Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Filemoni 1:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

komabe ndikupempha mwachikondi. Ine Paulo, munthu wokalamba, ndipo tsopano ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu,

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Komabe chifukwa cha chikondi makamaka ndingochita kukupempha, ine Paulo amene ndili nkhalamba, amenenso ndili m'ndende tsopano chifukwa cha Khristu Yesu.

Onani mutuwo



Filemoni 1:9
17 Mawu Ofanana  

Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu musanditaye Inu Mulungu, mpaka nditalengeza mphamvu zanu kwa mibado yonse yakutsogolo.


Musanditaye pamene ndakalamba; musandisiye pamene mphamvu zanga zatha.


Imvi zili ngati chipewa chaufumu chaulemerero; munthu amazipeza akakhala moyo wolungama.


Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi ndidzakusamalirani ndithu. Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani, ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.


Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.


Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu.


Pogwira naye ntchito pamodzi, tikukudandaulirani kuti musangolandira chisomo cha Mulungu pachabe.


Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu,


Nʼchifukwa chake ine Paulo, ndili wamʼndende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu anthu a mitundu ina.


Ine monga wamʼndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukulimbikitsani kuti mukhale moyo woyenera mayitanidwe amene munalandira.


Ndine kazembe wa Uthenga Wabwinowu ngakhale ndili womangidwa mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire mopanda mantha, monga ndiyenera.


Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene anandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Iye ananditenga kukhala wokhulupirira, nandipatsa ntchito mu utumiki wake.


Phunzitsa amuna achikulire kuti akhale osaledzera, aulemu wawo, odziletsa, okhwima mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkupirira.


Ine ndikukupemphani kuti mundipempherere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga.


Okondedwa, ndikukupemphani, ngati alendo pansi pano, pewani zilakolako za uchimo, zimene zimachita nkhondo ndi moyo wanu.


Ngati abambo awo kapena alongo awo adzabwera kudzadandaula kwa ife, tidzawawuza kuti, ‘Chonde, tikomereni mtima powalola kuti atenga ana anu aakaziwo popeza kuti ife sitinawapezere akazi pomenya nkhondo. Inunso simunachite kuwapatsa. Mukanatero ndiye mukanapalamula.’ ”