Iwe ukuti uli ndi luso ndiponso mphamvu pa nkhondo, komatu ukuyankhula mawu opanda pake. Kodi tsono iwe ukudalira yani kuti undiwukire ine?
Eksodo 5:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muwakhawulitse ndi ntchito anthu amenewa kuti azitanganidwa, asakhale ndi mpata omvera zabodza.” Buku Lopatulika Ilimbike ntchito pa amunawo, kuti aigwiritsitse, asasamalire mau amabodza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ilimbike ntchito pa amunawo, kuti aigwiritsitse, asasamalire mau amabodza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muŵagwiritse ntchito yakalavulagaga anthu ameneŵa, kuti azitanganidwa ndi ntchito m'malo momangomvera zabodza.” |
Iwe ukuti uli ndi luso ndiponso mphamvu pa nkhondo, komatu ukuyankhula mawu opanda pake. Kodi tsono iwe ukudalira yani kuti undiwukire ine?
Kodi mawu anu ochulukawo adzatha? Kodi chikukuvutani nʼchiyani kuti muzingoyankhula mawu otsutsawa?
Choncho akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu anapita kwa anthu aja nati, “ ‘Farao akuti sadzakupatsaninso udzu.
Koma musawachepetsere chiwerengero cha njerwa chomwe munawalamulira kale kuti aziwumba. Iwowa ndi aulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, ‘Tiloleni tipite tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’
Azariya mwana wa Hosayia ndi Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi anthu onse odzikuza anawuza Yeremiya kuti, “Ukunama iwe! Yehova Mulungu wathu sanakutume kuti unene kuti, ‘Musapite ku Igupto kukakhala kumeneko.’
Kodi mawu anga ndi malangizo anga, amene ndinawawuza atumiki anga aneneri, suja anawachitira makolo anu? “Tsono iwo analapa ndi kunena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse watichitira zomwe zikuyenera njira zathu ndi machitidwe athu, monga anatsimikiza kuti adzachita.’ ”
“Mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nʼkosapindulitsa. Kodi timapindulanji pochita zofuna zake, ndi kumayenda ngati anamfedwa pamaso pa Yehova Wamphamvuzonse?
Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera.