Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
Numeri 3:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amenewa ndi mayina a ana aamuna a Aaroni, ansembe odzozedwa omwe anapatulidwa kuti azitumikira ngati ansembe. Buku Lopatulika Awa ndi maina a ana aamuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao achite ntchito ya nsembe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Awa ndi maina a ana amuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao achite ntchito ya nsembe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ameneŵa ndiwo maina a ana a Aroni, ansembe odzozedwa amene iye adaŵasankha kuti azitumikira pa ntchito yaunsembe. |
Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
Zovala zimenezi umuveke Aaroni, mʼbale wako ndi ana ake. Kenaka uwadzoze, uwapatse udindo ndi kuwapatula kuti anditumikire ngati ansembe anga.
Kenaka umuveke Aaroni zovala zopatulika, umudzoze ndi kumupatula kotero kuti athe kunditumikira monga wansembe.
Uwadzoze monga momwe unadzozera abambo awo, kotero kuti anditumikire monga ansembe. Kudzozedwako kudzakhala unsembe wawo pa mibado ndi mibado”
Kenaka Mose anatenga mafuta wodzozera ansembe ndi magazi amene anali pa guwa nawaza pa Aaroni ndi zovala zake ndiponso ana ake aja ndi zovala zawo. Motero Mose anapatula Aaroni ndi zovala zake, ndiponso ana ake ndi zovala zawo.
Koma Nadabu ndi Abihu, anagwa nafa pamaso pa Yehova pamene ankapereka nsembe ndi moto wachilendo pamaso pa Yehova mʼchipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana aamuna. Choncho Eliezara ndi Itamara ndiwo amene ankatumikira ngati ansembe nthawi imene Aaroni abambo awo anali moyo.
Pakuti lamulo limasankha anthu amene ndi ofowoka kukhala akulu a ansembe; koma lumbiro, lomwe linabwera pambuyo pa lamulo, linasankha Mwana, amene anapangidwa kukhala wangwiro kwamuyaya.