Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi. Uchite chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo.
Eksodo 26:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Panga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo. Buku Lopatulika Ndipo uziika magango a nsalu ya madzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi, ku mkawo wa chilumikizano; nuchite momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uziika magango a nsalu ya madzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi, ku mkawo wa chilumikizano; nuchite momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Upange timagonga ta nsalu yobiriŵira m'mbali mwake mwa nsalu imodzi kumapeto kwake. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu inzakeyo. |
Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi. Uchite chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo.
Upange zokolowekamo 50 pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Upange motero kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana.
Kenaka anasokerera zokolowekamo makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija ndiponso anapanga zokolowekamo zina makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija.