Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Obadiya 1:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa, iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe ndipo umamanga nyumba zako pa mapiri ataliatali, iwe amene umanena mu mtima mwako kuti, ‘Ndani anganditsitse pansi?’

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mwanyengedwa ndi mtima wanu wonyada. Likulu lanu lili pakati pa matanthwe, mumakhala pa mapiri aatali. Mumanena kuti, ‘Ndani angatitsitse pansi?’

Onani mutuwo



Obadiya 1:3
21 Mawu Ofanana  

Choncho Esau (amene ndi Edomu) anakakhazikika ku dziko la mapiri ku Seiri.


Iye ndiye amene anapha Aedomu 10,000 mʼchigwa cha Mchere nalanda mzinda wa Sela pa nkhondo ndipo anawutcha Yokiteeli, dzina lake ndi lomwelo mpaka lero lino.


Ndipo Amaziya analimba mtima ndipo anatsogolera gulu lake lankhondo ku Chigwa cha Mchere, kumene anapha anthu 10,000 a ku Seiri.


Gulu la ankhondo la Yuda linagwiranso anthu amoyo 10,000, napita nawo pamwamba pa thanthwe ndipo anawaponya pansi kotero kuti onse ananyenyeka.


Ngakhale atamayenda mapewa ake ali mmwamba ndipo mutu wake uli nengʼaa,


Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wodzikuza adzagwa.


Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umakhala wonyada, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.


Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa, koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.


Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri. Kunyada kwawo ndi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo, zonse ndi zopanda phindu.


Ndidzalimbana nanu, inu amene mukukhala pamwamba pa chigwa, inu okhala ngati thanthwe lapachidikha, akutero Yehova. Inu amene mumanena kuti, ‘Ndani amene angabwere kudzalimbana nafe? Ndani amene angathe kulowa mʼmalinga mwathu?’


“Yehova akuti: Musadzinyenge, nʼkumaganiza kuti, ‘Ndithu Ababuloni adzatisiya.’ Ndithudi sadzakusiyani!


Inu amene mumakhala ku Mowabu, siyani mizinda yanu ndi kukakhala pakati pa matanthwe. Khalani ngati nkhunda imene imamanga chisa chake pa khomo la phanga.


Kuopseza kwako kwakunyenga; kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa, iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe ndi mʼmapiri. Ngakhale utamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga, ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,” akutero Yehova.


Chifukwa chiyani mukunyadira chigwa chanu, inu anthu osakhulupirika amene munadalira chuma chanu nʼkumati: ‘Ndani angandithire nkhondo?’


Unatanganidwa ndi zamalonda. Zotsatira zake zinali zoti unachulukitsa zandewu ndi kumachimwa. Choncho ndinakuchotsa ku phiri langa lopatulika. Mkerubi amene ankakulondera uja anakupirikitsa kukuchotsa ku miyala yamoto.


Mwina Edomu nʼkunena kuti, “Ngakhale taphwanyidwa, tidzamanganso mʼmabwinja.” Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Iwo angathe kumanganso, koma Ine ndidzazigwetsanso. Iwo adzatchedwa dziko loyipa, la anthu amene Yehova wayipidwa nawo mpaka muyaya.