Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


64 Mau a Mulungu Olimbitsa Achinyamata

64 Mau a Mulungu Olimbitsa Achinyamata

Unyamata ndi nthawi yofunika kwambiri pa moyo wathu. Popanda mfundo zolimba, makhalidwe abwino, ndi kudziwa bwino Khristu, tingasochere m’dziko lodzala ndi mayesero. Ndikofunika kwambiri kumufunafuna Mulungu tili aang’ono, chifukwa nthawi zovuta ndi mayesero zikafika, ndi Iye yekha amene angatithandize kupambana.

Mulungu akufuna achinyamata omudziwa, omukhulupirira, ndi okhala moyo wom’kondweretsa. Achinyamata omwe amagwiritsitsa mawu ake ndi kutsatira malamulo ake. Tikatero, tidzakhala ndi moyo wodalitsidwa, ndipo ngakhale mavuto atafika, dzanja la Mulungu lidzatilimbitsa ndipo tidzakhalabe olimba m’chikhulupiriro chathu.

Kwa inu omwe mukuwerenga mawu awa, kumbukirani kuti Khristu akubwera posachedwa. Mufunafuneni tsopano popeza mungamupeze, musanachedwe. Ndi chikondi cha Yesu chomwe chingakuthandizeni kupirira mpaka kumapeto, chifukwa ali ndi mapulani abwino kwa inu, ndipo nthawi yomufunafuna ndi lero!

Kumbukiraninso kuti Mulungu ali nanu pakati pa mavuto ndi mayesero omwe mukukumana nawo. Khalani olimba mtima ndipo thawirani kwa Atate wanu wakumwamba, Iye adzakupatsani chipambano.




2 Timoteyo 2:22

Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:12

Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 12:1-2

Uzikumbukanso Mlengi wako pa masiku a unyamata wako, masiku oipa asanafike, zisanafikenso zaka zoti uzidzati, “Moyowu wandikola.” Mlalikiyo ankafunafuna mau ogwira mtima, ndipo adalemba mau oona ndi mtima wolungama. Mau a anthu anzeru ali ngati zisonga, ndipo zokamba zao zimene adasonkhanitsa zili ngati misomali yokhomerera kwambiri. Zolankhula zonsezo amapereka ndi Mbusa mmodzi yekha. Mwana wanga, uchenjere ndi kalikonse kobzola pamenepa. Kulemba mabuku sikutha, ndipo kuphunzira kwambiri kumatopetsa thupi. Basi, zonse zamveka. Mfundo yeniyeni ya zonsezi ndi iyi: Uzimvera Mulungu, ndipo uzitsata malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wake wonse wa munthu. Pajatu Mulungu adzaweruza zonse zimene timachita, zabwino kapena zoipa, ngakhale ndi zam'chinsinsi zomwe. Nthaŵi ya ukalamba wako, dzuŵa, kuŵala, mwezi, nyenyezi, zonse zidzakudera, ndipo mitambo idzabweranso mvula itagwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:9

Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:11

Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:13

Mudzandifunafuna, ndipo mudzandipeza. Mukadzandifunafuna ndi mtima wanu wonse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:21-22

koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino, ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:12

Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:23

Zinthu zonse nzololedwa, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwa, koma si zonse zimathandiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:16

Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:13

Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:10

Ngakhale bambo wanga ndi mai wanga andisiye ndekha, Inu Chauta mudzandisamala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-4

Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:9

Ndiye kuti pamene anthu osamala za Mulungu akuyesedwa, Iye amadziŵa kuŵapulumutsa kwake. Koma amadziŵanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:18

Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:26

Mwana wanga, mtima wako ukhulupirire ine, maso ako apenyetsetse njira zanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:17

Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga, ndipo ndikulalikabe ntchito zanu zodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:41

Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:10

Inu Mulungu, mwatiyesa, mwatiyeretsa monga m'mene amayeretsera siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:3

Paja mukudziŵa kuti mukamayesedwa m'chikhulupiriro chanu, mumasanduka olimbika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:1-4

Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera. Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga. Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu. Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.” Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:20

Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:16

“Uzilemekeza atate ako ndi amai ako, monga momwe Chauta, Mulungu wako, adakulamulira, kuti pakutero masiku a moyo wako achuluke ndipo kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 3:4

Kodi si tsopano apa wakhala ukundiwuza kuti, ‘Atate, ndinu bwenzi la unyamata wanga,’ numadzifunsa kuti,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:23-24

Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 23:10-11

Komabe Mulungu amadziŵa m'mene ndimayendera, akandiyesa adzapeza kuti ndine wangwiro ngati golide. Mapazi anga akuponda m'mapazi mwake, ndasunga njira yake, ndipo sindidaitaye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:1-3

Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku. Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 8:10

Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:12

Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 11:9

Anyamata inu, muzikondwerera unyamata wanu. Mitima yanu izisangalala pa nthaŵi ya unyamata wanu. Inde muzitsata zimene mtima wanu ukufuna, ndiponso zimene maso anu akupenya. Koma mudziŵe kuti pa zonsezo Mulungu adzakuweruzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:10

Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:13-14

Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu. Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:14

Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23-24

Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:7

Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru ndiye zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:7

Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14-16

“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:29

M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:1-2

Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga. Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina. Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha. Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta. Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.” Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira. Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.” Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:14

Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:4

Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6-7

Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:9

Chauta ndi wabwino kwa onse, amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:9

Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28-30

“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20

Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga wamuyaya, wamkulu, komanso wamphamvu ndinu! Ndikubwera kwa Inu kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu, ndikupempherera achinyamata onse omwe akukumana ndi mayesero. Mzimu Wanu Woyera uwalimbikitse ndi kuwatsogolera nthawi zonse. Ambuye, apatseni nzeru zosiyanitsa chabwino ndi choipa, kuti asanyengedwe, koma akhale okonzeka ndi odziteteza ku ziwembu zonse za mdani. Pakuti kwalembedwa, "Khalani oyera, chifukwa Ine ndine woyera." Ambuye, awathandize kuzindikira mayesero onse a mdani, awateteze ku anthu olankhula monyenga ndi okopa. Awathandize kusankha zoyenera ndi kupambana pa mayesero onse. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa