1 Mbiri INTRO1 - Buku LopatulikaMau Oyamba Mabuku awiri otchedwa Mbiri akambanso zina ndi zina zimene zidakambidwa kale m'mabuku a Samuele ndi a Mafumu; koma kakambidwe kake nkosiyaniranapo polongosola mbiri ya ufumu wa Israele, chifukwa olemba mabuku a Mbiri ali ndi zolinga ziwiri: 1. Afuna kuwonetsa kuti, ngakhale Israele ndi a Yuda adawonongeka kotheratu, Mulungu salephera kuchita zimene analonjeza, mwakuti akuwongolerabe zinthu kudzera mwa anthu okhala mu Yuda, monga momwe adaziganiziratu pa chiyambi. Pofuna kulimbikitsa chiyembekezo chimenechi, olemba mabukuwa akukumbutsa zazikulu zimene adachita Davide ndi Solomoni, ndiponso ntchito za Yehosafati, Hezekiya ndi Yosiya, zothandiza anthu kukhala okhulupirika kwa Mulungu. 2. Afunanso kulongosola za chiyambi cha chipembedzo mu Kachisi wa Yehova ku Yerusalemu, ndiponso za udindo wa ansembe ndi Alevi pa mwambo wa chipembedzo. M'mabuku awiriwo Davide akuwoneka kuti iye ndi mkulu woyambitsa zonsezi, ngakhale amene anamanga Kachisi wa Yehova anali Solomoni. Buku loyamba la Mbiri lifotokoza makamaka za ufumu wa Davide. Za mkatimu Mndandanda wa anthu akale ndiponso wa makolo a Israele 1.1—9.44 Imfa ya Saulo 10.1-14 Ufumu wa Davide 11.1—29.30 a. Mavuto ake ndipo ntchito za zazikulu 11.1—22.1 b. Zokonzekera kumanga Kachisi wa Yehova 22.2—29.30 |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi