Hagai INTRO1 - Buku LopatulikaMau Oyamba Mneneriyu adalalika mau ake chaka cha 520 BC., Ayuda ena atabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo. Anthuwo anali atabwerera ku ukapolo namakhala ku Yerusalemu kwa zaka zingapo, koma Kachisi anali bwinja lenileni. Atsogoleri anapereka uthenga kwa anthu kuti amangenso Kachisi, ndipo Ambuye akulonjeza kuti m'tsogolo anthu ake adzakhala pabwino ndi pa mtendere. Za mkatimu Yehova awalamula kuti amangenso Nyumba yake 1.1-15 Mau ena owalimbitsa mtima Ayudawo 2.1-23 |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi