pamene ali wosamba. Sazunza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole chigwiriro chake. Saaba, amadyetsa anjala, ndipo amaveka ausiwa. Sakongoza ndalama kuti apezepo phindu kapena kulandira chiwongoladzanja. Amadziletsa kuchita zoipa, ndipo sachita mokondera pogamula milandu ya anthu. Amatsata malangizo anga, ndipo amamvera malamulo anga mokhulupirika. Munthu wotereyu ndi wolungama, adzakhala ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wosalakwa,” anthu adzamtemberera, ndipo mitundu ya anthu idzaipidwa naye. Koma aweruzi amene amalanga anthu oipa adzapeza bwino, ndipo adzakhala ndi madalitso ambiri.
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
Pamenepo mpando wachifumu udzakhazikitsidwa mwachikondi, mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika. Iyeyo poweruza adzatsata zachilungamo, ndipo adzalimbikira kuchita zaungwiro.
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo.
Chauta akunena kuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu: chifukwa cha machimo anu mwafiira kwambiri, koma Ine ndidzakutsukani, inu nkukhala oyera kuti mbee. Mwachita kuti psuu ngati magazi, koma mudzakhala oyera ngati thonje. Ngati muli okonzeka kundimvera, mudzalidyera dziko.
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende. Chauta amatsekula maso a anthu osapenya, Chauta amakweza anthu otsitsidwa. Chauta amakonda anthu ochita chilungamo. Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
Chauta akuti, “Nayu mtumiki wanga amene ndimamchirikiza, amene ndamsankhula, amene ndimakondwera naye. Ndaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, ndi cha timbeu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.
Zolinga zanu nzazikulu, ndipo ntchito zanu nzamphamvu. Maso anu amaona makhalidwe onse a anthu. Ndipo aliyense mumampatsa mphotho malinga ndi makhalidwe ake ndi ntchito zake.
Ngati mumvera Chauta, adzakuyang'anirani ndipo adzayankha kupempha kwanu. Koma Chauta amaŵakwiyira anthu ochita zoipa, anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano.
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
Maziko a ufumu wanu ndiwo kulungama ndi kuweruza mosakondera. Mumaonetsa chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika pa zonse zimene mumachita. Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero, amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta.
Motero mfumuyo idzaweruza anthu anu molungama ndiponso anthu anu osauka mosakondera. Ano ndiwo mathero a mapemphero a Davide, mwana wa Yese. Mapiri adzabweretsa madalitso kwa anthu, magomo adzadzetsa mphotho ya chilungamo. Mfumu idzateteza anthu osauka, idzapulumutsa anthu osoŵa, koma idzaononga anthu ozunza anzao.
Chilungamo ndicho chidzakhala ngati chingwe choyesera maziko ake, ndipo ungwiro udzakhala ngati choongolera chake. Koma matalala adzaononga mabodza amene mumaŵakhulupirira, ndipo chigumula chidzamiza malo anu opulumukirapo.”
Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse.
Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa.
Muzidana ndi zoipa, muzikonda zabwino. Mukhazikitse chilungamo m'mabwalo a milandu. Mwina mwake Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, adzakukomerani mtima inu anthu otsala a m'banja la Yosefe.
Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu, koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.
Ulamuliro ndi mtendere wake zidzanka zikukulirakulira. Iye adzakhala pa mpando wa mfumu Davide, ndipo adzakhazikitsa ndi kuchirikiza ufumu wake, pochita zachilungamo ndi zangwiro kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse Chauta Wamphamvuzonse watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi.
Chauta ndi wabwino ndi wolungama. Nchifukwa chake amaphunzitsa ochimwa njira zake. Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama, amaŵaphunzitsa njira zake.
Koma Chauta ndi wolungama mumzindamo, Iyeyo salakwa. Amaweruza molungama tsiku ndi tsiku, nthaŵi zonse salephera, koma osalungama akuchitabe zoipa opanda manyazi.
pamaso pa Chauta, pamene zabwera kudzalamulira dziko lapansi. Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo, adzalamulira anthu a mitundu yonse moona.
M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
Ngati mukudziŵa kuti Khristu ndi wolungama, musapeneke konse kuti aliyense wochita chilungamo, ndi mwana wa Mulungu.
“Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu. Muzichitirana zolungama. Musazunze alendo kapena ana amasiye kapena akazi amasiye. Musaphe anthu osachimwa pa malo ano. Musamatsate milungu ina, kuti ingakuwonongeni. Mukamvera mau anga, ndidzakulolani kuti mukhale pa malo ano, m'dziko limene ndidapatsa makolo anu mpaka muyaya.
Chauta ndi wolemekezeka kwambiri, pakuti akukhala pamwamba pa zonse. Adzadzaza mzinda wa Ziyoni ndi chilungamo ndi ungwiro.
Oweruza adzaŵapatsa mtima wachilungamo. Adzaŵalimbitsa mtima onse amene amalimbana ndi adani pa zipata za mzinda.
Inu Chauta, ndinu olungama, munditsogolere pakati pa adani ondizonda. Mundikonzere njira yoongoka kuti ndidzeremo.
Anthu oipa samvetsa kuti chilungamo nchiyani, koma amene amatsata kufuna kwa Chauta amachimvetsa kwathunthu.
Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaŵeta nkhosa zanga mwachilungamo.”
Inu Chauta, ndikudziŵa kuti kuweruza kwanu nkolungama, ndipo mwandilanga potsata kukhulupirika kwanu.
Chauta akuuza anthu ake kuti, “Muzichita zabwino ndi zolungama, chifukwa ndikuwombolani posachedwa, chipulumutso changa chiwoneka.”
Koma amphaŵi adzaŵaweruza mwachilungamo, ndipo anthu otsika a pa dziko lapansi adzaŵagamulira mlandu wao mosakondera. Mau ochokera m'kamwa mwake adzakhala ngati ndodo yokanthira ochimwa, atalamula iyeyo anthu oipa adzaphedwa.
Ndithu iyo idzalanditsa anthu osoŵa amene amaiitana, idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda woŵathandiza. Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osoŵa, ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphaŵi. Idzaombola moyo wao kwa anthu oŵapsinja ndi kwa oŵachita zankhanza, pakuti magazi ao ndi amtengowapatali pamaso pake.
Chiweruzo chanu mudachilengeza kumwamba, anthu a pa dziko lapansi adaopa nakhala chete, pamene Inu Mulungu mudaimirira kuti muweruze anthu, ndi kupulumutsa opsinjidwa onse a pa dziko lapansi.
Mkwiyo wa Mulungu ukuwoneka kuchokera Kumwamba. Amakwiyira anthu chifukwa cha kusalungama kwao konse ndi kusamchitira ulemu. Kusalungama kwaoko kumaŵalepheretsa kudziŵa zoona.
Mulungu akutsogolera msonkhano wakumwamba. Akugamula mlandu milungu ya pansi pano. Akuti, “Mudzakhalabe mukuweruza mopanda chilungamo mpaka liti? Bwanji mukupitirizabe kumakondera anthu oipa? Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi. “Landitsani ofooka ndi osoŵa. Apulumutseni kwa anthu oipa.”
Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.
Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama, koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe.
Pakuti Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wopambana milungu yonse, ndiponso ndi Ambuye oposa ambuye onse. Ndi wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, sakondera, ndipo salandira ziphuphu. Amateteza ana amasiye ndi akazi amasiye. Amakonda anthu achilendo amene amakhala pakati panu, ndipo amaŵapatsa chakudya ndi zovala zomwe.
Ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira aŵakomere mtima, koma munthu amamuweruza molungama ndi Chauta yekha.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Koma mpulumutsi wao ndi wamphamvu, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Adzaŵaimira pa mlandu, kuti apatse mtendere dziko lonse lapansi, koma adzavutitsa okhala ku Babiloni.
Koma tsopano yaoneka njira yopezera chilungamo pamaso pa Mulungu, ndipo njira yake si kutsata Malamulo ai. Malamulowo ndi aneneri omwe amaichitira umboni. Njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupirire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupirira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai, popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera. Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola. Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa. Koma tsopano wapereka Yesu pofuna kutsimikiza chilungamo chake, kuti anthu adziŵe kuti Iye mwini ngwolungama, adziŵenso kuti aliyense wokhulupirira Yesu amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu.
Chauta wachotsa chilango chanu. Wapirikitsa adani anu. Chauta, Mfumu ya Israele, ali nanu pamodzi. Simudzaopanso choipa chilichonse.
Mau a Chauta ndi olungama, zochita zake zonse amazichita mokhulupirika. Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera. Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.
Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu. Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena. Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira. Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa. Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango.
Paja Chauta ndiye amapatsa nzeru, Iye ndiye kasupe wa kudziŵa zinthu ndi wa kumvetsa. Amasungira anthu olungama nzeru zenizeni, ali ngati chishango choteteza oyenda mwaungwiro. Ndiye mlonda wa njira zolungama, amatchinjiriza njira ya anthu ake oyera mtima.
Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.
Ankaimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa uja. Mau ake ankati, “Ambuye, Mulungu Mphambe, ntchito zanu nzazikulu ndi zododometsa. Inu, Mfumu ya anthu a mitundu yonse, njira zanu nzolungama ndi zoona. Ambuye, ndani angapande kukuwopani ndi kutamanda dzina lanu? Paja ndinu nokha oyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera nkudzakupembedzani, popeza kuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”