Estere INTRO1 - Buku LopatulikaMau Oyamba Bukuli likukamba za Estere, mtsikana wina wachiyuda, amene ankakonda kwambiri anthu a mtundu wake, naonetsa kulimba mtima kwake pothandiza kuwapulumutsa Ayudawo kwa adani ao. Lifotokozanso za chiyambi chake komanso tanthauzo la chikondwerero cha Chiyuda chotchedwa Purimu. Za mkatimu Estere asankhidwa kuti akhale mfumukazi kudziko la Persiya 1.1—2.23 Hamani apanga chiwembu chofuna kuwonongeratu fuko la Ayuda 3.1—5.14 Hamani atsutsidwa naphedwa 6.1—7.10 Ayuda agonjetsa adani ao 8.1—10.3 |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi