Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Obadiya INTRO1 - Buku Lopatulika

1

Mau Oyamba
Mneneriyu adalalikira mau ake pa nthawi ina yosadziwika bwinobwino Yerusalemu atangopasuka kumene m'chaka cha 586 BC. Nthawi imeneyo, Edomu anasangalala atamva kuti Yerusalemu wagwa. Edomu anali mdani wa Ayuda kuyambira kalekale wa dera lakum'mwera chakumadzulo. Sipokhapo ai, iye anatengerapo mwai pa chipsinjo cha Yuda pofunkha katundu wolandidwa ndi kumuthandizira mdaniyo. Obadiya analosera kuti Edomu adzalangidwa ndi kugonjetsedwa, pamodzi ndi maiko ena onse amene anali adani a Israele.
Za mkatimu
Chilango cha Edomu 1-14
Tsiku la Ambuye 15-21

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa