Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake, chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
Eksodo 39:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anasula golide wopyapyala ndi kumulezaleza kuti alumikize kumodzi ndi nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yosalala yofewa yolukidwa mwaluso. Buku Lopatulika Ndipo anasula golide waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya m'misiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anasula golide waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adasula golide mwaphanthiphanthi, namlenzalenza, kuti amlukire kumodzi ndi thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, ndiponso la bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ntchito yaumisiri. |
Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake, chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
“Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi.
Anthu onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo anapanga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso anapeta pa nsaluzo Akerubi.
Popanga efodi, iwo anagwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yosalala yofewa.
Iwo anapanga efodi imene inali ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa, tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga.