Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 8:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aaroni anachitadi zomwezo. Anayimika nyale ndi kuziyangʼanitsa kumene kunali choyikapo nyale monga Yehova analamulira Mose.

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikaponyali, monga Yehova adauza Mose.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikapo nyali, monga Yehova adauza Mose.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aroni adaikadi nyalezo. Adaziika kuti ziwunikire patsogolo pa choikaponyale, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.

Onani mutuwo



Numeri 8:3
5 Mawu Ofanana  

choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri pamodzi ndi nyale zake ndi zipangizo zake zonse, ndiponso mafuta anyalezo;


Ndipo anayikapo nyale zija pamaso pa Yehova, monga Yehova analamulira Mose.


“Yankhula ndi Aaroni kuti pamene uyimika nyale zisanu ndi ziwiri, nyalezo ziziyaka kutsogolo kwa choyikapo nyale.”


Choyikapo nyalecho chinapangidwa motere: chinasulidwa kuchokera ku golide, kuyambira pa tsinde pake mpaka ku maluwa ake. Choyikapo nyalecho chinapangidwa monga momwe Yehova anaonetsera Mose.


Anthu sayatsa nyale ndikuyivundikira ndi mbiya, mʼmalo mwake amayika poonekera ndipo imawunikira onse mʼnyumbamo.