Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 7:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka atsogoleri a Aisraeli, akuluakulu a mabanja omwe ankayangʼanira mafuko a anthu omwe anawawerenga aja, anachita chopereka.

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

akalonga a Israele, akulu a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mafuko akuyang'anira owerengedwa;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

akalonga a Israele, akulu a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mafuko akuyang'anira owerengedwa;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsiku lomwelo akulu a Aisraele, ndiye kuti atsogoleri a mabanja ndi a mafuko amene ankayang'anira kuŵerenga kuja,

Onani mutuwo



Numeri 7:2
11 Mawu Ofanana  

Pamenepo Mfumu Solomoni inasonkhanitsa akuluakulu a Israeli, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli mu Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi la Chipangano la Yehova ku Ziyoni, Mzinda wa Davide.


Akuluakulu akenso anapereka mwaufulu kwa anthu ndi kwa ansembe ndi Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehieli oyangʼanira ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu anapereka kwa ansembe zopereka za Paska 2,600 ndi ngʼombe 300.


Atsogoleri anabweretsa miyala ya onikisi ndi miyala yokongola yoyika pa efodi ndi chovala chapachifuwa.


Mose anawuza Aisraeli onse zonse zimene Yehova anamulamula. Iye anati, “Zimene Yehova walamula ndi izi:


Ndipo Mose ndi wansembe Eliezara analandira kuchokera kwa atsogoleriwo golide pamodzi ndi zipangizo zonse zosula.