Eksodo 8:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ngati simulola kuti apite Ine ndidzalanga dziko lonse la Igupto polidzaza ndi achule. Buku Lopatulika Ndipo ukakana kuwalola amuke, taona, Ine ndidzapanda dziko lako lonse ndi achule; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ukakana kuwalola amuke, taona, Ine ndidzapanda dziko lako lonse ndi achule; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ukakana kuŵalola, dziko lako lonse ndidzalilanga polidzaza ndi achule. |
Iye anawatumizira magulu a ntchentche zimene zinawawononga, ndiponso achule amene anawasakaza.
Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Farao ndi wowuma mtima. Akukana kulola anthu anga kuti apite.
Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Ukamuwuze Farao kuti, Lolani anthu anga kuti apite, akandipembedze.
Mtsinje wa Nailo udzadzaza ndi achule. Achulewo adzatuluka ndi kukalowa mʼnyumba yaufumu, ku chipinda chogona ndi pa bedi lako, mʼnyumba za nduna zako ndi pa anthu ako ndi mophikira buledi ndiponso mopangira bulediyo.