Mbiri ya momwe kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera pa tsiku lija Yehova Mulungu ankazilenga ndi iyi: Yehova Mulungu atapanga dziko lapansi ndi kumwamba,
Genesis 1:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi. Buku Lopatulika Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mulungu adati, “Kuyere,” ndipo kudayeradi. |
Mbiri ya momwe kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera pa tsiku lija Yehova Mulungu ankazilenga ndi iyi: Yehova Mulungu atapanga dziko lapansi ndi kumwamba,
Taonani momwe amawalitsira zingʼaningʼani pa malo ake onse, zimafika ngakhale pansi pa nyanja.
Yehova ndi Mulungu, ndipo kuwala kwake kwatiwunikira Ife. Lowani nawo pa mʼdipiti wa ku chikondwerero mutanyamula nthambi mʼdzanja lanu, mpaka ku nyanga za guwa.
Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa, zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.
Ndimalenga kuwala ndi mdima, ndimabweretsa madalitso ndi tsoka; ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.
Sipadzakhala dzuwa kuti likuwunikire, kapena mwezi kuti uwunikire usiku, pakuti Yehova ndiye adzakhale kuwunika kwako kwa muyaya, ndipo Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.
Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!” Nthawi yomweyo anachiritsidwa khate lake.
Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa.
Pakuti Mulungu amene anati, “Kuwala kuwunike kuchokera mu mdima,” Iyeyo ndiye anawunikira mʼmitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuoneka pa nkhope ya Yesu Khristu.
Nʼchifukwa chake Malemba akuti, “Dzuka, wamtulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuwalira.”
Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika
Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni.
Uthenga umene tinamva kwa Iye ndipo tikuwulalikira kwa inu ndi uwu: Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye mulibe mdima konse.
Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Choonadi chake chikuoneka mwa Yesu ndiponso mwa inu, chifukwa mdima ukutha ndipo kuwunika kwenikweni kwayamba kale kuwala.