Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


49 Mau a Mulungu Okhudza Chakudya

49 Mau a Mulungu Okhudza Chakudya

Chakudya ndi nkhani yofunika kwambiri imene imapezeka kangapo m’Baibulo. Uku mu Genesis, mukupezeka nkhani ya zipatso ndi zomera monga chakudya cha munthu.

Mu Chipangano Chakale, mulinso malamulo okhudza zakudya, omwe amatiuza zamitundu ya nyama zomwe tingadye. Ndipo mu Chipangano Chatsopano, pali nkhani zambiri zomwe Yesu anadya limodzi ndi otsatira ake, kusonyeza kufunika kwa ubale wathu ndi Mulungu ndi anzathu pamene tidya limodzi.

Komanso, Baibulo limatiphunzitsa kuti thupi lathu ndi kachisi wa Mzimu Woyera, choncho tiyenera kulisamalira bwino. Ndipo kusamalira thupi lathu kumaphatikizapo kudya bwino.

Zonsezi zimatiphunzitsa kuti chakudya si chongotipatsa mphamvu zokha, koma ndi njira yoti tilimbikitse ubale wathu ndi Mulungu komanso ndi anzathu. Monga mwambi umati, “M’mimba mulibe m’bale”. Koma ife, monga Akhristu, tiyenera kuona chakudya ngati njira yoti tigwirizanitse anthu, monga momwe Yesu anachitira.




Luka 12:22-23

Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Pakuti moyo umaposa chakudya, ndipo thupi limaposa zovala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:9

Chauta amapha ludzu la munthu womva ludzu, amamudyetsa zinthu zabwino munthu womva njala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 136:25

Amapatsa zamoyo zonse chakudya, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:3

Amene amadya chilichonse, asanyoze mnzake amene amazisala. Amene amasala zinthu zina asaweruze mnzake amene amazidya, pakuti Mulungu wamulandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:7

Wokhuta amaipidwa ndi chisa cha uchi, koma kwa munthu wanjala ndi zoŵaŵa zomwe zimatsekemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 16:4

Apo Chauta adauza Mose kuti, “Chabwino, ndikupatsani chakudya chimene chidzagwa ngati mvula kuchokera kumwamba. Anthu azituluka tsiku ndi tsiku kukatola chakudya chokwanira tsiku limodzi, kuti ndiŵayese ndipo ndiwone ngati adzayenda motsata malamulo anga kapena ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 16:12-15

“Ndamva madandaulo a Aisraele. Ndiye uŵauze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama, ndipo m'maŵa mudzadya buledi, choncho mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’ ” Motero madzulo kudagwa zinziri, ndipo zidadzaza ponseponse pamahemapo. M'maŵa ndithu padagwa mame ponse pozungulira mahemawo. Mamewo atangokamuka, panthakapo m'chipululu muja padapezeka tinthu tina topyapyala, tambee ngati chipale, ndiponso tonyata. Aisraele ataona tinthuto sadatidziŵe kuti nchiyani, mwakuti adayamba kufunsana kuti “Kodi timeneti ntiyani?” Mose adaŵauza kuti, “Ameneyu ndi buledi yemwe Chauta wakupatsani kuti mudye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:31

Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 26:4-5

ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake, ndipo nthaka idzakubalirani zokolola zochuluka, ndipo mitengo yam'minda idzakubalirani zipatso. “Tsono adzaulula machimo ao ndi machimo a makolo ao chifukwa cha kunyenga kwao kumene adandinyenga nako, ndiponso chifukwa cha kuyenda motsutsana ndi Ine. Paja chifukwa cha zimenezo Ine ndidatsutsana nawo ndi kuŵafikitsa ku dziko la adani ao. Tsono mitima yao youma idzadzichepetsa ndi kulola kulangidwa chifukwa cha machimo ao. Pamenepo ndidzakumbukira chipangano changa ndi Yakobe, Isaki, ndi Abrahamu, ndipo dzikolo ndidzalikumbukira. Koma ayambe aisiya nthaka yaoyo, kuti ikondwerere zaka zoipumuza, pamene dziko lili lopanda anthu, iwo atachoka. Tsono iwo adzalangika chifukwa cha machimo ao, popeza kuti adanyoza zimene ndidaŵalamula, ndipo mitima yao idadana ndi malangizo anga. Ngakhale zitachitika zonsezo, pamene ali m'dziko la adani ao, sindidzaŵanyoza ndipo sindidzadana nawo mpaka kuŵaononga kwathunthu ndi kuphwanya chipangano changa ndi iwo, chifukwa Ine ndine Chauta, Mulungu wao. Koma poŵachitira chifundo ndidzakumbukira chipangano changa ndi makolo ao amene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, mitundu ina ya anthu ikupenya, kuti ndikhale Mulungu wao. Ine ndine Chauta.” Ameneŵa ndiwo malamulo ndi malangizo amene Chauta adaika pakati pa Iye mwini ndi Aisraele pa phiri la Sinai, kudzera mwa Mose. Mudzakhala mukupuntha dzinthu mpaka nthaŵi yothyola zipatso, ndipo mudzakhala mukuthyola zipatso mpaka nthaŵi yobzala. Mudzadya chakudya mpaka kukhuta, ndi kumakhala m'dziko mwanu popanda chokuvutani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 8:3

Adakutsitsani pokukhalitsani ndi njala, komanso adakupatsani mana kuti mudye. Inu ndi makolo anu simudadyepo ndi kale lonse chakudya chimenechi. Adachita zimenezi kuti akuphunzitseni kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha ai, koma ndi mau onse otuluka m'kamwa mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 11:14-15

Ndipo Iye azidzagwetsa mvula m'dziko mwanu pa nthaŵi yake, monga nthaŵi yadzinja ndiponso nthaŵi yachilimwe, kotero kuti mudzakhala ndi tirigu wambiri, vinyo wambiri ndiponso mafuta aolivi ambiri. Adzameretsa udzu woti ng'ombe zanu zizidzadya, ndipo inunso mudzapeza chakudya ndi kukhuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:4

Koma Yesu adati, “Malembo akuti, “ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:22-24

Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Pakuti moyo umaposa chakudya, ndipo thupi limaposa zovala. Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:12

Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:1

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:15-16

Maso onse amayang'anira kwa Inu, ndipo mumaŵapatsa chakudya pa nthaŵi yake. Mumafumbatula dzanja lanu, ndipo mumapatsa chamoyo chilichonse zofuna zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:10

Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:1-2

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:13-14

Tsono Petro adamva mau akuti, “Petro dzuka, ipha udye.” Koma Petro adati, “Iyai, pepani Ambuye, ine sindinadyepo ndi kale lonse chinthu chosayera kapena chonyansa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:25

Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 9:3-4

Tsopano mungathe kudya nyama zonse, monga ndidakulolani kudya ndiwo zamasamba. Ndakupatsani zonsezi kuti zikhale chakudya chanu. Koma pali chinthu chimodzi chokha chimene simuyenera kudya, ndicho nyama imene ikali ndi magazi. Ndaletsa poti magaziwo ndiwo moyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:1-2

Chauta akunena kuti, “Inu nonse omva ludzu, bwerani, madzi ali pano. Ndipo inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule chakudya, kuti mudye. Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka, osalipira ndalama, osalipira chilichonse. “Mvula ndi chisanu chambee zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko, koma zimathirira nthaka. Zimameretsa ndi kukulitsa zomera, kenaka nkupatsa alimi mbeu ndi chakudya. Ndimonso amachitira mau ochokera m'kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidaŵatumira zidzayenda bwino. “Inu anthu anga, mudzachoka ku Babiloni mokondwa, adzakutulutsani mumzindamo mwamtendere. Inu mukufika, mapiri ndi magomo adzakuimbirani nyimbo. Nayonso mitengo yonse yam'thengo idzakuwomberani m'manja. Kumene tsopano kuli mitengo yaminga kudzamera mitengo ya paini. Kumene tsopano kuli mkandankhuku kudzamera michisu. Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Ine Chauta, ngati chizindikiro chamuyaya chimene sichidzafafanizika konse.” Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:24-25

Poŵagwetsera mana kuti adye, adaŵapatsa tirigu wakumwamba. Motero anthu adadya buledi wa angelo, ndipo Mulungu adaŵatumizira chakudya chochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:14-15

Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka. Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 9:3

Tsopano mungathe kudya nyama zonse, monga ndidakulolani kudya ndiwo zamasamba. Ndakupatsani zonsezi kuti zikhale chakudya chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 111:5

Amapatsa chakudya anthu omuwopa, amakumbukira chipangano chake nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 132:15

“Ndidzadalitsa kwambiri mzinda wa Ziyoni poupatsa zosoŵa zake, anthu ake osauka, ndidzaŵapatsa chakudya chokwanira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 8:8

Nzoona kuti chakudya sichitifikitsa pafupi ndi Mulungu. Tikapanda kudya chakudyacho, sititayapo kanthu, komanso tikachidya, sitipindulapo kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:29

Ndipo Mulungu adati, “Ndikukupatsani zomera zonse za mtundu wokhala njere, ndi mitundu yonse ya zomera zobala zipatso zanjere, kuti muzidya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17

Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:13

Chakudya, kwake nkuloŵa m'mimba, ndipo mimba, kwake nkulandira chakudya. Koma Mulungu adzaononga ziŵiri zonsezo. Thupi la munthu si lochitira dama, koma ndi la Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo mwiniwake thupilo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:3

Chauta salola kuti munthu womukondweretsa iye, azikhala ndi njala, koma zimene woipa amazilakalaka, Mulungu amam'mana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:29-30

Ndipo Mulungu adati, “Ndikukupatsani zomera zonse za mtundu wokhala njere, ndi mitundu yonse ya zomera zobala zipatso zanjere, kuti muzidya. Tsono Mulungu adati, “Kuyere,” ndipo kudayeradi. Koma nyama zonse zakuthengo, mbalame, ndi zokwaŵa zonse, ndazipatsa msipu kuti zizidya,” ndipo zidachitikadi momwemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:8-9

Musalole kuti ndikhale wabodza kapena wonama. Ndisakhale mmphaŵi kapena khumutcha. Muzindidyetsa chakudya chondiyenera, kuwopa kuti ndikakhuta kwambiri, ndingayambe kukukanani nkumanena kuti, “Chauta ndiye yaninso?” Kuwopanso kuti ndikakhala mmphaŵi, ndingayambe kuba, potero nkuipitsa dzina la Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:2

Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:11

Mutipatse ife lero chakudya chathu chamasikuwonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:36

Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, ndi nsomba zija, adathokoza Mulungu, nazinyemanyema nkuzipereka kwa ophunzira ake, iwowo nakazigaŵira anthu aja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:25-26

“Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala? Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 14:19-20

Atatero, adalamula kuti anthu aja akhale pansi pa udzu. Tsono adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake, ophunzira aja nkukagaŵira anthuwo. Tsono adauza nduna zake kuti, “Ameneyu ndi Yohane Mbatizi uja, adauka kwa akufa, nkuwona akuchita zamphamvu zonsezi.” Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Pambuyo pake ophunzira aja adatola zotsala nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:35-37

Apo Yesu adalamula anthu aja kuti akhale pansi. Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, ndi nsomba zija, adathokoza Mulungu, nazinyemanyema nkuzipereka kwa ophunzira ake, iwowo nakazigaŵira anthu aja. Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Adatola zotsala, nkudzaza madengu asanu ndi aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:24

Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:35

Yesu adaŵauza kuti, “Chakudya chopatsa moyocho ndine. Munthu aliyense wodza kwa Ine, sadzamva njala. Ndipo aliyense wokhulupirira Ine, sadzamva ludzu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 14:17

Komabe sankaleka kudzichitira umboni mwa zabwino zimene amachita. Kuchokera kumwamba amakupatsani mvula ndi nyengo za zipatso. Amakupatsani zakudya ndi zina zambiri zodzaza mitima yanu ndi chimwemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:6

Amene amasunga tsiku lakutilakuti, amatero kuti alemekeze Ambuye. Amene amadya chilichonse, amatero kuti alemekeze Ambuye, pakuti amayamika Mulungu chifukwa cha chakudyacho. Amene amasala zina, amatero kuti alemekeze Ambuye, ndipo amayamika Mulungu pakutero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:19

Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:4-5

Pajatu chilichonse chimene Mulungu adalenga nchabwino, palibe chilichonse choti munthu asale, akamachilandira moyamika Mulungu, pakuti chimayeretsedwa ndi mau a Mulungu ndi mapemphero aja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:17

Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Chauta wanga Wamuyaya, Ambuye Wapamwamba! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, ndi woyenera kutamandidwa konse ndi kupembedzedwa. Atate, zikomo chifukwa chakuti zonse munazipanga bwino kwambiri ndipo munalenga zabwino kwambiri kwa anthu, munatipatsa zipatso za dziko lapansi ndi chakudya choti tidye. Ndikukupemphani kuti mundithandize kusamalira thupi langa chifukwa ndi kachisi ndi nyumba ya Mzimu wanu Woyera. Mundiphunzitse kukhala wanzeru pa kudya, kusamalira thupi langa, kugwiritsa ntchito bwino chakudya, ndi kudya zakudya zabwino. Mundithandize kuti ndisadye dala zakudya zoipa zomwe zingandichititse kudwala. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa