Filemoni 1:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kwa Apiya mlongo wathu, Arkipo msilikali mnzathu, ndiponso mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwanu. Buku Lopatulika ndi kwa Afiya mlongoyo, ndi Arkipo msilikali mnzathu, ndi kwa Mpingo uli m'nyumba yako: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi kwa Afiya mlongoyo, ndi Arkipo msilikali mnzathu, ndi kwa Mpingo uli m'nyumba yako: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kalata yomweyinso tikulembera Afiya, mlongo wathu, ndi Arkipo, msilikali mnzathu pa nkhondo ya Mulungu, ndiponso mpingo wonse umene umasonkhana kunyumba kwanu. |
Perekaninso moni kwa mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwawo. Perekani moni kwa mʼbale wanga wokondedwa Epeneto, amene ndi woyamba kukhulupirira Khristu mʼchigawo cha Asiya.
Mpingo wa mʼchigawo cha ku Asiya ukupereka moni. Akula ndi Prisila akuperekanso moni wachisangalalo, mwa Ambuye, ndiponso mpingo umene umakumana mʼnyumba mwawo ukupereka moni.
Koma ndikuganiza kuti nʼkofunika kuti ndikutumizireni mʼbale wanga Epafrodito, mtumiki mnzanga ndi msilikali mnzanga, amenenso ndi mtumiki wanu amene munamutumiza kuti adzandithandize pa zosowa zanga.
Perekani moni kwa abale a ku Laodikaya, ndiponso kwa Numfa ndi mpingo wa mʼnyumba mwake.