Ngamira zija zitatha kumwa, mlendo uja anatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli ndi zibangiri zagolide ziwiri zolemera masekeli 100.
Eksodo 32:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero anthu onse anavula ndolo zagolide ndi kubwera nazo kwa Aaroni. Buku Lopatulika Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthuwo adavuladi nsapule zao, ndipo adabwera nazo kwa Aroni. |
Ngamira zija zitatha kumwa, mlendo uja anatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli ndi zibangiri zagolide ziwiri zolemera masekeli 100.
Choncho anamupatsa Yakobo milungu yachilendo yonse imene anali nayo pamodzi ndi ndolo. Iye anazikwirira pansi pa mtengo wa thundu ku Sekemu.
Aaroni anawayankha kuti, “Vulani ndolo zagolide zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi aakazi ndipo muzibweretse kwa ine.”
Choncho Aaroni analandira golideyo ndipo anamuwumba ndi chikombole ndi kupanga fano la mwana wangʼombe. Kenaka anthu aja anati, “Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.”
Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo ndipo amayeza siliva pa masikelo; amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu, kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.
Siliva wosula amabwera naye kuchokera ku Tarisisi ndipo golide amachokera naye ku Ufazi. Mafanowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi odziwa kuzokota golide. Tsono mafanowo amawaveka zovala za mtundu wamtambo ndi pepo. Yonseyo ndi ntchito ya anthu a luso.