“Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti, ‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’ Ndipo fuwulani kuti, ‘Sonkhanani! Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’
Numeri 10:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene akuliza malipenga onse awiri, anthu onse asonkhane kwa iwe pa khomo la tenti ya msonkhano. Buku Lopatulika Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la chihema chokomanako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la chihema chokomanako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akaliza aŵiri onsewo, mpingo wonse usonkhane kwa iwe pa chipata cha chihema chamsonkhano. |
“Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti, ‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’ Ndipo fuwulani kuti, ‘Sonkhanani! Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’
Lizani lipenga mu Ziyoni. Chenjezani pa phiri langa loyera. Onse okhala mʼdziko anjenjemere, pakuti tsiku la Yehova likubwera, layandikira;