Mulungu sanatilembere malangizo enieni a chilengedwe chake, koma adakhazikitsa malamulo achilengedwe kuti alamulire mphamvu za chilengedwe, zomwe zimagwirira ntchito nthawi zonse mogwirizana ndi chifuniro chake champhamvu. Chilengedwecho chimandiwonetsa kuti Mulungu aliko, monga momwe Salmo 19:1 imanenera: "Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo limasonyeza ntchito ya manja ake".
Monga wokhulupirira, ndikofunikira kumvetsa kuti zinthu zosaoneka za Mulungu, monga mphamvu zake ndi ulemerero wake, zimawululidwa kudzera mu chilengedwe chake. Mulungu amasangalala pamene ine ndimadabwa ndi ntchito zake, chifukwa chilichonse chotizinga chidalengedwa kuti ndizindikire kuchuluka kwa chikondi chake kwa ine komanso kuti ndidziwe kukongola kwake, zomwe zimandilola kumulambira ndi mtima wanga wonse.
Ndiyenera kuyamikira chilengedwe, kuganizira za Mulungu ndi kumuthokoza, chifukwa chifundo chake chimawonekera m'moyo wanga nthawi iliyonse dzuwa likamatuluka.
Pamene iwo adamva zimenezi, onse adayamba kupemphera ndi mtima umodzi. Adati, “Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lakumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi zonse zili m'menemo.
Zakumwamba ndi zanu, dziko lapansi nalonso ndi lanu. Mudapanga dziko lonse ndi zonse zam'menemo.
Mtamandeni inu dzuŵa ndi mwezi, mtamandeni inu nonse nyenyezi zoŵala! Mtamandeni inu thambo lakumwambamwamba, ndi inu madzi a pamwamba pa thambo! Zonsezo zitamande dzina la Chauta! Paja Iye adaalamula, izo nkulengedwa.
Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko,
Inu mudaika maziko a dziko lapansi kalekale, ndipo zakumwamba mudazipanga ndi manja anu.
Zakumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere, nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo. Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam'menemo. Mitengo yam'nkhalango idzaimba mokondwa
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
“Inu Ambuye athu ndi Mulungu wathu, ndinu oyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu, pakuti ndinu mudalenga zinthu zonse. Mudafuna kuti zonsezo zikhalepo, ndipo zidalengedwa.”
Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri. Tsono kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
Ndidalenga dziko lapansi ndi mphamvu zanga ndi nyonga zanga. Ndidalenga anthu ndi nyama pa dziko lapansi, ndipo ndimalipereka kwa amene ndimamuwona kuti ndi woyenera.
Adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthaŵi yake. M'mitima mwa anthu Mulungu adaikanso nzeru zotanthauzira zochitika za pa mibadwo ndi mibadwo. Komabe anthuwo sangathe kuzitulukira ntchito zonse za Mulungu kuyambira pa chiyambi mpaka pomalizira.
Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera. Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa. Pakuti zolengedwazo zidaasanduka zogonjera zopanda pake, osati chifukwa zidaafuna kutero ai, koma chifukwa Mulungu adaagamula choncho. Komabe zili ndi chiyembekezo ichi,
Zakumwamba zimalalika ulemerero wa Mulungu, thambo limasonyeza ntchito za manja ake. Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide, ngakhale golide wambiri wamtengowapatali, nzotsekemera kupambana uchi, ngakhale uchi wozuna kwambiri. Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu, poŵasunga ndimalandira mphotho yaikulu. Nanga ndani angathe kudziŵa zolakwa zake? Inu Chauta, mundichotsere zolakwa zanga zobisika. Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala, kulakwa koteroku ndisakutsate. Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu. Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga. Usana umasimbira zimenezo usana unzake, usiku umadziŵitsa zimenezo usiku unzake. Palibe kulankhula, palibe kunena mau aliwonse. Liwu lao silimveka konse. Komabe uthenga wao umafalikira pa dziko lonse lapansi. Mau aowo amafika mpaka ku mathero a dziko. Mulungu adamangira dzuŵa nyumba m'thambomo.
Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu. Kuli nyanja yaikulu ndi yotambalala, yodzaza ndi zinthu zosaŵerengeka, zinthu zamoyo, zazing'ono ndi zazikulu zomwe.
ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake, ndipo nthaka idzakubalirani zokolola zochuluka, ndipo mitengo yam'minda idzakubalirani zipatso.
Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko, ndimadzifunsa kuti, “Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?”
Tsono Chauta adamtenga munthuyo, namukhazika m'munda wa Edeni uja kuti azilima ndi kumausamala.
“Inu anthu anga, mudzachoka ku Babiloni mokondwa, adzakutulutsani mumzindamo mwamtendere. Inu mukufika, mapiri ndi magomo adzakuimbirani nyimbo. Nayonso mitengo yonse yam'thengo idzakuwomberani m'manja. Kumene tsopano kuli mitengo yaminga kudzamera mitengo ya paini. Kumene tsopano kuli mkandankhuku kudzamera michisu. Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Ine Chauta, ngati chizindikiro chamuyaya chimene sichidzafafanizika konse.”
Ngakhale ku mabusa akuchipululu kumamera msipu wambiri, ndipo mapiri amadzazidwa ndi chimwemwe.
mzinda wokongola wa Ziyoni pa phiri la Mulungu, wopatsa chimwemwe ku dziko lonse lapansi. Mzinda wa Ziyoni umene uli kumpotowu, ndi mzinda wa Mfumu yathu yaikulu.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame? Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake? “Ndipo mumaderanji nkhaŵa ndi zovala? Onani maluŵa akuthengo m'mene amakulira. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu ai. Komatu kunena zoona, ngakhale mfumu Solomoni yemwe, mu ulemerero wake wonse, sankavala zokongola kulingana ndi limodzi lomwe mwa maluŵa ameneŵa.
Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta, dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake. Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta Wamphamvuzonse. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero. Pakuti iye ndi amene adaika dziko lapansi pa nyanja yaikulu, adalikhazika pa mitsinje yozama.
Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera. Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.
Kumwamba ndi zonse zili kumeneko ndi zake za Chauta, pamodzi ndi dziko lapansi pano ndi zonse zili m'menemo.
Kodi inu simukhutira kudya pa busa labwino? Nanga mumaponderezeranji zimene simudya? Kodi simukhutira kumwa madzi abwino? Nanga madzi amene simumwa mumaŵadetsereranji ndi mapazi anu?
Pamenepo Ezara adapemphera kuti, “Inu nokha ndiye Chauta. Inu mudalenga kumwamba, kumwambamwamba, ndiponso zonse zokhala komweko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Mudalenga nyanja ndi zonse zam'menemo. Zonse zakumwamba zimakupembedzani.
“Mtunda usagulitsidwe mpaka muyaya, pakuti dzikolo ndi langa. Inu ndinu alendo ndiponso oyendayenda okhala ndi Ine. M'dziko monse m'mene mudzakhalemo, mudzaloleza anzanu kuwombola mtunda umene unali wao kale.
Inu mumatumphutsa akasupe m'zigwa, mitsinje imayenda pakati pa mapiri. Imapatsa nyama zonse zakuthengo madzi akumwa, mbidzi zimapherapo ludzu. Mbalame zimamanga zisa pafupi ndi mitsinjeyo, zimaimba m'nthambi za mitengo. Inu mumathirira mapiri ndi madzi ochokera ku malo anu akumwamba. Dziko lapansi ladzaza ndi madalitso anu. Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka.
“Inu aYobe, tamvani izi, imani, muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu. Kodi mukudziŵa m'mene Mulungu amazichitira, ndi m'mene amang'anipitsira mphezi m'mitambo yake? Kaya mukudziŵa m'mene Mulungu amayalira mitambo, ntchito yosonyeza nzeru zake zodabwitsa,
Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziŵeto zake, koma munthu woipa mtima chifundo chake nchankhwidzi.
Amaphimba zakumwamba ndi mitambo, amapatsa nthaka mvula, amameretsa udzu pa magomo. Amapereka chakudya kwa nyama ndi kwa ana a khungubwi pamene akulira chakudya.
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwanawambuzi, mwanawang'ombe ndi mwanawamkango adzadyera limodzi, mwana wamng'ono nkumaziŵeta zonsezo. Ng'ombe yaikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi, ndipo ana ao adzagona pamodzi. Mkango udzadya udzu ngati ng'ombe. Mwana woyamwa adzaseŵera pa dzenje la mamba, ndipo mwana woleka kuyamwa adzapisa dzanja lake ku funkha la mphiri, osalumidwa. Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena choononga pa phiri lopatulika la Mulungu. Ndipo anthu a pa dziko lonse lapansi adzakhala odzaza ndi nzeru ya kudziŵa Chauta, monga nyanja imadzazira ndi madzi.
Adayala dziko lapansi pa madzi, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adalenga miyuni yaikulu yamumlengalenga, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Dzuŵa kuti lizilamulira usana, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira usiku, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Ndipo Mulungu adati, “Nachi chizindikiro cha chipangano chamuyaya chimene ndikuchiika pakati pa Ine ndi inu ndi cholengedwa chilichonse chimene chili ndi inu. Ndikuika utawaleza m'mitambo, ndipo udzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi dziko lapansi.
Akutero Chauta amene adalenga zakumwamba, ndi Iyeyo Mulungu amene adaumba ndi kulenga dziko lapansi, ndipo adalikhazikitsa mwamphamvu. Sadalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma kuti likhale malo okhalamo anthu. Iyeyo akunena kuti: “Chauta ndine, palibenso wina ai.
Nanga Ine, kodi sindiyenera kuumvera chisoni mzinda waukulu wa Ninive? M'mene mujatu muli anthu opitirira zikwi 120, amene sadziŵa kusiyanitsa kuti zabwino nziti, zoipa nziti, mulinso ziŵeto zochuluka.”
Ndidakufikitsani ku dziko lachonde kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina. Koma mutangoloŵa m'dzikolo, mudaliipitsa, dziko limene ndidakupatsani mudalisandutsa lonyansa.
Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi.
“Popeza kuti nyama iliyonse yam'nkhalango ndi yanga, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku mapiri ochuluka. Mbalame zonse zamumlengalenga, zamoyo zonse zoyenda ku thengo ndi zanga.
“Muzibzala mbeu zaka zisanu ndi chimodzi m'munda mwanu, ndi kumakolola mbeuzo. Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe.
Maziko ozama a dziko lapansi ali m'manja mwake. Mapiri aatali omwe ngakenso. Nyanja ndi yake, popeza kuti ndiye adailenga. Mtunda ndi wakenso, popeza kuti ndiye adaupanga.
Dziko likulira ndipo likufota. Dziko lonse lapansi likuvutika ndipo likuuma. Mlengalenga ukuvutika pamodzi ndi dziko lapansi. Anthu aipitsa dziko lapansi posatsata malamulo a Mulungu, ponyoza mau ake, ndipo pophwanya chipangano chamuyaya chimene Iye adapangana nawo.
Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene amasamalira dziko limenelo ndi kumaliyang'anira chaka chonse mosalekeza.
M'mapiri aatali ndimo m'mene mumakhala mbalale, m'matanthwe ndimo m'mene mumathaŵira mbira. Inu mudapanga mwezi kuti uzisiyanitsa nyengo, ndipo dzuŵa limadziŵa nthaŵi yake yoloŵera. Mumadzifunditsa ndi kuŵala ngati chovala, mwatambasula mlengalenga ngati hema. Mumapanga mdima nukhala usiku, ndipo nyama zam'nkhalango zimatuluka. Misona ya mikango imabangula pofunafuna nyama, kupempha chakudya kwa Mulungu. Dzuŵa likamatuluka, imabwerera nkukagona m'mapanga mwake. Munthu amapita ku ntchito yake, amakagwira ntchito mpaka madzulo. Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
Uzidziŵe bwino nkhosa zako m'mene ziliri, ndipo usamalire ziŵeto zako. Paja chuma sichikhala mpaka muyaya. Kodi ufumu umakafika mpaka ku mibadwo yonse? Udzu ukatha, msipu nkuphuka, ndipo atatuta udzu wakumapiri, anaankhosa adzakupatsa chovala, ndi ubweya wao, ndipo pogulitsa mbuzi udzapeza chogulira munda. Udzakhala ndi mkaka wambiri wa mbuzi kuti uzidya, iweyo ndi banja lako, ndiponso ndi adzakazi ako omwe.
“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri musamagwira ntchito, kuti ng'ombe zanu zipume pamodzi ndi abulu anu omwe, kutinso akapolo anu ndi alendo omwe apezenso mphamvu.
Tamandani Chauta! Tamandani Chauta inu okhala kumwamba, mtamandeni inu okhala mu mlengalenga! Inu nyama zakutchire ndi zoŵeta zonse, inu zinthu zokwaŵa ndi mbalame zouluka! Inu mafumu a pa dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akuluakulu ndi olamulira dziko lapansi! Inu anyamata pamodzi ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe! Onsewo atamande dzina la Chauta, pakuti dzina lake lokha nlolemekezeka, ulemerero wake ndi woposa, pansi pano nkumwamba komwe. Chauta wakweza anthu ake poŵapatsa mphamvu. Walemekeza anthu ake onse oyera mtima, Aisraele amene Iye amaŵakonda. Tamandani Chauta! Mtamandeni inu angelo ake onse, mtamandeni inu magulu a ankhondo ake onse! Mtamandeni inu dzuŵa ndi mwezi, mtamandeni inu nonse nyenyezi zoŵala! Mtamandeni inu thambo lakumwambamwamba, ndi inu madzi a pamwamba pa thambo! Zonsezo zitamande dzina la Chauta! Paja Iye adaalamula, izo nkulengedwa.
Chauta akunena kuti, “Ndikulenga thambo lam'mwamba latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zakale sadzazikumbukiranso, zidzaiŵalika kotheratu. Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya, chifukwa cha zimene ndidzalenga. Ndidzalengadi Yerusalemu watsopano wodzaza ndi chimwemwe, ndipo anthu ake adzakhala okondwa.
Pambuyo pake ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Paja thambo loyamba lija ndi dziko lapansi loyamba lija zinali zitazimirira, ndipo nyanja panalibenso.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Mulungu amene adalenga dziko lapansi ndiponso zonse zili m'menemo, ndiye Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi. Iye sakhala m'nyumba zachipembedzo zomangidwa ndi anthu ai. Anthu sangamtumikire ndi manja ao, ngati kuti Iye amasoŵa kanthu. Pajatu Iye ndiye amapatsa anthu onse moyo, mpweya ndi zina zonse.
Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa. Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.