“Uwawuzenso kuti, ‘Tengani ngolo zingapo za kuno ku Igupto kuti mukakwezepo ana anu, akazi anu pamodzi ndi abambo ako ndi kubwera nawo kuno.
Numeri 7:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anabweretsa zopereka zawo pamaso pa Yehova: ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ngʼombe zothena khumi ndi ziwiri. Mtsogoleri mmodzi ngʼombe yothena imodzi ndipo atsogoleri awiri ngolo imodzi. Izi anazipereka ku chihema. Buku Lopatulika anadza nacho chopereka chao pamaso pa Yehova, magaleta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi kalonga awiru anapereka galeta ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa chihema. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 anadza nacho chopereka chao pamaso pa Yehova, magaleta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa Kachisi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa adatenga zopereka zao, ndipo adabwera nazo pamaso pa Chauta. Adapereka ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ng'ombe khumi ndi ziŵiri: atsogoleri aŵiri ngolo imodzi, ndipo mtsogoleri aliyense ng'ombe imodzi. Zimenezo adafika nazo ku chihema cha Chauta. |
“Uwawuzenso kuti, ‘Tengani ngolo zingapo za kuno ku Igupto kuti mukakwezepo ana anu, akazi anu pamodzi ndi abambo ako ndi kubwera nawo kuno.
Choncho ana a Israeli anachita zimenezo. Yosefe anawapatsa ngolo monga Farao analamulira, ndipo anawapatsanso chakudya cha paulendo wawo.
Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale.
“Uza Aisraeli kuti abweretse chopereka kwa Ine. Iwe ulandire choperekacho mʼmalo mwanga kuchokera kwa munthu amene akupereka mwakufuna kwake.
Ndipo adzabwera nawo abale anu onse ngati mphatso yopereka kwa Yehova kuchokera kwa anthu a mitundu yonse. Iwo adzakwera nawo kupita ku Yerusalemu, phiri langa loyera ku Yerusalemu monga nsembe kwa Yehova, atakwera akavalo, magaleta ndi ngolo, ndi pa abulu ndi ngamira,” akutero Yehova. “Adzabwera nawo ngati momwe Aisraeli amabwerera ndi zopereka zachakudya ku Nyumba ya Yehova mu ziwiya zoyeretsedwa monga mwa mwambo.