Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


48 Mau a m'Baibulo Okhudza Zivomerezi ndi Chivomezi

48 Mau a m'Baibulo Okhudza Zivomerezi ndi Chivomezi

Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, mwina mukudziwa nkhani ya Adamu ndi Eva, momwe anachimwira Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, dziko lathu lino linaledzera. Baibulo limatiuza mu Genesis 3:17 kuti Mulungu anauza Adamu kuti, "Popeza wamvera mkazi wako, nudya zipatso za mtengo umene ndinakuletsa, dziko lapansi lidzatembereredwa chifukwa cha iwe; udzadya zipatso zake ndi zowawa masiku onse a moyo wako."

Kumbukirani kuti Mulungu analenga dziko lino labwino kwambiri. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi la chilengedwe, zonse zinali zabwino kwambiri. Koma uchimo unabweretsa temberero ndi matenda. Zinthu ngati zivomerezi zimatipatsa chenjezo. Zimatiwonetsa kuti ufumu wa Khristu ukubwera, ndipo tiyenera kulapa machimo athu ndi mtima wonse.

Ngati sitilapa, tidzatayika miyoyo yathu ndi kukhala pamalo okhetsa mano ndi kulira kwamuyaya. Mulungu akufuna kuti tisinthe miyoyo yathu, tisiye zoyipa ndi machimo, ndi kukhala oyera mtima. Tiyeni timvere mawu a Mulungu ndikukhala moyo woyenera.




Luka 21:11

Kudzachita zivomezi zazikulu. Kudzakhala njala ndi mliri ku malo osiyanasiyana. Kudzakhalanso zoopsa ndi zizindikiro zodabwitsa mu mlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 13:8

Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana, ndipo kudzakhala njala. Tsono zonsezitu nkuyamba chabe kwa mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 29:6

Chauta Wamphamvuzonse adzakupulumutsa ndi mabingu, zivomezi ndi phokoso lalikulu. Adzatumizanso kamvulumvulu, namondwe ndi malaŵi a moto woononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 19:18

Phiri lonse la Sinai lidaphimbidwa ndi utsi, chifukwa choti Mulungu adaatsikira paphiripo. Utsiwo unkangokwera ngati utsi wam'ng'anjo, ndipo anthu onse aja ankangonjenjemera kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 19:11-12

Apo Chauta adati, “Tuluka, ukaime pa phiri, pamaso panga.” Tsono Chauta adadutsa pamenepo, ndipo mphepo yamphamvu idaomba ning'amba mapiri ndi kuswa matanthwe, koma Chauta sanali m'mphepomo. Itapita mphepoyo, padachita chivomezi, koma Chauta sanali m'chivomezimo. Chitapita chivomezi chija, padafika moto, koma Chauta sanali m'motomo. Utapita motowo, padamveka kamphepo kongoti wii.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:54

Mkulu wa asilikali ndiponso amene anali naye polonda Yesu, ataona chivomezi chija ndi zina zonse zimene zidaachitika, adachita mantha kwambiri nati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:7

Pamenepo dziko lapansi lidanjenjemera ndi kuchita chivomezi. Maziko a mapiri nawonso adanjenjemera ndi kugwedezeka, chifukwa Iye adaakalipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:26

Mwadzidzidzi kudachita chivomezi champhamvu, kotero kuti maziko a ndende adagwedezeka. Nthaŵi yomweyo zitseko zonse zidatsekuka, maunyolo a mkaidi aliyense nkumasuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:2

Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 11:19

Pamenepo mudatsekuka m'Nyumba ya Mulungu Kumwamba, ndipo bokosi lachipangano lidaoneka m'Nyumbamo. Kenaka kudachita mphezi, phokoso, mabingu ndi chivomezi, ndipo kudagwa matalala akuluakulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:7

Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:2-3

Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama, ngakhale nyanja zikokome ndi kututuma. Ngakhale mapiri anjenjemere ndi kulindima kwa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 6:12

Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chimodzi. Ndipo padachitika chivomezi champhamvu. Dzuŵa lidadzangoti bii ngati chiguduli chakuda, mwezi wathunthu nkungoti psuu ngati magazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 24:19-20

Dziko lapansi lidzathyokathyoka, lidzang'ambika kwathunthu ndi kugwedezeka kwamphamvu. Aliyense adzaona zimodzimodzi: ansembe ndi anthu, akapolo aamuna ndi ambuyao aamuna, adzakazi ndi ambuyao aakazi, ogula ndi ogulitsa, obwereka ndi oŵabwereka, ndiponso okongola ndi okongoza. Dziko lapansi lidzadzandira ngati munthu woledzera, lidzagwedezeka ngati chisimba nthaŵi ya mkuntho. Dziko lapansi lalemedwa ndi zoipa zake, lidzagwa ndipo silidzaukanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 24:20

Dziko lapansi lidzadzandira ngati munthu woledzera, lidzagwedezeka ngati chisimba nthaŵi ya mkuntho. Dziko lapansi lalemedwa ndi zoipa zake, lidzagwa ndipo silidzaukanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:2

Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 11:13

Nthaŵi yomweyo kudachita chivomezi chachikulu, mwakuti chimodzi mwa zigawo khumi za mzinda chidagwa, ndipo anthu zikwi zisanu ndi ziŵiri adaphedwa ndi chivomezicho. Otsalawo adaopsedwa kwambiri nayamba kutamanda Mulungu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 16:18

Nthaŵi yomweyo kudachita mphezi, phokoso ndi mabingu. Kudachitanso chivomezi champhamvu. Chilengedwere cha anthu pa dziko lapansi sikudachitikeponso chivomezi chotero: chimenecho chinali choopsa zedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:10

Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 38:19

Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo, ndikulumbira kuti kudzachita chivomezi chachikulu m'dziko lonse la Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 13:13

Tsono ndidzagwedeza mlengalenga, ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Ine Chauta Wamphamvuzonse pa tsiku la mkwiyo wanga woopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:10

Koma Chauta ndiye Mulungu woona, Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo ndiponso Mfumu yamuyaya. Dziko lapansi limagwedezeka ndi ukali wa Chauta. Anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 3:16

Chauta akukhuluma ku Ziyoni, mau ake amveka ngati bingu kuchokera ku Yerusalemu. Ndipo thambo ndi dziko lapansi zikugwedezeka. Koma Chauta ndiye pothaŵirapo anthu ake, ndiye linga lotetezera a ku Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 14:15

Tsono Afilisti onse m'dzikomo adasokonezeka ndi mantha aakulu. Ankhondo a ku kaboma kankhondo kaja ndi anzao enanso ankanjenjemera kwambiri. Kudachita chivomezi ndipo kugwedezeka kwa dziko kudakulitsa mantha a Afilisti aja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 38:19-20

Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo, ndikulumbira kuti kudzachita chivomezi chachikulu m'dziko lonse la Israele. “Iwe mwana wa munthu, udzudzule Gogi, wa ku dziko la Magogi, kalonga wamkulu wa mzinda wa Meseki ndi wa Tubala, ndipo umuimbe mlandu. Nsomba za m'nyanja ndi mbalame zamumlengalenga, nyama zakuthengo ndi zokwaŵa zonse, pamodzi ndi anthu onse okhala pa dziko lapansi, zonsezo zidzanjenjemera ndi mantha. Mapiri adzaphwanyika, magomo adzanyenyeka, ndipo makoma onse adzagwa pansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 38:20

Nsomba za m'nyanja ndi mbalame zamumlengalenga, nyama zakuthengo ndi zokwaŵa zonse, pamodzi ndi anthu onse okhala pa dziko lapansi, zonsezo zidzanjenjemera ndi mantha. Mapiri adzaphwanyika, magomo adzanyenyeka, ndipo makoma onse adzagwa pansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 1:1

Naŵa mau a Amosi amene ankaŵeta nkhosa ku Tekowa. Zimenezi, zodzachitikira Aisraele, Chauta adamuululira pa nthaŵi ya Uziya, mfumu ya ku Yuda, ndi pa nthaŵi ya Yerobowamu, mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Israele, kutatsala zaka ziŵiri kuti chivomezi chija chichitike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nahumu 1:5

Mapiri amagwedezeka pamaso pake, magomo amasungunuka. Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake, ndiye kuti dziko ndi zonse zokhala m'menemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 8:8

Chifukwa cha zonsezi dziko lapansi lidzagwedezeka, ndipo onse okhala m'menemo adzamva chisoni! Dziko lonse lapansi lidzagwedezeka ngati Nailo, lidzafufuma ndi kuteranso ngati mtsinje wa Nailo wa ku Ejipito.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 14:4

Tsiku limenelo adzaimirira pa phiri la Olivi loyang'anana ndi Yerusalemu chakuvuma, ndipo phirilo lidzagaŵika paŵiri ndi chigwa chachikulu choyenda kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Theka la phiri lidzasunthira chakumpoto, theka lina chakumwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 14:5

Inu mudzapulumuka podzera m'chigwa chimenecho cha pakati pa mapiri. Mudzathaŵa monga m'mene mudaathaŵira nthaŵi ija ya chivomezi pa nthaŵi ya Uziya mfumu ya ku Yuda. Kenaka Chauta, Mulungu wanu, adzabwera pamodzi ndi oyera ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:51-54

Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika. Manda adatsekuka ndipo anthu a Mulungu ambiri amene anali atamwalira kale, adauka kwa akufa. Adatuluka m'manda, ndipo Yesu atauka kwa akufa, iwo adaloŵa mu Yerusalemu, Mzinda Wopatulika, anthu ambiri nkumaŵaona. Mkulu wa asilikali ndiponso amene anali naye polonda Yesu, ataona chivomezi chija ndi zina zonse zimene zidaachitika, adachita mantha kwambiri nati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:51

Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:26

Nthaŵi imeneyo mau a Mulungu adaagwedeza dziko, koma tsopano lino walonjeza ndi mau akuti, “Kamodzi kenanso ndidzagwedeza, osati dziko lokha ai, koma ndi thambo lomwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:31

Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:32

Iye amati akayang'ana dziko lapansi, limanjenjemera, akakhudza mapiri, mapiriwo amafuka nthunzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:26-27

Nthaŵi imeneyo mau a Mulungu adaagwedeza dziko, koma tsopano lino walonjeza ndi mau akuti, “Kamodzi kenanso ndidzagwedeza, osati dziko lokha ai, koma ndi thambo lomwe.” Mau akuti “Kamodzi kenanso” akuwonetsa poyera kuti zolengedwa zonse zogwedezeka zidzachotsedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zidzakhalitse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:2

pakuti mosachedwa amanyala ngati udzu, ndipo amafota ngati masamba aaŵisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 8:5

Pamenepo mngeloyo adatenga chofukiziracho nachidzaza ndi moto wochokera ku guwa lija. Adachiponya pa dziko lapansi, ndipo nthaŵi yomweyo padachitika mabingu, phokoso, mphezi ndi chivomezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 3:12

Pamenepo Mzimu wa Mulungu udandinyamula, ndipo kumbuyo kwanga ndidamva liwu lamphamvu ngati chivomezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Chauta kumene Iye amakhala!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 1:3

Taonani, Chauta akubwera kuchokera ku malo ake. Akutsika pansi ndipo akuyenda pa nsonga za mapiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:8

dziko lidagwedezeka, mlengalenga udagwetsa mvula chifukwa cha kubwera kwanu, Inu Mulungu. Phiri la Sinai lidagwedezeka chifukwa cha kubwera kwanu, Inu Mulungu, Mulungu wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 17:26-30

“Monga momwe zidaachitikira pa nthaŵi ya Nowa, zidzateronso pa nthaŵi ya Mwana wa Munthu. Masiku amenewo anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kumakwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Pamenepo chigumula chidafika nkuŵaononga onse. Monga momwe zidaachitikiranso pa nthaŵi ya Loti. Anthu ankangodya ndi kumwa, ankagulitsana malonda, ankabzala mbeu, ankamanga nyumba. Koma tsiku limene Loti adatuluka m'Sodomu, Mulungu adagwetsa moto ndi miyala yoyaka ya sulufule nkuŵaononga onsewo. Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire. Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 19:11

Apo Chauta adati, “Tuluka, ukaime pa phiri, pamaso panga.” Tsono Chauta adadutsa pamenepo, ndipo mphepo yamphamvu idaomba ning'amba mapiri ndi kuswa matanthwe, koma Chauta sanali m'mphepomo. Itapita mphepoyo, padachita chivomezi, koma Chauta sanali m'chivomezimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 75:3

Pamene dziko lapansi likugwedezeka pamodzi ndi zonse zokhalamo, ndine amene ndimachirikiza mizati yake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:19

Anthu adzathaŵira m'mapanga am'matanthwe ndi m'maenje am'nthaka, kuthaŵa mkwiyo wa Chauta, kuthaŵanso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzabwere kudzaopsa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 102:25-26

Inu mudaika maziko a dziko lapansi kalekale, ndipo zakumwamba mudazipanga ndi manja anu. Zonsezi zidzatha ngati malaya, koma Inu mulipobe. Inu mumazisintha ngati chovala, ndipo zimatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:24-26

Tsono padauka namondwe woopsa panyanjapo, kotero kuti mafunde ankaloŵa m'chombomo. Koma Yesu anali m'tulo. Pamenepo ophunzira ake aja adamudzutsa, adati, “Ambuye, tipulumutseni, tikumiratu!” Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha, inu anthu a chikhulupiriro chochepa?” Atatero adaimirira nkudzudzula mphepoyo ndi nyanjayo, kenaka padagwa bata lalikulu ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, Wamuyaya, wapamwamba koposa, m'dzina la Yesu ndikubwera kwa Inu, Inu nokha ndinu woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa kwakukulu. Atate, nthawi ino yachisoni ndi masoka pomwe mabanja ambiri akhudzidwa ndi zivomezi ndi masoka achilengedwe, ndikupemphani kuti muchitire chifundo ndi kutambasula dzanja lanu lamphamvu pa miyoyo yawo ndipo chitetezo chanu chikhale pa iwo, kuti athe kuyang'ana kumwamba ndi kulira kwa Inu kuti amvetsetse kuti Inu ndinu thandizo lawo, chithandizo chawo chachangu m'mavuto, ndipo muli ndi mphamvu pa chilichonse chifukwa m'manja mwanu muli kuzama kwa dziko lapansi ndipo Inu nokha muli ndi mphamvu zolilimbitsa. Ndikupemphani kuti pakati pa kutaya mtima kwawo, mtendere ndi mphamvu zanu zilamulire mitima yawo. Sungani ndi kuteteza omwe avulala ndi omwe akhudzidwa m'maganizo, tambasulani dzanja lanu lochiritsira pa iwo, awapatse mankhwala, chakudya ndi pokhala kuti miyoyo yawo itetezedwe ku mantha ndi kutaya mtima. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa