Eksodo 3:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Mose anati mu mtima mwake, “Ine ndipita komweko ndikaone zodabwitsazi, chitsamba sichikunyeka chifukwa chiyani?” Buku Lopatulika Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone chooneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone chooneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mumtima mwake adati, “Ndipita pafupi, kuti ndikaonetsetse zozizwitsa ndikupenyazi. Chifukwa chiyani chitsambacho sichilikupsa?” |
Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi chifukwa cha machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,
Kumeneko mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye mʼmalawi amoto mʼchitsamba. Mose anaona kuti ngakhale chitsambacho chimayaka koma sichimanyeka.
Iye ataona zimenezi, anadabwa. Akupita kuti akaonetsetse pafupi, Mose anamva mawu a Ambuye: