Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


135 Mau a Mulungu Pa Chilungamo Chake

135 Mau a Mulungu Pa Chilungamo Chake


Masalimo 11:7

Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama; woongoka mtima adzapenya nkhope yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:18

Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:4

Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:7-8

Koma Yehova akhala chikhalire, anakonzeratu mpando wachifumu wake kuti aweruze. Ndipo Iyeyu adzaweruza dziko lapansi m'chilungamo, nadzaweruza anthu molunjika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:19

Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:3

Kuchita chilungamo ndi chiweruzo kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:8

Pakuti Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m'zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:5

Iye ndiye wakukonda chilungamo ndi chiweruzo, dziko lapansi ladzala ndi chifundo cha Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:6-8

amene adzabwezera munthu aliyense kolingana ndi ntchito zake; kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha; koma kwa iwo andeu, ndi osamvera choonadi, koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 6:8

Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:28

Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:10

pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:14

Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wachifumu wanu; chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 1:6

popeza nkolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:15

Kuchita chiweruzo kukondweretsa wolungama; koma kuwaononga akuchita mphulupulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:17

phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 9:24

koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:16

koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'chiweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 16:20

Chilungamo, chilungamo ndicho muzichitsata, kuti mukhale ndi moyo ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:6

Ndipo zakumwamba zionetsera chilungamo chake; pakuti Mulungu mwini wake ndiye woweruza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 82:3-4

Weruzani osauka ndi amasiye; weruzani molungama ozunzika ndi osowa. Pulumutsani osauka ndi aumphawi; alanditseni m'dzanja la oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 33:22

Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 97:2

Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wachifumu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:12

Ukanena, Taonani, sitinadziwa chimenechi; kodi woyesa mitima sachizindikira ichi? Ndi wosunga moyo wako kodi sachidziwa? Ndipo kodi sabwezera munthu yense monga mwa machitidwe ake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 7:11

Mulungu ndiye Woweruza wolungama, ndiye Mulungu wakukwiya masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 23:5

Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzachita mwanzeru, nadzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dziko lino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:9

Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:26

kuti aonetse chilungamo chake m'nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:6

Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:7

wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulangira ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:17

Ndinati mumtima wanga, Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi ntchito zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 98:9

Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 9:14-15

Ndipo tsono tidzatani? Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ai. Pakuti anati ndi Mose, Ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:6

Yehova achitira onse osautsidwa chilungamo ndi chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 10:18

Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:7

Wolungama asamalira mlandu wa osauka; koma woipa alibe nzeru yakuudziwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 51:4-5

Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kunditcherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga; pakuti lamulo lidzachokera kwa Ine, ndipo ndidzakhazikitsa chiweruziro changa chikhale kuunika kwa anthu. Chilungamo changa chili pafupi, chipulumutso changa chamuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 19:7

Ndipo tsono, kuopa Yehova kukhale pa inu, musamalire ndi kuchita; pakuti palibe chosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu, kapena kulandira mphatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:6

Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika, ndi kuweruza kwako monga usana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:4-5

Kumwamba adzaitana zakumwamba, ndi dziko lapansi, kuti aweruze anthu ake. Mundisonkhanitsire okondedwa anga; amene anapangana ndi Ine ndi nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:6

Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:30

pakuti timdziwa Iye amene anati, Kubwezera chilango nkwanga, Ine ndidzabwezera. Ndiponso, Ambuye adzaweruza anthu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:12

Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:9

Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:17-18

Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu; kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa pa dziko lapansi angaonjeze kuopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:23

amene pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 42:4

Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa chiweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira chilamulo chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:5

Mulungu, mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:8

kuti atchinjirize njira za chiweruzo, nadikire khwalala la opatulidwa ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 5:4

Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa mphulupulu siikhala ndi Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:33-34

Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye amene awayesa olungama; ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:137

Inu ndinu wolungama, Yehova, ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:35

Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 75:7

Pakuti Mulungu ndiye woweruza; achepsa wina, nakuza wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:27

Ziyoni adzaomboledwa ndi chiweruzo, ndi otembenuka mtima ake ndi chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:7-8

Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima? Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. Koma Mwana wa Munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi kodi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 5:24

Koma chiweruzo chiyende ngati madzi, ndi chilungamo ngati mtsinje wosefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:1

Muyeso wonyenga unyansa Yehova; koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 51:6

Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi pa dziko pakuti kumwamba kudzachoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati chofunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa ngati njenjete; koma chipulumutso changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chilungamo changa sichidzachotsedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 22:3

Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:13

Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:18-21

Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzaika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja. Sadzalimbana, sadzafuula; ngakhale mmodzi sadzamva mau ake m'makwalala; Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la Sabata. bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse. Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 35:24

Mundiweruze monga mwa chilungamo chanu, Yehova Mulungu wanga; ndipo asandisekerere ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:32

mverani Inu pamenepo m'mwambamo, ndipo chitani, weruzani akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera tchimo lake, ndi kulungamitsa wolungamayo kumbwezera monga chilungamo chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 37:23

Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa; koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:5-6

Koma ngati chosalungama chathu chitsimikiza chilungamo cha Mulungu, tidzatani ife? Kodi ali wosalungama Mulungu, amene afikitsa mkwiyo? (Ndilankhula umo anenera munthu). Msatero ai. Ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji mlandu wa dziko lapansi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:1

Taonani mfumu idzalamulira m'chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m'chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:3

Odala iwo amene asunga chiweruzo, iye amene achita chilungamo nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 10:1-2

Tsoka kwa iwo amene alamulira malamulo osalungama, ndi kwa alembi olemba mphulupulu; Popeza dzanja langa lapeza maufumu a mafano, mafano ao osema anapambana ndi iwo a ku Yerusalemu ndi ku Samariya; monga ndachitira Samariya ndi mafano ake, momwemo kodi sindidzachitira Yerusalemu ndi mafano ake? Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse pa phiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa. Popeza anati, Mwa mphamvu ya dzanja langa ndachita ichi, ndi mwa nzeru yanga; pakuti ine ndili wochenjera; ndachotsa malekezero a anthu, ndalanda chuma chao, ndagwetsa monga munthu wolimba mtima iwo okhala pa mipando yachifumu; dzanja langa lapeza monga chisa, chuma cha mitundu ya anthu, ndipo monga munthu asonkhanitsa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe chogwedeza phiko, kapena chotsegula pakamwa, kapena cholira pyepye. Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo. Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto. Ndipo kuwala kwa Israele kudzakhala moto, ndi Woyera wake adzakhala lawi; ndipo lidzatentha ndi kuthetsa minga yake ndi lunguzi wake tsiku limodzi. Ndipo adzanyeketsa ulemerero wa m'nkhalango yake, ndi wa m'munda wake wopatsa bwino, moyo ndi thupi; ndipo padzakhala monga ngati pokomoka wonyamula mbendera. Ndipo mitengo yotsala ya m'nkhalango yake idzakhala yowerengeka, kuti mwana ailembera. kuwapatulira osowa kuchiweruziro, ndi kuchotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:15

Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama, onse awiriwa amnyansa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:142

Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha; ndi chilamulo chanu ndicho choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1-2

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende; Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Ine wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo. Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse. ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:10

Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 18:5-9

Koma munthu akakhala wolungama, nakachita chiweruzo ndi chilungamo, wosadya pamapiripo, wosakweza maso ake kumafano a nyumba ya Israele, wosaipsa mkazi wa mnansi wake, kapena kuyandikira mkazi ataoloka, wosasautsa munthu aliyense, koma wambwezera wangongole chigwiriro chake, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala, wosapereka molira phindu, wosatenga choonjezerapo wobweza dzanja lake lisachite chosalungama, woweruza zoona pakati pa munthu ndi mnzake, amayenda m'malemba anga, nasunga maweruzo anga kuchita chokhulupirika; iye ndiye wolungama, adzakhala ndi moyo ndithu, anena Ambuye Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 75:2

Pakuona nyengo yake ndidzaweruza molunjika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:24-25

Wonena kwa woipa, Wolungama iwe; magulu a anthu adzamtemberera, mitundu ya anthu idzamkwiyira. Omwe amdzudzula adzasekera, nadzadalitsika ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:12

Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 16:5

Ndipo mpando wachifumu udzakhazikika m'chifundo, ndimo wina adzakhala pamenepo m'zoona, m'chihema cha Davide, nadzaweruza, nadzafunitsa chiweruziro, nadzafulumira kuchita chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:11

pakuti Mulungu alibe tsankho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:8

Zapang'ono, pokhala chilungamo, ziposa phindu lalikulu lopanda chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:17

Yehova ali wolungama m'njira zake zonse, ndi wachifundo m'ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:18-19

Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu. Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:7-9

ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi. Yehova apenyetsa osaona; Yehova aongoletsa onse owerama; Yehova akonda olungama. Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 42:1

Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:23

Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 32:19

wamkulu m'upo, wamphamvu m'ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:15-16

Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao. Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:9

Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:14-15

Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wachifumu wanu; chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu. Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:2-4

Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m'chilungamo, ndi ozunzika anu ndi m'chiweruzo. Mapemphero a Davide mwana wa Yese atha. Mapiri adzatengera anthu mtendere, timapiri tomwe, m'chilungamo. Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:5

Maganizo a olungama ndi chiweruzo; koma uphungu wa oipa unyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 28:17

Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chilili; ndipo matalala adzachotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:11

Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:10

Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 5:15

Danani nacho choipa, nimukonde chokoma; nimukhazikitse chiweruzo kuchipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:34

Chilungamo chikuza mtundu wa anthu; koma tchimo lichititsa fuko manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:7

Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:8-9

Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima, chifukwa chake adzaphunzitsa olakwa za njira. Adzawatsogolera ofatsa m'chiweruzo; ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zefaniya 3:5

Yehova pakati pake ali wolungama; sadzachita chosalungama, m'mawa ndi m'mawa aonetsera chiweruzo chake poyera, chosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 96:13

Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:12

Chotero munthu aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:2

Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:29

Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:5-7

Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi machitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wake; ndi kuleka kutsendereza mlendo, ndi wamasiye, ndi mkazi wamasiye, osakhetsa mwazi wosachimwa m'malo muno, osatsata milungu ina ndi kudziipitsa nayo; ndipo ndidzakukhazikani inu m'malo muno, m'dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuyambira kale lomwe kufikira muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 33:5

Yehova wakwezedwa; pakuti akhala kumwamba; Iye wadzaza Ziyoni ndi chiweruzo ndi chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:9

Njira ya oipa inyansa Yehova; koma akonda wolondola chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 28:6

ndipo adzakhala mzimu wa chiweruziro kwa oweruza milandu, ndi mphamvu kwa iwo amene abweza nkhondo pachipata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 5:8

Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:5

Oipa samvetsetsa chiweruzo; koma omwe afuna Yehova amvetsetsa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 34:16

Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:75

Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova, ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 56:1

Atero Yehova, Sungani inu chiweruziro, ndi kuchita chilungamo; pakuti chipulumutso changa chili pafupi kudza, ndi chilungamo changa chili pafupi kuti chivumbulutsidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 11:4

koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:12-14

Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 76:8-9

Mudamveketsa chiweruzo chochokera Kumwamba; dziko lapansi linachita mantha, nilinakhala chete, pakuuka Mulungu kuti aweruze, kuti apulumutse ofatsa onse a pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:18

Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera Kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi m'chosalungama chao;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 82:1-4

Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu, aweruza pakati pa milungu. Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti, ndi kusamalira nkhope ya oipa? Weruzani osauka ndi amasiye; weruzani molungama ozunzika ndi osowa. Pulumutsani osauka ndi aumphawi; alanditseni m'dzanja la oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:11

Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:16

Anadziwika Yehova, anachita kuweruza, woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 10:17-18

Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu. Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:26

Ambiri afunafuna chiyanjano cha mkulu; koma chiweruzo cha munthu chichokera kwa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 34:12

Ndithu zoonadi, Mulungu sangachite choipa, ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 50:34

Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lake Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumutse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala m'Babiloni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:21-26

Koma tsopano chilungamo cha Mulungu chaoneka chopanda lamulo, chilamulo ndi aneneri achitira ichi umboni; ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana; pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu; amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe; kuti aonetse chilungamo chake m'nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zefaniya 3:15

Yehova wachotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israele, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:4-5

Pakuti mau a Yehova ali olunjika; ndi ntchito zake zonse zikhulupirika. Iye ndiye wakukonda chilungamo ndi chiweruzo, dziko lapansi ladzala ndi chifundo cha Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1-2

Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu. Chikondano sichichitira mnzake choipa; chotero chikondanocho chili chokwanitsa lamulo. Ndipo chitani ichi, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira. Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika. Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake. Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:160

Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi; ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:6-8

Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m'kamwa mwake. Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni; ndiye chikopa cha oyenda molunjika; kuti atchinjirize njira za chiweruzo, nadikire khwalala la opatulidwa ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 15:3-4

Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha. Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa