Ngʼombe ndi mbuzi zoperekera nsembe yopepesera machimo zimene magazi ake anabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera Malo Wopatulika, azitulutsire kunja kwa msasa. Koma zikopa zake, nyama yake ndi matumbo ake azitenthe.
Numeri 19:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muyipereke kwa Eliezara, wansembe ndipo apite nayo kunja kwa msasa. Iphedwe iye ali pomwepo. Buku Lopatulika ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naitulutse iye kunja kwa chigono, ndipo wina aiphe pamaso pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naitulutse iye kunja kwa chigono, ndipo wina aiphe pamaso pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muupereke kwa wansembe Eleazara, kenaka anthu atuluke nawo kunja kwa mahema, ndipo auphe pamaso pake. |
Ngʼombe ndi mbuzi zoperekera nsembe yopepesera machimo zimene magazi ake anabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera Malo Wopatulika, azitulutsire kunja kwa msasa. Koma zikopa zake, nyama yake ndi matumbo ake azitenthe.
“Pita naye kunja kwa msasa munthu wotembererayo. Onse amene anamumva akutemberera asanjike manja awo pamutu pake ndipo gulu lonse la anthu limugende miyala.
Koma chikopa cha ngʼombe yayimunayo ndi mnofu wake wonse, pamodzi ndi mutu ndi miyendo, zamʼkati ndi matumbo,
kapena kuti ngʼombe yonse yotsalayo apite nayo kunja kwa msasa ku malo woyeretsedwa, kumene amatayako phulusa ndi kuyitentha pa nkhuni, pa phulusapo.
Kenaka atulutse ngʼombeyo kunja kwa msasa ndi kuyitentha monga anatenthera ngʼombe yoyamba ija. Imeneyi ndiyo nsembe yopepesera machimo a gulu lonse.
Choncho gululo linamutengera kunja kwa msasa ndi kumupha pomugenda ndi miyala, monga momwe Yehova analamulira Mose.
“Munthu amene ndi woyeretsedwa achotse phulusa la ngʼombeyo ndi kuliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa msasa. Aisraeli adzasunge phulusalo kuti azikaligwiritsa ntchito polithira mʼmadzi woyeretsera ndi wochotsera tchimo.
Koma Nadabu ndi Abihu, anagwa nafa pamaso pa Yehova pamene ankapereka nsembe ndi moto wachilendo pamaso pa Yehova mʼchipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana aamuna. Choncho Eliezara ndi Itamara ndiwo amene ankatumikira ngati ansembe nthawi imene Aaroni abambo awo anali moyo.
“Lamula Aisraeli kuti achotse mu msasa aliyense amene ali ndi matenda opatsirana a pa khungu kapena matenda otuluka madzi mʼthupi a mtundu uliwonse, kapena aliyense wodetsedwa chifukwa cha munthu wakufa.