Ndithu Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake, zipewa za ubweya za iwo amene amapitiriza kuchita machimo awo.
Eksodo 9:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati ukana kuti apite ndi kupitiriza kuwaletsa, Buku Lopatulika Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira chigwiritsire, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira chigwiritsire, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ukakananso kuŵalola kuti apite, ndi kuŵaletsa ndithu, |
Ndithu Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake, zipewa za ubweya za iwo amene amapitiriza kuchita machimo awo.
Choncho ndikuti, ‘Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’ ”
Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ”
Ndipo ngati simulola kuti apite Ine ndidzalanga dziko lonse la Igupto polidzaza ndi achule.
Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mawa mmawa upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso ndipo ukamuwuze kuti Yehova Mulungu wa Ahebri akuti ulole anthu anga apite kuti akandipembedze.
dzanja la Yehova lidzakantha ziweto zako zimene zili ku munda, pamodzi ndi akavalo, abulu, ngamira, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi ndi mliri woopsa kwambiri.
Koma Mulungu adzakhuthulira mkwiyo ndi ukali wake pa amene amachita zofuna zawo ndi kukana choonadi nʼkumatsatira zoyipa.
Anapserera nako kutentha kwakukuluko ndipo anatukwana Mulungu, amene anali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi, koma anakana kulapa ndi kumulemekeza.