Kale, anthu ankapereka nsembe za nyama kwa Mulungu m’Chipangano Chakale. Koma, pali mavesi ambiri omwe amasonyeza kuti Mulungu safuna nsembe zimenezo ndipo amafuna kuti tisamalire zinyama.
Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 12:10a limati, “Wolungama asamalira moyo wa nyama yake; Koma mtima wa oipa ndi wankhanza.” Mawu a Mulungu amalankhulapo zoteteza zinyama; ngati titayang’anitsitsa mau a aneneri, tipeza mavesi ambiri amene amatilimbikitsa kusamalira zinyama.
M’buku la Hoseya 8:13b timawerenga kuti, “Nsembe zawo za nyama ndi kudya nyama kwandibweretsera chonyansa, ndipo Ambuye sakondwera nazo, koma adzakumbukira mphulupulu zawo ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.”
Motero Mulungu adalenga nsomba zazikulu zam'nyanja, pamodzi ndi zolengedwa zina zonse zokhala m'madzi, ndiponso mbalame ndi zouluka zina zamitundumitundu. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Koma nyama zonse zakuthengo, mbalame, ndi zokwaŵa zonse, ndazipatsa msipu kuti zizidya,” ndipo zidachitikadi momwemo.
Zitatha izo Mulungu adati, “Tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam'nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoŵeta, ndi zokwaŵa zonse za pa dziko lapansi.”
Ndipo Mulungu adati, “Padziko pakhale mitundu yonse ya zamoyo potsata mitundu yake: zoŵeta, zokwaŵa, ndi nyama zakuthengo, potsata mitundu yake.” Ndipo zidachitikadi.
Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.”
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwanawambuzi, mwanawang'ombe ndi mwanawamkango adzadyera limodzi, mwana wamng'ono nkumaziŵeta zonsezo.
Zitatha izo Mulungu adati, “Tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam'nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoŵeta, ndi zokwaŵa zonse za pa dziko lapansi.” Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi. Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.”
Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziŵeto zake, koma munthu woipa mtima chifundo chake nchankhwidzi.
Zamoyo zonse za pa dziko lapansi pamodzi ndi mbalame zomwe, nyama zokwaŵa ndi zonse zam'nyanja zidzakuwopani. Zonsezi ndaziika kuti muzilamule. Nowa anali mlimi ndipo anali woyamba kulima munda wamphesa. Tsiku lina atangomwa vinyo, adaledzera, ndipo adavula zovala zake zonse, nakagona ali maliseche m'hema mwake. Hamu, bambo wake wa Kanani, ataona kuti Nowa bambo wake ali maliseche, adapita nakauza abale ake aŵiri aja. Koma Semu ndi Yafeti adatenga chofunda nachiika kumbuyo kwao, atachinyamula pa mapewa. Tsono adayenda chafutambuyo nafunditsa bambo wao. Sadapenyeko kumene kunali bambo wao uja ndipo sadaone maliseche ake. Nowa atadzuka, adamva zonse zimene mwana wake wamng'onoyo adaachita, ndipo adati, “Atembereredwe Kanani! Adzakhala kapolo weniweni wa abale ake.” Popitiriza mau adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Semu, Kanani adzakhale kapolo wa Semuyo. Mulungu amkuze Yafeti. Zidzukulu zake zidzagaŵane madalitso ndi zidzukulu za Semu. Kanani adzakhale kapolo wa Yafetiyo.” Chitatha chigumulacho, Nowa adakhala ndi moyo zaka zina 350. Adamwalira ali wa zaka 950. Tsopano mungathe kudya nyama zonse, monga ndidakulolani kudya ndiwo zamasamba. Ndakupatsani zonsezi kuti zikhale chakudya chanu.
Tsono Chauta adamtenga munthuyo, namukhazika m'munda wa Edeni uja kuti azilima ndi kumausamala.
“Ukaona ng'ombe ya mdani wako ikusokera, kapena bulu wake, utenge ukampatse. Bulu wa mdani wako akagwa ndi katundu, usabzole ndi kumsiya, koma umthandize kuti adzuke.
Mimbulu ndi anaankhosa zidzadyera pamodzi. Mkango udzadya udzu monga ng'ombe. Fumbi ndiye lidzakhale chakudya cha njoka. Pa phiri langa loyera la Ziyoni sipadzakhala chinthu chopweteka kapena choononga,” akuterotu Chauta.
Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako.
Uzidziŵe bwino nkhosa zako m'mene ziliri, ndipo usamalire ziŵeto zako. Paja chuma sichikhala mpaka muyaya. Kodi ufumu umakafika mpaka ku mibadwo yonse? Udzu ukatha, msipu nkuphuka, ndipo atatuta udzu wakumapiri, anaankhosa adzakupatsa chovala, ndi ubweya wao, ndipo pogulitsa mbuzi udzapeza chogulira munda. Udzakhala ndi mkaka wambiri wa mbuzi kuti uzidya, iweyo ndi banja lako, ndiponso ndi adzakazi ako omwe.
Kulungama kwanu kumaonekera ngati mapiri aatali, kuweruza kwanu nkozama ngati nyanja yakuya, Inu Chauta, mumasamalira anthu ndi nyama zomwe.
Ndipo udzatengenso nyama za mtundu uliwonse, yaimuna ndi yaikazi, kuti zisungidwe ndi moyo.
“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri musamagwira ntchito, kuti ng'ombe zanu zipume pamodzi ndi abulu anu omwe, kutinso akapolo anu ndi alendo omwe apezenso mphamvu.
Mukaona ng'ombe kapena nkhosa ya Mwisraele mnzanu ikusokera, musailekerere. Itengeni, mukampatse mwiniwake. Musamange ng'ombe ndi bulu kuti zilimire pamodzi. Musamavale nsalu yoombedwa ndi ubweya pamodzi ndi thonje. Sokani mphonje pa ngodya zinai za miinjiro yanu imene mumavala. Mwina munthu angathe kukwatira mtsikana, namakhala naye ndithu, pambuyo pake nkunena kuti mkaziyo sakumfuna. Tsono ayamba kumnenera zabodza zochititsa manyazi ndi kuipitsa mbiri yake ponena kuti, “Mkazi ameneyu sadaoneke ngati namwali wosadziŵa mwamuna pa nthaŵi yomukwatira.” Zitatero, makolo a mkaziyo atenge zizindikiro zotsimikizira akuluakulu abwalo am'mudzimo kuti mwana waoyo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ndithu. Pamenepo bambo wake wa mtsikanayo aŵauze abwalowo kuti, “Ndidalola mwana wanga wamkazi kuti akwatiwe ndi munthu uyu, koma tsopano akuti sakumufuna. Wamnamizira momchititsa manyazi kuti ati sadali namwali wosadziŵa mwamuna pomkwatira. Koma pano tili ndi umboni wotsimikizira kuti mwana wangayu adaali namwali wangwiro ndithu. Onani, zizindikiro zake ndi izi.” Apo adzaonetse chovala cha mkaziyo kwa akuluakuluwo. Tsono akuluakulu am'mudzimo amtenge mwamunayo ndi kumkwapula. Pambuyo pake amlipitsenso masekeli asiliva makumi khumi, ndipo azipereke kwa bambo wa mtsikanayo. Alipe ndithu chifukwa choti adanyozetsa mnamwali Wachiisraele amene sadamdziŵeko mwamuna. Komanso adzakhalabe mkazi wake ndithu, ndipo pa moyo wake wonse sadzathanso kumsudzula. Koma ngati mwiniwake kwao nkutali, kapena simumdziŵa, itengeni mupite nayo kwanu, muisunge komweko. Koma mwiniwake akabwera kudzaifunafuna, mumpatse. Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo umboni wakuti mtsikanayo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ukusoŵa, pamenepo apite naye pakhomo pa bambo wake. Pomwepo amuna amumzindamo amuphe pakumponya miyala. Mtsikanayo wachita chinthu chochititsa manyazi pakati pa mtundu wathu wa Israele pochita zadama m'nyumba ya bambo wake. Motero mudzachotsa choipa pakati pa inu. Munthu akagwidwa akuchita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, aphedwe onsewo, mwamuna ndi mkazi yemwe. Choncho mudzachotsa choipa pakati pa inu. Tiyese kuti mwagwira munthu mumzinda momwemo akuchita chigololo ndi mnamwali wofunsidwa mbeta, amene sadamdziŵeko mwamuna. Muŵatenge onsewo, mupite nawo kunja kwa mzinda, ndipo muŵaphe poŵaponya miyala. Mtsikanayo aphedwe chifukwa ngakhale anali m'mudzi, sadakuwe kuti anthu adzamthandize. Mwamunayo aphedwe chifukwa wachimwa ndi mtsikana wofunsidwa mbeta ndi mnzake. Motero mudzachotsa choipa pakati panu. Mwina munthu, kuthengo koteroko, achita kugwirira mtsikana wofunsidwa mbeta nachita naye chigololo momkakamiza. Zikatero, munthu wamwamuna yekhayo ndiye aphedwe. Mtsikanayo musamchite kanthu chifukwa choti sadachite tchimo loyenera kufa nalo. Mlandu umenewu ukufanafana ndi wakuti munthu aputa mnzake, namupha. Munthuyo wachita kumgwira mtsikanayo nkuchita naye chigololo kuthengo. Ndipo ngakhale adaakuwa, panalibe amene akadampulumutsa. Mwina munthu agwidwa akugwirira mnamwali wosafunsidwa mbeta, amene sadamdziweko mwamuna, nachita naye chigololo momkakamiza. Munthuyo alipe bambo wake wa mtsikanayo mtengo wofunsira mbeta, ndiye kuti masekeli asiliva makumi asanu, ndipo amtenge kuti akhale mkazi wake chifukwa choti adamkakamiza kuchita naye chigololo. Tsono pa moyo wake wonse sangathenso kumsudzula. Mukapeza bulu, chovala kapena kanthu kena kalikonse kamene Mwisraele mnzanu wataya, chitani chimodzimodzi, musakalekerere ai. Munthu asakwatire mkazi wa bambo wake, kapena kuchita chipongwe chomuvula. Bulu wa Mwisraele mnzanu akagona mu mseu, muutseni. Muchitenso chimodzimodzi ndi ng'ombe yake, musailekerere. Mthandizeni mnzanu kuti adzutse choŵetacho.
Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake. pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo. Zonse zimapita kumodzimodzi. Zonsezo nzochokera ku dothi, ndipo zimabwerera kudothi komweko.
Ngati mupeza chisa cha mbalame mu mtengo kapena pansi, make ali pa mazira, kapena ali ndi tiana take, musaitenge mbalameyo pamodzi ndi tiana take. Tianato mungathe kutenga, koma makeyo mloleni apite, kuti mukakhale ndi moyo wabwino ndi wautali.
Bulu wa mdani wako akagwa ndi katundu, usabzole ndi kumsiya, koma umthandize kuti adzuke.
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwanawambuzi, mwanawang'ombe ndi mwanawamkango adzadyera limodzi, mwana wamng'ono nkumaziŵeta zonsezo. Ng'ombe yaikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi, ndipo ana ao adzagona pamodzi. Mkango udzadya udzu ngati ng'ombe. Mwana woyamwa adzaseŵera pa dzenje la mamba, ndipo mwana woleka kuyamwa adzapisa dzanja lake ku funkha la mphiri, osalumidwa. Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena choononga pa phiri lopatulika la Mulungu. Ndipo anthu a pa dziko lonse lapansi adzakhala odzaza ndi nzeru ya kudziŵa Chauta, monga nyanja imadzazira ndi madzi.
Pamenepo Nowa adamanga guwa kumangira Chauta. Adatengako mtundu uliwonse wa nyama ndi mbalame zimene anthu amaperekera nsembe, ndipo adazipha, napereka nsembe zopsereza paguwapo.
“Popeza kuti nyama iliyonse yam'nkhalango ndi yanga, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku mapiri ochuluka. Mbalame zonse zamumlengalenga, zamoyo zonse zoyenda ku thengo ndi zanga.
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa.
Kenaka adaŵafunsa kuti, “Ndani mwa inu, bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime pa tsiku la Sabata, sangaitulutse pa Sabata pomwepo?”
“Suja amagulitsa atimba asanu tindalama tiŵiri? Komabe Mulungu saiŵala ndi mmodzi yemwe. Ndipo tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.”
Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera. Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa. Pakuti zolengedwazo zidaasanduka zogonjera zopanda pake, osati chifukwa zidaafuna kutero ai, koma chifukwa Mulungu adaagamula choncho. Komabe zili ndi chiyembekezo ichi, chakuti izonso zidzamasulidwa ku ukapolo wa kuwola, ndi kulandirako ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu.
Nanga Ine, kodi sindiyenera kuumvera chisoni mzinda waukulu wa Ninive? M'mene mujatu muli anthu opitirira zikwi 120, amene sadziŵa kusiyanitsa kuti zabwino nziti, zoipa nziti, mulinso ziŵeto zochuluka.”
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu. Kuli nyanja yaikulu ndi yotambalala, yodzaza ndi zinthu zosaŵerengeka, zinthu zamoyo, zazing'ono ndi zazikulu zomwe.
Mngelo wa Chauta adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako chotere katatu? Ndabwera kudzakutsekera njira, chifukwa ulendo wakowu ukundiipira. Bulu wako anandiwona, ndipo anasiya njira katatu konse atandiwona. Akadapanda kusiya njira atandiwona, ndithu ndikadakuphera pomwepo, koma buluyo ndikadamleka kuti akhale moyo.”
Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu.
chakuti izonso zidzamasulidwa ku ukapolo wa kuwola, ndi kulandirako ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu. Tikudziŵa kuti mpaka tsopano zolengedwa zonse zakhala zikubuula ndi kumva zoŵaŵa, zonga za mkazi pa nthaŵi yake yochira.
“Kodi iwe umaidziŵa nthaŵi imene zinkhoma zimaswera? Kodi udaziwonapo nswala zikubadwa? Kodi ungathe kuimanga ndi nsinga kuti izilima? Kodi ingasalaze nthumbira m'munda mwako? Kodi ungadalire njatiyo chifukwa cha mphamvu zake? Kodi ungayembekeze kuti ikugwirira ntchito yako? Kodi ungakhulupirire kuti idzabwera nkudzatuta tirigu wako ku malo opunthira? “Nthiŵatiŵa ikukupiza mapiko ake monyadira, koma nthenga zake ndi mapiko ake sizikuithandiza kuuluka monga amachitira kakoŵa. Nthiŵatiŵa imafotsera mazira ake pansi, kuti afundidwe m'nthaka. Koma imaiŵala kuti mapazi ake omwe angathe kuphwanya mazirawo, ndipo kuti nyama zakuthengo nkuŵapondereza. Nthiŵatiŵa imachita ana ake nkhalwe ngati si ake. Zakuti idaavutika poŵabereka imaiŵalako. Paja Mulungu adaimana nzeru, kotero kuti simvetsa kanthu kalikonse. Komabe nthiŵatiŵayo ikadzambatuka nkuyamba kuthaŵa, imamsiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake. “Kodi ndiwe amene umapatsa mphamvu kavalo? Nanga ndiwe amene umaveka chenjerere m'khosi mwake? Kodi ungathe kuŵerenga miyezi imene zimakhala ndi bele? Kodi nthaŵi imene nyamazi zimaswa iwe umaidziŵa? Kodi ndiwe amene umamlumphitsa ngati dzombe? Kavalo akamadzuma, mpweya wake ndi waukali ndiponso woopsa. Kavaloyo amalumphalumpha m'chigwa, ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse. Sachita mantha, sachita nkhaŵa, ndipo sabwerera m'mbuyo akaona lupanga. Zida zankhondo za wokwerapo wake zimachita kwichikwichi m'phodo, ndipo mkondo ndi nthungo zimanyezemira pa dzuŵa. Akavalowo amanjenjemera ndi ukali nathamangira kutsogolo, ndipo akangomva lipenga sangathe kuima. Lipenga likalira amati, ‘Twee!’ Amamva fungo la nkhondo ali patali. Amamva kufuula kwa atsogoleri ankhondo. “Kodi ndi nzeru zako zimene zimaphunzitsa kabaŵi kuuluka, ndi kutambalitsa mapiko ake kupita chakumwera? Kodi umalamula chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwuluka? Kodi udachiphunzitsa ndiwe kukamanga chisa pamwamba penipeni? Chimakhala pa phiri, nkumanga chisa chake pamenepo, pansonga penipeni pa thanthwe losakwereka. Pamenepo chimayang'ana choti chigwire kuti chidye, ndipo maso ake amachiwonera patali chinthucho. Kodi ukuidziŵa nthaŵi imene zidzakhala tsonga nkuswa ana, kenaka nkutayiza? Ana ake amayamwa magazi, amapezeka kumene kuli mitembo.” Kuyankha kwa Yobe. Ana a nyamazi amakhala amphamvu, namakulira ku thengo. Pambuyo pake amapita, osabwereranso kwa mai wao.
Mudampatsa ulamuliro pa ntchito za manja anu. Mudamgonjetsera zolengedwa zonse, nkhosa, ng'ombe ndi nyama zakuthengo, mbalame zamumlengalenga, nsomba zam'nyanja, ndi zonse zoyenda pansi pa nyanja.