Maliro INTRO1 - Buku LopatulikaMau Oyamba Mau a m'bukuli ali ngati ndakatulo zolira chifukwa cha kupasuka kwa Yerusalemu ndi mavuto aakulu a ukapolo, zimene zidachitika m'chaka cha 586 BC. Mau ake ndi achisoni ndi odandaula, komabe mauwo aonetsanso mtima wokhulupirira Mulungu poyembekeza kuti adzakhalanso pabwino nthawi yake itakwana. Ayuda akhala akugwiritsabe ntchito ndakatulo zimenezi pa chipembedzo mpaka lero, pa masiku okumbukira kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu m'chaka cha 586 BC. Za mkatimu Zomumvetsa chisoni Yerusalemu 1.1-22 Chilango chogwera mzindawo 2.1-22 Yerusalemu azunzika, alapa ndipo ayembekeza chikhululukiro 3.1-66 Yerusalemu wasanduka bwinja 4.1-22 Pemphero lopempha chikhululukiro 5.1-22 |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi