Levitiko INTRO1 - Buku LopatulikaMau Oyamba Buku la Levitiko likukamba za malamulo a chipembedzo ndi miyambo yosiyanasiyana mu Israele wakale, komanso za malamulo okhudza ansembe amene anali ndi udindo woonetsetsa kuti malamulowo akutsatidwa bwino lomwe. Mutu waukulu mu bukuli ndiwakuti Yehova ndi Woyera ndipo anthu ake ayenera kukhala oyera mtima pa kupembedza kwao ndiponso moyo wao onse kuti ubale wao ndi Mulungu usasokonezeke. Mau amene amadziwika bwino kuchokera mu bukuli ndi omwe Yesu adawanena kuti ndilo lamulo lachiwiri lalikulu: “Udzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” (19.18) Za mkatimu Malamulo onena za zopereka ndi nsembe 1.1—7.38 Aroni ndi ana ake awadzoza kukhala ansembe 8.1—10.20 Malamulo onena za mwambo wa kuyeretsedwa ndi kudetsedwa 11.1—15.33 Za tsiku lotetezera 16.1-34 Malamulo onena za chiyero pa moyo ndi pa chipembedzo 17.1—27.34 |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi