Numeri 2:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, |
Tsono tenti ya msonkhano ndi msasa wa Alevi zidzakhala pakati pa misasayo. Iwo adzasamuka monga momwe anamangira misasa yawo, aliyense pa malo ake pamene pali mbendera yake.
“Aisraeli azimanga misasa yawo mozungulira tenti ya msonkhano motalikira pangʼono. Munthu aliyense amange pamene pali mbendera ya fuko lake.”
Kenaka atsogoleri a Aisraeli, akuluakulu a mabanja omwe ankayangʼanira mafuko a anthu omwe anawawerenga aja, anachita chopereka.