Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -

Miyambo INTRO1 - Buku Lopatulika

1

Mau Oyamba
Bukuli liphunzitsa nzeru zosiyanasiyana zothandiza anthu ndi kuwongolera moyo wao wa masiku onse mwa njira yokomera Mulungu ndi anzao. Mau ake ambiri akuwoneka ngati miyambi. Mau oyamba akuti, “Kudziwa nzeru ndi mwambo; kuzindikira mau ozindikiritsa; kulandira mwambo wakusamalira machitidwe, chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika.” Kenaka bukuli likupereka malangizo osiyanasiyana okhudza makhalidwe, kusunga mwambo, kupatsana ulemu ndi kukhalirana mwamtendere, kutsata choona ndi chilungamo, moyo wa pa banja, pa ntchito, pa malonda, pa maphwando ndi pa zochitika zina zilizonse. Nzeru ndizo zimene akuluakulu a Israele ankaphunzitsa anthu ao pa masiku akale. Wofuna kutsata nzeruzo ayenera kudzilamulira, kudzichepetsa, kuleza mtima, kulemekeza osauka ndi kukhala okhulupirika pa chibwenzi.
Za mkatimu
Bukuli lili ndi zigawo zingapo:
Mau oyamikira nzeru 1.1—9.18
Miyambi ya Solomoni 10.1—29.27
Mau a Aguri 30.1-33
Mau ena osiyanasiyana 31.1-31

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa